Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Imfa
    Kukambitsirana za m’Malemba
    • mukuchitiramo. Kodi munali kudziŵa kuti unyinji wa Agiriki akale anali ndi lingaliro lofananalo? Iwo anakhulupirira kuti panali milungu yachikazi itatu imene imapima utali wa moyo umene munthu aliyense akakhala nawo. Koma Baibulo limafotokoza lingaliro losiyana kwambiri.’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (1) (Ŵerengani Mlaliki 9:11.) Mwachitsanzo: Chidutswa cha konkire chingasweke kunyumba ndi kugwera pamunthu woyenda ndi miyendo. Kodi anachichititsa ndi Mulungu? Ngati ziri choncho, kodi nkolungama kuimba mlandu mwininyumbayo wa kunyalanyaza? . . . Monga momwe Baibulo limanenera, kwa woyenda ndi miyendoyo, chinali chochitika chosalinganizidwa ndi chosawonedweratu chakuti iye anali pamenepo pamene konkire inagwa.’ (2) ‘Baibulo limatiuza kuti ngati tipeŵa khalidwe loipa timatetezera moyo wathu. (Miy. 16:17) Ngati inu muli kholo, ndiri wotsimikiza kuti mumagwiritsira ntchito lamulo lamakhalidwe abwino limenelo kwa ana anu. Mumawachenjeza kusachita zinthu zimene zingachititse kutayika kwa moyo. Yehova akuchita chinthu chofanana kaamba ka anthu onse lerolino.’ (3) ‘Yehova amadziŵa chimene chiri mtsogolo. Kupyolera mwa Baibulo amatiuza mmene tingakhalire moyo kwanthaŵi yaitali kwambiri koposa anthu amene amanyalanyaza zimene limanena. (Yoh. 17:3; Miy. 12:28)’ (Wonaninso mutu waukulu wakuti “Choikidwiratu.”)

  • Kubadwanso
    Kukambitsirana za m’Malemba
    • Kubadwanso

      Tanthauzo: Kubadwanso kumaphatikizapo kubatizidwa m’madzi (“kubadwa mwa madzi”) ndi kubadwa ndi mzimu wa Mulungu (“kubadwa ndi . . . mzimu”), chotero kukhala mwana wa Mulungu ndi chiyembekezo cha kukhala ndi phande mu Ufumu wa Mulungu. (Yoh. 3:3-5) Yesu anali ndi chokumana nacho ichi, monga momwe a 144 000 aliri amene ali oloŵa nyumba limodzi naye mu Ufumu wakumwamba.

      Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kwa Akristu alionse “kubadwanso”?

      Mulungu analinganiza kugwirizanitsa chiŵerengero chochepa cha anthu okhulupirika limodzi ndi Yesu Kristu mu Ufumu wa wakumwamba

      Luka 12:32: “Musawopa, kagulu kankhosa inu; chifukwa Atate wanu akonda kukupatsani ufumu.”

      Chiv. 14:1-3: “Ndinapenya, tawonani, Mwanawankhosayo [Yesu Kristu] ali kuimirira paphiri la Ziyoni, ndipo pamodzi ndi iye zikwi zana mphambu makumi anayi kudza anayi . . . ogulidwa kuchokera kudziko.” (Wonanitsamba 208, 209, pamutu wakuti “Kumwamba.”)

      Anthu sangapite kumwamba ndi matupi anyama ndi mwazi

      1 Akor. 15:50: “Ndinena ichi, abale, kuti thupi ndi mwazi sizingathe kuloŵa ufumu wa Mulungu; kapena chivundi sichimaloŵa chisavundi.”

      Yoh. 3:6: “Chobadwa m’thupi chikhala thupi, ndipo chobadwa mwa mzimu, chikhala mzimu.”

      Anthu okha amene “abadwanso,” mwanjira iyi kukhala ana aamuna a Mulungu, angagaŵane mu Ufumu wakumwamba

      Yoh. 1:12, 13: “Koma onse amene anamulandira iye [Kristu Yesu], kwa iwo anapatsa mphamvu ya kukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lake; amene sanabadwa ndi mwazi, kapena ndi chifuniro chathupi, kapena ndi chifuniro chamunthu, koma cha Mulungu.” (“Onse amene anamulandira iye” samatanthauza kuti anthu onse amene akhulupirira mwa Kristu. Tawonani amene akutchulidwa, monga kwasonyezedwa ndi vesi 11 [“ake amwini yekha,” Ayuda]. Mwaŵi umodzimodziwo waperekedwa kwa ena amtundu wa anthu, koma kokha ku “kagulu kankhosa.”)

      Aroma 8:16, 17, NW: “Mzimu uwo wokha umachitira umboni ndi mzimu wathu kuti ife tiri ana a Mulungu. Pamenepa, ngati, tiri ana, tirinso oloŵa nyumba ogwirizana limodzi ndi Kristu, malinga ngati tivutika limodzi kuti tikalemekezedwenso limodzi.”

      1 Pet. 1:3, 4: “Wodalitsidwa Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, iye amene, monga mwa chifundo chake chachikulu, anatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, pa kuuka kwa akufa kwa Yesu Kristu; kuti tilandire choloŵa chosavunda ndi chosadetsa ndi chosafota, chosungikira m’Mwamba inu.”

      Kodi iwo adzachitanji kumwamba?

      Chiv. 20:6: “Adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Kristu, nadzachita ufumu pamodzi ndi iye zaka chikwizo.”

      1 Akor. 6:2: “Kodi sumudziŵa kuti oyera mtima adzaweruza dziko?”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena