-
KubadwansoKukambitsirana za m’Malemba
-
-
[Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti Yohane sadzakhala m’miyamba ndipo chotero panalibe chifukwa chakuti iye “abadwenso”]. Ndipo kuyambira masiku a Yohane mbatizi kufikira tsopano lino [pamene Yesu analankhula mawuwa] ufumu wakumwamba uli wokakamizidwa.”—Mat. 11:11, 12.
Mzimu wa Yehova “unagwira ntchito” pa Davide ndipo “unalankhula” mwa iye (1 Sam. 16:13; 2 Sam. 23:2), koma palibe paliponse pamene Baibulo limanena kuti iye “anabadwanso.” Panalibe kufunikira kwa iye “kubadwanso,” chifukwa chakuti, monga momwe Machitidwe 2:34 amanenera kuti: “Davide sanakwere kumwamba.”
Kodi nchiyani chimene lerolino chimadziŵikitsa anthu okhala ndi mzimu wa Mulungu?
Wonani tsamba 320, 321, pamutu waukulu wakuti “Mzimu.”
Ngati Wina Anena Kuti—
‘Ndinabadwanso’
Mungayankhe kuti: ‘Ndiko kuti tsiku lina mukuyembekezera kukakhala ndi Kristu kumwamba, kodi sichoncho? . . . Kodi munayamba mwadabwa chimene opita kumwamba adzachita kumeneko?’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (1) ‘Adzakhala mafumu ndi ansembe, kulamulira pamodzi ndi Kristu. (Chiv. 20:6; 5:9, 10) Yesu ananena kuti amenewa akakhala kokha “kagulu kankhosa.” (Luka 12:32)’ (2) ‘Ngati pali mafumu, payeneranso kukhala nzika zimene iwo adzalamulira. Kodi zimenezi zidzakhala ayani? . . . Nazi mfundo zina zimene ndinapeza kukhala zokondweretsa kwambiri pamene zinasonyezedwa kwa ine. (Sal. 37:11, 29; Miy. 2:21, 22)’
‘Kodi munabadwanso?’
Mungayankhe kuti: ‘Ndimawona kuti chimene anthu amatanthauza mwa kumati “kubadwanso” sichiri nthaŵi zonse chofanana. Kodi mungandiuze chimene kumatanthauza kwa inu?’
Kapena munganene kuti: ‘Mufuna kudziŵa kuti kaya ndinavomereza Yesu Kristu monga Mpulumutsi wanga ndi kulandira mzimu woyera, kodi sichoncho? Ndiloleni ndikutsimikizireni kuti yankho ndilo Inde; ngati sizinali zotero sindikanakhala ndikulankhula ndi inu za Yesu.’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (1) ‘Koma pamene ndikuganiza za kukhala ndi mzimu woyera, ndimapeza kuti umboni wamzimu umenewu ukusoŵeka momvetsa chisoni mwa ambiri odzitcha kukhala Akristu. (Agal 5:22, 23)’ (2) ‘Kodi mukanasangalala kukhala ndi moyo padziko lapansi iri ngati aliyense anasonyeza mikhalidwe yaumulungu imeneyo? (Sal. 37:10, 11)’
Kuthekera kwina: ‘Ngati mwa mawuwo mutanthauza kuti, “Kodi ndinavomereza Kristu monga Mpulumutsi wanga?” yankholo ndilo Inde. Onse a Mboni za Yehova atero. Koma, kwa ife, kubadwanso kumaphatikizapo zowonjezereka kuposa zimenezo.’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (1) ‘Pamene Yesu analankhula za kubadwanso ananena kuti kunali kofunika kuloŵa Ufumu wa Mulungu, boma lake lakumwamba. (Yoh. 3:5)’ (2) ‘Baibulo limasonyezanso kuti anthu ambiri amene amachita chifuniro cha Mulungu adzakhala ndi moyo pano padziko lapansi, monga nzika zachimwemwe za Ufumu umenewo. (Mat. 6:10; Sal. 37:29)’
Malingaliro owonjezereka: Awo amene ali a kagulu kakumwamba angayankhe kuti: ‘Inde, ndiri. Koma Baibulo limachenjeza tonsefe kusakhala ndi chidaliro chopambanitsa cha ife eni. Tifunikira kudzipenda kuti titsimikizire kuti tikuchitadi zimene Mulungu ndi Kristu akuyembekezera kwa ife. (1 Akor. 10:12)’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: ‘Kodi ndithayo lotani limene Yesu anaika pa ophunzira ake owona? (Mat. 28:19, 20; 1 Akor. 9:16)’
-
-
Kubweranso kwa KristuKukambitsirana za m’Malemba
-
-
Kubweranso kwa Kristu
Tanthauzo: Asanachoke padziko lapansi, Yesu Kristu analonjeza kubweranso. Zochitika zochititsa nthumanzi zogwirizanitsidwa ndi Ufumu wa Mulungu nzogwirizanitsidwa ndi lonjezo limenelo. Kuyenera kudziŵika kuti pali kusiyana pakati pa kudza ndi kukhalapo. Chotero, pamene kuli kwakuti kudza kwa munthu (kogwirizanitsidwa ndi kufika kapena kubwerera kwake) kumawonekera panthaŵi yotchulidwa, kukhalapo kwake kungakhaleko kwanyengo yokwanira zaka zambiri pambuyo pake. M’Baibulo liwu Lachigiriki erʹkho·mai (kutanthauza “kudza”) likugwiritsiridwanso ntchito kunena kupereka chisamaliro kwa Yesu kuntchito yofunika panthaŵi yeniyeni mkati mwa kukhalapo kwake, ndiko kuti, kuntchito yake monga wolipsira wa Yehova pankhondo yatsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.
-