-
KuululaKukambitsirana za m’Malemba
-
-
chitseko chako, nupemphere Atate wako ali mtseri . . . Atate wathu wakumwamba dzina lanu liyeretsedwe . . . mutikhululukire mangaŵa anthu, monga ifenso takhululukira amangaŵa athu.”
Sal. 32:5: “Ndinavomereza choipa changa kwa inu [Mulungu], ndipo mphulupulu yanga sindinaibisa. Ndinati, ndidzaululira Yehova machimo anga; ndipo munakhululukira choipa cha kulakwa kwanga.”
1 Yoh. 2:1: “Akachimwa wina, nkhoswe tiri naye kwa Atate, ndiye Yesu Kristu wolungama.”
Pamene munthu aliyense payekha achimwira munthu mnzake kapena pamene achimwiridwa
Mat. 5:23, 24: “Ngati uli kupereka mtulo wako paguwa lansembe, ndipo pomwepo ukakumbukira kuti mbale wako ali ndi kanthu pa iwe, usiye pomwepo mtulo wako kuguwako, nuchoke, nuyambe kuyanjana ndi mbale wako, ndipo pamenepo idza nupereke mtulo wako.”
Mat. 18:15: “Ngati mbale wako akuchimwira iwe, pita, numlangize panokha iwe ndi iye.”
Luka 17:3: “Akachimwa mbale wako umdzudzule; akalapa umkhululukire.”
Aef. 4:32: “Mukhalirane okoma mtima wina ndi mnzake, amtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Kristu anakhululukira inu.”
Pamene munthu aphatikizidwa m’cholakwa chachikulu ndipo afuna chithandizo chauzimu
Yak. 5:14-16: “Kodi pali wina adwala [mwauzimu] mwa inu? Adziitanire akulu ampingo, ndipo apemphere pa iye, atamdzoza ndi mafuta m’dzina la Ambuye; ndipo pemphero la chikhulupiriro lidzapulumutsa wodwalayo, ndipo Ambuye adzamuukitsa; ndipo ngati adachita machimo adzakhululukidwa kwa iye [ndi Mulungu]. Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupemphere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe.”
Miy. 28:13: “Wobisa machimo ake sadzawona mwaŵi; koma wakuwavomereza, nawasiya adzachitiridwa chifundo.”
Bwanji ngati anthu ochita machimo safunafuna chithandizo?
Agal. 6:1: “Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu mubweze woteroyo mu mzimu wachifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso.”
1 Tim. 5:20: “Iwo akuchimwa uwadzudzule pamaso pa onse [ndiko kuti, awo amene amadziŵa za nkhaniyo], kuti otsalawo achite mantha.”
1 Akor. 5:11-13: “Musayanjane naye, ngati wina wotchedwa mbale ali wachigololo, kapena wosirira, kapena wopembedza mafano, kapena wolalatira, kapena woledzera, kapena wolanda, ngakhale kukadya naye wotere, iyayi. . . . Chotsani woipayo pakati pa inu nokha.”
-
-
KuvutikaKukambitsirana za m’Malemba
-
-
Kuvutika
Tanthauzo: Chokumana nacho chimene munthu amakhala nacho pamene akupirira zopweteka kapena nsautso. Kuvutikako kungakhale kwakuthupi, kwamaganizo, kapena kwamalingaliro. Zinthu zambiri zingachititse kuvutika; mwachitsanzo, chivulazo chochitidwa ndi nkhondo ndi umbombo wa zamalonda, mikhalidwe yoipa yobadwa nayo, matenda, ngozi, “masoka achilengedwe,” zinthu zankhalwe zonenedwa kapena kuchitidwa ndi ena, zipsinjo za ziŵanda, kuzindikira kuyandikira kwa tsoka, kapena kupusa kwa munthu mwiniyo. Kuvutika kumeneku kumachititsidwa ndi zovutitsa zosiyanasiyana zimenezi kudzalingaliridwa panopa. Komabe, munthu angavutike chifukwa cha kuzindikira kwake mikhalidwe ya anthu ena kapena nkhaŵa yake yaikulu pakuwona mkhalidwe wopanda umulungu.
Kodi nchifukwa ninji Mulungu amalola kuvutika?
Kodi ndani amene kwenikweni amakuchititsa?
Anthu ndiwo amachititsa ambiri a mavutowo. Amamenya nkhondo, amachita upandu, amaipitsa malo, kaŵirikaŵiri amachita mabizinesi mu mkhalidwe wosonkhezeredwa ndi umbombo mmalo mwa kudera nkhaŵa ndi anthu anzawo, ndipo nthaŵi zina amadziloŵetsa m’zizoloŵezi zimene iwo amadziŵa kuti zingakhale zovulaza thanzi lawo. Pamene achita zinthu zimenezi, amavulaza anzawo ndi iwo eni. Kodi kuyenera kuyembekezeredwa kuti anthu akakhala osayambukiridwa ndi zotulukapo za zimene iwo amachita? (Agal. 6:7; Miy. 1:30-33) Kodi kuli kwanzeru kuimba Mulungu mlandu wa zinthu izi zimene anthu iwo eni amachita?
-