Nyimbo 13
Kudzipatulira Kwachikristu
1. Chifukwa Ya analenga
Chilengedwe chonse,
Dziko ndi miyamba nzake,
Ziri ntchito zake.
Wapatsa mpweya wa moyo
Nasonyeza kuti
Ngwoyenera kutamandidwa,
Kulambiranso nkwake.
2. Pa Sinai Israyeli
Wakale anati:
Tidzasunga Lamulo la
Yehova mokondwa.
Anali mwamuna wawo;
Powagula m’nyanja.
Mtundu wa odziperekawo
Mwenzi ukadatero.
3. Yesu anabatizidwa
Ka’mba ka Ubwino,
Nadzipereka kuchita
Chifuno cha M’lungu.
Atatuluka m’Yordano
Monga wodzozedwa,
Kuti atumikire monga
Wopatulika wa Ya.
4. Tidza kwa inu Yehova,
Kudzakutamani.
Modzichepetsa mtimatu
Tikudzipereka.
Munatipatsa Mwanayo,
Napereka mtengo.
Sitidzadzikhalira moyo,
Koma ka’mba ka inu.