Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Imfa
    Kukambitsirana za m’Malemba
    • ali ndi moyo wosakhoza kufa umene umapulumuka pa imfa yathupi ndipo, chotero, akuzindikira zimene amoyowo akuchita. Koma Baibulo limati: “Akufa . . . sadziŵa kanthu bi.” (Mlal. 9:5) Ndiponso, limati “Moyo wochimawo ndiwo udzafa.”—Ezek. 18:4.

      Miyambo yambiri imabuka kuchokera m’kukhulupirira kuti akufa afunikira chithandizo cha amoyo kapena mantha akuti iwo angavulaze amoyo ngati sakukondweretsedwa. Koma Mawu a Mulungu amasonyeza kuti akufa sakuvutika kapena kukondwera konse. “Mpweya wake uchoka, abwerera kumka kunthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.” (Sal. 146:4; wonaninso 2 Samueli 12:22, 23.) “Chikondano chawo ndi mdano wawo ndi dumbo lawo lomwe zatha tsopano; ndipo nthaŵi yamuyaya sagaŵa konse kanthu kalikonse kachitidwa pansi pano.”—Mlal. 9:6.

      Ngati Wina Anena Kuti—

      ‘Chiri chifuniro cha Mulungu’

      Mungayankhe kuti: ‘Chimenecho chiri chikhulupiriro chofala kwambiri. Ndakupeza kukhala kothandiza kusanthula chimene Mulungu iye mwiniyo amanena za ichi.’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (1) ‘(Ŵerengani Genesis 2:17.) Ngati atate achenjeza mwana wake wamwamuna kuti kuchita chinthu chakutichakuti kukamuwonongetsera moyo, kodi mukananena kuti atateyo akufuna kuti mwanayo achichite?’ (2) ‘Pamenepa kodi nchiyani chimene kwenikweni chiri chifuno cha Mulungu kwa anthu? Yesu anati: “Chifuniro cha Atate wanga ndi ichi, kuti yense wa kuyang’ana Mwana [ndiko kuti, kuzindikira ndi kuvomereza kuti Yesu alidi Mwana wa Mulungu] ndi kukhulupirira iye, akhale nawo moyo wosatha; ndipo ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza.” (Yoh. 6:40)’

      ‘Anthu adzafa nthaŵi zonse’

      Mungayankhe kuti: ‘Ndithudi zimenezo ndizo zimene zachitika kwa anthu kufikira tsiku lathu, kodi sichoncho?’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: ‘Koma wonani lonjezo lodabwitsa loperekedwa ndi Mulungu pa Chivumbulutso 21:3, 4 (kapena Yesaya 25:8).’

      ‘Zimachitika ngati nthaŵi yako yakwana’

      Mungayankhe kuti: ‘Anthu ochuluka amalingalira mmene mukuchitiramo. Kodi munali kudziŵa kuti unyinji wa Agiriki akale anali ndi lingaliro lofananalo? Iwo anakhulupirira kuti panali milungu yachikazi itatu imene imapima utali wa moyo umene munthu aliyense akakhala nawo. Koma Baibulo limafotokoza lingaliro losiyana kwambiri.’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (1) (Ŵerengani Mlaliki 9:11.) Mwachitsanzo: Chidutswa cha konkire chingasweke kunyumba ndi kugwera pamunthu woyenda ndi miyendo. Kodi anachichititsa ndi Mulungu? Ngati ziri choncho, kodi nkolungama kuimba mlandu mwininyumbayo wa kunyalanyaza? . . . Monga momwe Baibulo limanenera, kwa woyenda ndi miyendoyo, chinali chochitika chosalinganizidwa ndi chosawonedweratu chakuti iye anali pamenepo pamene konkire inagwa.’ (2) ‘Baibulo limatiuza kuti ngati tipeŵa khalidwe loipa timatetezera moyo wathu. (Miy. 16:17) Ngati inu muli kholo, ndiri wotsimikiza kuti mumagwiritsira ntchito lamulo lamakhalidwe abwino limenelo kwa ana anu. Mumawachenjeza kusachita zinthu zimene zingachititse kutayika kwa moyo. Yehova akuchita chinthu chofanana kaamba ka anthu onse lerolino.’ (3) ‘Yehova amadziŵa chimene chiri mtsogolo. Kupyolera mwa Baibulo amatiuza mmene tingakhalire moyo kwanthaŵi yaitali kwambiri koposa anthu amene amanyalanyaza zimene limanena. (Yoh. 17:3; Miy. 12:28)’ (Wonaninso mutu waukulu wakuti “Choikidwiratu.”)

  • Kubadwanso
    Kukambitsirana za m’Malemba
    • Kubadwanso

      Tanthauzo: Kubadwanso kumaphatikizapo kubatizidwa m’madzi (“kubadwa mwa madzi”) ndi kubadwa ndi mzimu wa Mulungu (“kubadwa ndi . . . mzimu”), chotero kukhala mwana wa Mulungu ndi chiyembekezo cha kukhala ndi phande mu Ufumu wa Mulungu. (Yoh. 3:3-5) Yesu anali ndi chokumana nacho ichi, monga momwe a 144 000 aliri amene ali oloŵa nyumba limodzi naye mu Ufumu wakumwamba.

      Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kwa Akristu alionse “kubadwanso”?

      Mulungu analinganiza kugwirizanitsa chiŵerengero chochepa cha anthu okhulupirika limodzi ndi Yesu Kristu mu Ufumu wa wakumwamba

      Luka 12:32: “Musawopa, kagulu kankhosa inu; chifukwa Atate wanu akonda kukupatsani ufumu.”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena