Phunziro 11
Kukhala ndi Kalankhulidwe Kabwino Tsiku ndi Tsiku
1. Kodi n’chiyani chingapangitse kalankhulidwe kathu kukhala kokondweretsa Yehova?
1 “Mawu a m’kamwa mwanga . . . avomerezeke pamaso panu, Yehova.” (Sal. 19:14) Kuti zikhale choncho kwa ife, m’pofunika kuti tizilankhula zinthu zoyenera komanso m’njira yoyenera mtumiki wa Mulungu. Timafuna kuti kalankhulidwe kathu kasonyeze kuti tili atumiki a Mulungu okhulupirika tsiku lina lililonse, osati kokha pamene tili pa Nyumba ya Ufumu kapena mu utumiki wakumunda. Tikatero, tidzaona kuti kalankhulidwe kathu panyumba, kuntchito, ndi kusukulu komwe, kadzapereka chithunzi chabwino cha utumiki wathu.—2 Akor. 6:3.
2, 3. N’chifukwa chiyani kalankhulidwe kathu ndi kusankha mawu zili zofunika kwambiri?
2 Kalankhulidwe kathu n’kofunika kwambiri. Zimenezi zimaphatikizapo ngakhale maonekedwe a nkhope yathu ndi mamvekedwe a mawu. Nkhope zathu ziyenera kusonyeza chimwemwe chathu pokhala atumiki a Yehova. Kukhala kwathu aubwenzi ndi kumwetulira kumakopa anthu. Ngakhale kuti choonadi cha Baibulo chimene timalankhula si nkhani yongocheza, icho chilinso chosangalatsa. Choncho khalani osangalala! Nkhope yamphwayi siyenerana ndi uthenga wathu wopatsa chiyembekezo.
3 Pamene mudzizoloŵeza kulankhula kwabwino mudzaona kuti mawu ndi maonekedwe a nkhope amakhala ndi “umunthu” wake. Angakhale owopseza kapena okopa, okoma mtima kapena aukali, aubwenzi kapena ankhanza, olimbikitsa kapena okhwethemula. Chotero, kusankha mawu abwino ndi kuwalankhula moyenera n’kofunika kwambiri. Zimenezi zili choncho makamaka polankhula za mawu a choonadi, amene ali uthenga wabwino wa Ufumu.
4. Kodi tingawonjezere motani nkhokwe yathu ya mawu?
4 Kuwonjezera nkhokwe yanu ya mawu. Palibe kusoŵeka kwa mawu otamanda nawo Yehova, monga mmene tingaonere tikangoyang’ana m’dikishonale ina iliyonse. Koma funso n’lakuti, Kodi nkhokwe ya mawu onsewo omwe alipo mumaigwiritsa ntchito kwenikweni? Kodi poŵerenga, mawu amene simukuwamvetsa bwino mumawayang’ana m’dikishonale, kapena kuwachonga kuti muwayang’ane m’dikishonale kapena kufunsa kwa ena mutamaliza nkhaniyo? Kuchita chimenechi kudzakuthandizani kudziŵa mawu ochuluka. Mudzaonanso kuti alipo mawu ambiri amene mukuwadziŵa koma simuwagwiritsa ntchito m’kulankhula kwanu kwa tsiku ndi tsiku. Yesetsani kuwalankhula pamene kukhala koyenera. Kunena zoona, zinthu zidzakuyenderani bwino monga mtumiki wachikristu kapena wophunzira ngati mupitiriza kukulitsa luso lanu la kulankhula bwino.
5, 6. Kodi n’chiyani chingatithandize kulankhula bwino mawu?
5 Phunzirani kulankhula mawu oyenera. Zimatheka kuti mawu aŵiri n’kutanthauza chinthu chimodzi koma angosiyana pang’ono powagwiritsa ntchito m’nkhani zosiyana. Ngati musamala zimenezi mudzapeŵa kukhumudwitsa anthu okumvetserani, ndipo mudzawongolera mamvekedwe anu polankhula. Kumakhala kothandiza kuyang’ana m’dikishonale yabwino kapena kufunsira kwa odziŵa bwino chinenero. Madikishonale ena amandandalikanso mawu ofanana matanthauzo ndi liwu limene alisonyezalo, komanso matanthauzo ena a liwulo. Ndipo mabuku ena amasonyeza mawu otsutsana matanthauzo. Chotero mumapeza mawu ena osiyanasiyana otanthauza chinthu chimodzi, komanso matanthauzo ena a liwulo. Zimenezi n’zothandiza kwambiri pamene mukufuna liwu loyenerera bwino pankhani yakutiyakuti. Kugwiritsa ntchito mawu oyenera kumakuthandizaninso kusalankhula mawu ambiri osafunikira, ndipo kumakutheketsani kulunjika pamfundo zofunikira. Kuchulukitsa mawu kumakwirira ganizo lofunikira. Choncho yesetsani kumalankhula ndi mawu ochepa. Pamene mukhoza, yambani kumaphatikiza m’kulankhula kwanu mawu olongosola zinthu kuti muwonjezerepo ukoma ndi tanthauzo.
6 Pamene mukuwonjezera nkhokwe yanu ya mawu, musamangoganiza za mawu atsopano okha, koma ganizaninso za mawu osonyeza mikhalidwe yakutiyakuti: maverebu [aneni] amene amasonyeza mphamvu; maajekitivu [afotokozi] amene amakometsera; mawu opitirizira kulankhula amene amathandiza kusinthasintha mamvekedwe a liwu; mawu osonyeza ubwenzi ndi a mamvekedwe achifundo. Poŵerenga mabuku a Sosaite mutha kuona mitundumitundu ya mawu amene mungasankhepo.
7, 8. Pofuna kuwonjezera nkhokwe yathu ya mawu, kodi tiyenera kusamala za chiyani?
7 Komabe, cholinga chodziŵira mawu ochuluka, sindicho kudzionetsera. Cholinga chathu ndicho kuti tipereke chidziŵitso, osati kuti omvetsera atitame ayi. Tiyenera kukhala ndi maganizo ofanana ndi a mtumwi Paulo amene anati: “Mu mpingo ndifuna kulankhula mawu asanu ndi chidziŵitso changa, kutinso ndikalangize ena, koposa kulankhula mawu zikwi m’lilime [lachilendo].” (1 Akor. 14:9, 19) Ngati kalankhulidwe ka munthu n’kovuta kwambiri kukamva kamangofanana ndi lilime lachilendo. Mofananamo, n’kwanzeru kupeŵa kulankhula mawu ovuta kwa anthu amene sangathe kuzindikira tanthauzo la mawu ocholoŵanawo. Ngakhale pokambirana wamba tisayese kudzionetsera kwa omvetserawo polankhula mawu ovuta ndi aatali. Chofunika n’choti omvetsera athu amvetse zimene tikunena. Kumbukirani, Miyambo 15:2 imati, “lilime la anzeru linena bwino zomwe adziŵa.” Kusankha mawu abwino komanso osavuta kumva, kumapangitsa kulankhula kwathu kukhala kotsitsimutsa ndi kosangalatsa, osati kozizira ndi kogwetsa mphwayi.—Akol. 4:6.
8 N’kofunikanso kudziŵa matchulidwe oyenera a mawu. Mukhoza kumvetsera mmene ena amatchulira mawu ena. Mukamatero mudzapeŵa kumangotchula mawu mosasamala. China chofunika kupeŵa m’kalankhulidwe ka tsiku ndi tsiku ndicho kulankhula kokhala ngati kumulumunya mawu, kutereretsa mawu pa lilime kapena kudulira mawu. Musalankhule choluma mano. Yesani kutchula mawu bwinobwino. Tsegulani pakamwa panu kuti mutchule mawu momvekera bwino.
9-12. Kodi ndi kalankhulidwe ndi mawu otani amene tiyenera kupeŵa, ndipo chifukwa chake n’chiyani?
9 Kalankhulidwe Kofunika Kupeŵa. Mawu a Mulungu amatithandiza kuona mawu oyenera kuwapeŵa pa moyo wathu wa tsiku ndi tsiku. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo, akutilangiza kuti tipeŵe “zimene siziyenera,” monga “zopusa.” (Aef. 5:3, 4) Tiyenera kupeŵa mawu onyoza ndi otukwana. Paulo analembanso kuti: “Nkhani yonse yovunda isatuluke m’kamwa mwanu, koma ngati pali ina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse chisomo kwa iwo akumva.” (Aef. 4:29) Choncho Akristu ayenera kupeŵa mawu otukwana ndi kulankhula mwandewu. Anthu ena amaganiza kuti kalankhulidwe koteroko ndiko kamamveketsa mwamphamvu zomwe akunenazo. Koma mawu abwino amphamvu alipo ambiri. N’kosafunika kuti ifenso titengere kalankhulidwe koipa koteroko ngakhale pamene tikulankhula nawo anthu amenewo. Kalankhulidwe kodekha kangakhale kothandiza, koma kakhale kokoma ndi koona.
10 Chofunikanso kupeŵa ndicho mawu ena ndi kalankhulidwe kamene kamaswa malamulo a chinenero, kaya kuti galamala. Kalankhulidwe koteroko kaŵirikaŵiri amakakonda ndi asangalatsi akudziko ndipo kamafala kwambiri m’nyimbo zamakono. Anthu amakonda kutengera asangalatsi amenewo. Koma si bwino kuti Akristunso atengere kalankhulidwe kameneko. Kuteroko kukatigwirizanitsa ndi dziko ndi moyo wake. Ogulitsa mankhwala osokoneza bongo ndi ena amene upandu ndi chiwerewere ndiwo moyo wawo ali ndi kalankhulidwe kawokawo, kotchula mawu m’njira yosadziŵika bwino kwa munthu wina. Koma kalankhulidwe kathu kasayambukiridwe ndi malankhulidwe adziko oterowo.—Aroma 12:2.
11 Akristu ayenera kusamala kuti apeŵe kunena mawu amwano. Anthu ena amatchula mawu akuti “Mulungu” ndi “Ambuye,” komanso “Jizasi” ndi “Jizasi Krasti” kungoti agogomeze zimene akunenazo, kapena monga m’loŵa m’malo wa liwu lotukwana kapena kunyoza. Mawu ena monga akuti “goshi,” “mayi godi,” “godi heveni” amatengedwa ku liwu lakuti “Mulungu,” n’chifukwa chake alinso osayenera.—Eks. 20:7; Mat. 5:34-37.
12 Nthaŵi zina zimene anthu amanena ndi kuchita zikhoza kutikwiyitsa. Ngakhale ndi choncho, kukakhala kosayenera kwa Mkristu kuyankha ndi mawu aukali kapena onyoza. Mtumwi Paulo akuti: “Tsopano tayani inunso zonsezi: mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, zonyansa zotuluka m’kamwa mwanu.” (Akol. 3:8) Choncho ngakhale pamene ena akukwiyitsani ndi kalankhulidwe kawo, njira yanzeru ikakhala kudziletsa.—Miy. 14:29; Yak. 3:11.
13-16. Kodi n’chiyani chingatithandize kuwongolera mawu athu ndi zizoloŵezi zina polankhula?
13 Kulankhula bwino chinenero. Anthu ena angaone kuti satha kulankhula bwino chinenero. Mwina anakulira kudziko lina kapena analibe mwayi wophunzira sukulu mokwanira adakali aang’ono. Amenewo asachite mphwayi ayi; m’malo mwake, ayesetse mwakhama kuti aphunzire, akumatero ndi cholinga cholalikira uthenga wabwino. Pali masitepe opindulitsa amene angawatsate. Mwachitsanzo, kuŵerenga kwa banja kumapereka mwayi wophunzira zimenezo. Zochuluka zimene timadziŵa za galamala ya chinenero timaziphunzira mwa kumva ena akulankhula. Chotero mvetserani mosamalitsa pamene abale achikulire, ophunzira bwino akulankhula. Pamene muŵerenga Baibulo ndi mabuku a Sosaite, onani kalembedwe ka masentensi kapena kuti ziganizo ndi mtundu wa mawu ogwiritsidwa ntchito m’mikhalidwe yosiyanasiyana. Yesani kulankhula motengera zitsanzo zabwino zimenezo.
14 Achinyamata ayenera kutengera mwayi wa kuphunzira galamala yabwino ndi kalankhulidwe koyenera adakali pasukulu. Mutaona kuti simutha kumvetsa lamulo linalake la galamala, kafunsireni kwa mphunzitsi wanu. M’pofunika kuti mulimbikire, chifukwa mukufuna kukhala mlaliki wogwira mtima wa uthenga wabwino.
15 Yesetsani kukhala ndi kalankhulidwe kabwino tsiku ndi tsiku. Munthu wokhala ndi chizoloŵezi cholankhula mosasamala m’makambirano ake a tsiku ndi tsiku sangathe kulankhula bwino pazochitika zapadera. Kulankhula bwino kumalira kuyesetsa. Koma ngati mukhala ndi kalankhulidwe kabwino m’zochitika za masiku onse, kudzakhala kosavuta ndipo kwachibadwa kulankhula papulatifomu kapena pochitira umboni kwa ena za choonadi cha Mulungu.
16 Kuyesetsa kulankhula bwino tsiku ndi tsiku kumathandiza kudzaza m’maganizo ndi mitima yathu mawu okoma amene tingathokoze nawo Yehova pa zifuniro zake zaulemerero zodzakwaniritsidwa mwa ufumu wake. Pamenepo tidzaona choonadi cha mawu a Yesu pa Luka 6:45: “Munthu wabwino atulutsa zabwino m’chuma chokoma cha mtima wake.”