Dziko Lapansi
Tanthauzo: Liwu lakuti “dziko lapansi” limagwiritsiridwa ntchito kuposa mu lingaliro limodzi m’Malemba. Kaŵirikaŵiri timaganiza za ilo kukhala likusonya kuplaneti lenilenilo, limene Yehova mokoma mtima anakongoletsa kotero kuti lichirikize moyo wa anthu ncholinga cha kupangitsa miyoyo yathu kukhala yokhutira molemerera. Komabe, kuyenera kudziŵika, kuti “dziko lapansi” lingagwiritsiridwenso ntchito mu lingaliro lophiphiritsira, mwachitsanzo, kunena, za anthu okhala paplaneti lino kapena ku chimangidwe cha anthu chimene chiri ndi zizoloŵezi zakutizakuti.
Kodi planetili dziko lapansi lidzawonongedwa m’nkhondo yanyukliya?
Kodi Baibulo limasonyeza kuti nchiyani chimene chiri chifuno cha Mulungu ponena za dziko lapansi?
Mat. 6:10: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.”
Sal. 37:29: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”
Wonaninso Mlaliki 1:4; Salmo 104:5
Kodi pali kuthekera kwakuti, popeza kuti mitundu ikusonyeza nkhaŵa yochepa kaamba ka chifuno cha Mulungu, kuti angawononge kotheratu dziko lapansi mwa njira ina yake kwakusankhoza kukhalika?
Yes. 55:8-11: “[Ati Yehova:] Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, momwemo njira zanga ziri zazitali kupambana njira zanu, ndi maganizo anga kupambana maganizo anu. . . . Mawu anga . . . sadzabwerera kwa ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula mmene ndinawatumizira.”
Yes. 40:15, 26: “Tawonani, [kwa Yehova Mulungu] amitundu akunga dontho la mu mtsuko, naŵerengedwa ngati fumbi losalala la m’miyeso. . . . Kwezani maso anu kumwamba, muwone [dzuŵa, mwezi ndi mabiliyoni anyenyezi] amene analenga izo, amene atulutsa khamu lawo ndi kuziŵerenga; azitcha zonse maina awo, ndi mphamvu zake zazikulu, ndi popeza ali wolimba mphamvu, palibe imodzi isoŵeka.” (Mphamvu yanyukliya yopangidwa ndi amitundu njochititsa mantha kwa anthu. Koma mabiliyoni ambiri anyenyezi amapambana mphamvu yanyukliya pamlingo wooti maganizo athu ngwosakhoza kuzindikira. Kodi ndani amene analenga ndi amene amalamulira makamu onse akumwamba awa? Kodi Iye sangalepheretse amitundu kugwiritsira ntchito zida zankhondo zanyukliya mwanjira imene ikanalepheretsa chifuno chake? Kuti Mulungu angachite zimenezo kwafotokozedwa mwafanizo mwa kuwononga kwake magulu ankhondo amphamvu a Igupto pamene Farao anafunafuna kuletsa chilanditso cha Israyeli.—Eks. 14:5-31.)
Chiv. 11:17, 18, NW: “Tikuyamikani, Yehova Mulungu, Wamphamvuyonse, amene muli ndi amene munali, chifukwa mwatenga mphamvu yanu yaikulu ndi kuyamba kulamulira monga mfumu. Koma mitundu inakwiya, ndipo mkwiyo wanu unafika, ndi nthaŵi yoikidwiratu . . . kuwononga awo owononga dziko lapansi.”
Kodi Mulungu mwiniyo adzawononga dziko lapansi ndi moto?
Kodi 2 Petro 3:7, 10 akuchirikiza lingaliro iri? “Miyamba ndi dziko la masiku ano, ndi mawu omwewo zaikika kumoto, zosungika kufikira tsiku lachiweruzo ndi chiwonongeko [“kuwonongeka,” RS] cha anthu osapembedza. . . . Tsiku la Ambuye lidzadza ngati mbala; mmene miyamba idzapita ndi chibumo chachikulu, ndi zam’mwamba zidzakanganuka ndi kutentha kwakukulu, ndipo dziko ndi ntchito ziri momwemo zidzatenthedwa [“wotchedwa (kunyeketsedwa),” RS, JB; “zidzazimiririka,” TEV; “zidzasonyezedwa,” NAB; “zidzavumbulutsidwa,” NE; “zidzatulukiridwa,” NW].” (Tamverani: Ma Codex Sinaiticus ndi Vatican MS 1209, onse a m’zaka za zana la 4 C.E., amati “kutulukiridwa.” Malembo apamanja apambuyo pake, otchedwa Codex Alexandrinus a m’zaka za zana la 5 ndi a m’zaka za zana la 16 opendedwa ndi Clementine a Vulgate amati “zidzawotchedwa.”)
Kodi Chivumbulutso 21:1 amasonyeza kuti planeti lathuli lidzawonongedwa? “Ndipo ndinawona m’mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano; pakuti m’mwamba moyamba ndi dziko loyamba zidachoka, ndipo kulibenso nyanja.”
Kuti akhale olondola, malongosoledwe a mavesi amenewa ayenera kuvomerezana ndi mawu apatsogolo ndi pambuyo ndiponso ndi mbali yotsala ya Baibulo
Ngati malemba awa (2 Petro 3:7, 10 ndi Chivumbulutso 21:1) amatanthauza kuti planeti lenileni Dziko Lapansi lidzawotchedwa ndi moto, pamenepo miyamba yeniyeni (nyenyezi ndi makamu ena akumwamba) nayonso idzawonongedwa ndi moto. Komabe, lingaliro losakhala lophiphiritsira limenelo, limawombana ndi zitsimikiziro zimene ziri m’malemba monga Mateyu 6:10, Salmo 37:29 ndi 104:5, ndiponso Miyambo 2:21, 22. Ndiponso, kodi nchiyambukiro chanji chimene moto ukanakhala nacho padzuŵa ndi nyenyezi zimene ziri ng’anjo kale? Chotero liwu lakuti “dziko lapansi” m’lemba logwidwa mawu pamwambapa liyenera kuzindikiridwa mwa lingaliro losiyana.
Pa Genesis 11:1, Mafumu Woyamba 2:1, 2, Mbiri Woyamba 16:31, Salmo 96:1, ndi ena, liwu lakuti “dziko lapansi” lagwiritsiridwa ntchito m’lingaliro lophiphiritsira, likumasonyeza anthu, chitaganya cha anthu. Kodi zimenezo sizingakhale zimene 2 Petro 3:7, 10 ndi Chivumbulutso 21:1 amatanthauza?
Tawonani kuti, m’mawu apatsogolo ndi pambuyo, pa 2 Petro 3:5, 6 (ndiponso 2:5, 9), akusonyezedwa kufanana ndi Chigumula cha Tsiku la Nowa, m’chimene chitaganya cha anthu oipa chinawongedwa, koma Nowa ndi banja lake, kudzanso mbulumbwa yeniyeniyo, anatetezeredwa. Mofananamo, pa 2 Petro 3:7 pamanena kuti odzawonongedwa ndiwo “anthu osapembedza.” Lingaliro lakuti “dziko lapansi” panopa likusonya ku chitaganya cha anthu oipa likuvomerezana kotheratu ndi mbali yotsala ya Baibulo, monga momwe kwafotokozedwera mwafanizo m’malemba otchulidwa pamwambapa. Ndiro “dziko lapansi” lophiphiritsira limenelo, kapena chitaganya cha anthu oipa chimene “chitulukiridwa”; ndiko kuti, Yehova adzachinyeketsa monga ngati kuti ndi moto wodzimbaitsa, akumavumbula kuipa kwa chitaganya cha anthu osapembedza ndi kuchisonyeza kukhala choyenerera chiwonongeko chotheratu. Chitaganya cha anthu oipa chimenecho ndicho chimenenso chiri “dziko loyamba,” lotchulidwa pa Chivumbulutso 21:1.
Mogwirizana ndi izi, mawu a Yesu pa Luka 21:33 akuti (“kumwamba ndi dziko lapansi zidzapita, koma . . . ”) ayenera kuzindikiridwa mounikiridwa ndi mawu ofanana nawo a pa Luka 16:17 akuti (“kuti kumwamba ndi dziko lapansi zichoke nkwapafupi, koposa . . . ”), mawu aŵiriwa amangogogomezera kusathekera kwa mikhalidwe yotchulidwayo.—Wonaninso Mateyu 5:18.
Kodi olungama adzatengedwera kumwamba ndiyeno kubwerera padziko lapansi pambuyo pooti oipa awonongedwa?
Kodi Chivumbulutso 21:2, 3 (“NW”) chimachirikiza lingaliro limenelo? Icho chimati: “Ndinawonanso mzinda woyera, Yerusalemu Watsopano, wotsika kumwamba kwa Mulungu ndi wokonzekeretsedwa ngati mkwatibwi wokometseredwa mwamuna wake. Limodzi ndi zimenezo ndinamva mawu ofuula ochokera kumpando wachifumu akuti: ‘Tawonani! Chihema cha Mulungu chiri ndi anthu, ndipo iye adzakhala pamodzi ndi iwo, ndipo iwo adzakhala anthu ake. Ndipo Mulungu mwiniyo adzakhala limodzi nawo.’” (Kodi chenicheni chakuti Mulungu “adzakhala” ndi anthu ndipo “adzakhala limodzi nawo” chimatanthauza kuti adzakhala Munthu wathupi? Zimenezo sizingatheke, chifukwa chakuti Yehova anauza Mose kuti: “Palibe munthu adzandiwona ine ndi kukhala ndi moyo.” [Eks. 33:20] Pamenepa, mogwirizana ndi izi, ziŵalo za Yerusalemu Watsopano sizidzabwereranso padziko lapansi monga zolengedwa zaumunthu. Pamenepa, kodi ndim’lingaliro lotani, kuti Mulungu “adzakhala limodzi ndi” anthu ndipo kodi ndimotani mmene Yerusalemu Watsopano ‘amatsikira kuchokera kumwamba’? Mosakaikira chisonyezero chikupezeka m’Genesis 21:1, amene amanena kuti Mulungu ‘anachezetsa’ Sara, akumamdalitsa ndi mwana wamwamuna muukalamba wake. Eksodo 4:31 amatiuza kuti Mulungu “anawazonda” Aisrayeli mwa kutumiza Mose monga momboli. Luka 7:16 amanena kuti kupyolera mwa uminisitala wa Yesu Mulungu ‘anachezera’ anthu ake. [Onsewo ngochokera mu KJ ndi RS] Matembenuzidwe ena amagwiritsira ntchito liwu lakuti Mulungu “anatembenuzira chisamaliro chake” kwa anthu ake [NW] kapena ‘anasonyeza nkhaŵa’ kaamba ka iwo [NE]. Chotero Chivumbulutso 21:2, 3 chiyenera kutanthauza kuti Mulungu ‘adzachezetsa,’ kapena kukhala, ndi anthu kupyolera mwa Yerusalemu Watsopano wakumwamba, kupyolera mwa amene madalitso adzatsanuliridwa anthu omvera.)
Miy. 2:21, 22: “Owongoka mtima adzakhala m’dziko [“padziko lapansi,” NE], angwiro [“anthu opanda banga,” NE] nadzatsalamo. Koma oipa adzalikhidwa m’dziko, achiwembu adzadulidwamo.” (Tawonani kuti sipamanena kuti opanda bangawo adzabwerera kudziko lapansi koma kuti “adzatsalamo.”)
Kodi chifuno choyambirira cha Mulungu kaamba ka dziko lapansi chinasintha?
Gen. 1:27, 28: “Mulungu ndipo adalenga munthu m’chifanizo chake, m’chifanizo cha Mulungu adamlenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi. Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, mubalane, muchuluke, mudzadze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pansomba za m’nyanja, ndi pambalame za m’lengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwaŵa padziko lapansi.” (Chotero Mulungu anasonyeza chifuno chake cha kukhala ndi dziko lapansi liri lodzazidwa ndi mbadwa za Adamu ndi Hava monga osamalira paradaiso wa dziko lonse. Pambuyo pooti Mulungu walinganiza modabwitsa dziko lapansili kuti likhalidwe ndi anthu, akumalipangitsa kukhala lapadera pakati pa maplaneti onse amene munthu wapenda ndi makina ake owonera kutali ndi zombo zake zam’lengalenga, kodi Mlengi anangosiya chifuno chake, kuchisiyiratu kosatha chiri chosakwaniritsidwa chifukwa cha uchimo wa Adamu?)
Yes. 45:18: “Atero Yehova amene analenga kumwamba, iye ndiye Mulungu amene anaumba dziko lapansi, nalipanga; iye analikhazikitsa, sanalilenga mwachabe; iye analiumba akhalemo anthu; ine ndine Yehova; ndipo palibenso wina.” (Wonaninso Yesaya 55:10, 11.)
Ngati palibe munthu amene adzafa m’Dongosolo Latsopano la Mulungu, kodi ndimotani mmene anthu onse adzakwanira padziko lapansi?
Kumbukirani kuti pamene Mulungu analankhula za chifuno chake kaamba ka dziko lapansi anati: “Mubalane muchuluke mudzadze dziko.” (Gen. 1:28) Mulungu anapatsa munthu mphamvu ya kubala ana, ndipo pamene chifuno Chake pamfundoyo chikwaniritsidwa Iye angakhoze kuchititsa kubala ana kulekeka padziko lapansi.
Kodi ndianthu amtundu wanji amene Mulungu adzapatsa moyo wosatha padziko lapansi?
Zef. 2:3: “Funani Yehova, ofatsa inu nonse a m’dziko, amene munachita chiweruzo chake; funani chilungamo, funani chifatso kapena mudzabisika tsiku lamkwiyo wa Yehova.”
Sal. 37:9, 11: “Iwo akuyembekeza Yehova iwowa adzalandira dziko lapansi. . . . Ofatsa adzalandira dziko lapansi, nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”