Nyimbo 109
Moyo Wosatha Ulonjezedwa
1. Moyo ulonjezedwadi
Ndi Mulungu wamkulu,
Pansi pano muungwiro.
Sikulota ndithu.
(Korasi)
2. Lonjezo la Ya n’lowona
Lidzakwaniritsidwa:
‘Ofatsa adzakondwera.’
Ndi chifuno cha Ya.
(Korasi)
3. Mulungu watsimikiza
Kuchita zatsopano.
Madalitso adzachoka
M’mwamba monga mame.
(Korasi)
4. Yesu anatsimikiza,
Paradaiso adza.
M’dziko latsopano M’lungu
Adzalambiridwa.
(KORASi)
Tingapeze moyo.
Tiyeseyesetse.
Ya ngwodalirika.
Ali wowona.