Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • rs tsamba 79-tsamba 82
  • Chilimbikitso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chilimbikitso
  • Kukambitsirana za m’Malemba
  • Nkhani Yofanana
  • Ufumu
    Kukambitsirana za m’Malemba
  • Chiyembekezo Chomwe Chipembedzo Choona Chimapereka
    Galamukani!—1999
  • Moyo M’Paradaiso
    Galamukani!—2008
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
    Nsanja ya Olonda—2011
Onani Zambiri
Kukambitsirana za m’Malemba
rs tsamba 79-tsamba 82

Chilimbikitso

Tanthauzo: Kanthu kena kamene kamapereka kulimbika mtima kapena kupereka chiyembekezo. Munthu aliyense amafuna chilimbikitso. Kuchipereka kungafunikire kupereka kwanu chithandizo kwa munthuyo kapena kuyamikira. Kaŵirikaŵiri chimaphatikizapo kuthandiza munthu winayo kuwona mmene angalakire mkhalidwe wovuta kapena kukambitsirana zifukwa zokhalira ndi chidaliro cha mtsogolo mwabwinopo. Baibulo limapereka maziko abwino koposa a chilimbikitso choterocho, ndipo malemba ogwidwa mawu pansipa angakhale othandiza m’kuchipereka kwa anthu oyang’anizana ndi mikhalidwe yosiyanasiyana. Panthaŵi zina zabwino kwambiri zimachitidwa mwa kungosonyeza mkhalidwe womvera chifundo.—Aroma 12:15.

Kwa okumana ndi mayeso chifukwa cha MATENDA—

Chiv. 21:4, 5, NW: “[Mulungu] adzapukuta msodzi uliwonse mmaso mwawo, ndipo sikudzakhalanso imfa, ngakhale kulira maliro ngakhale kufuula ngakhale kupweteka sizidzakhalakonso. Zinthu zoyambazo zapita. Ndipo Wokhala pampando wachifumuyo anati: ‘Tawonani! Ndikupanga zinthu zonse zatsopano’. Ndiponso, iye akuti: ‘Lemba, chifukwa chakuti mawu amenewa ngokhulupirika ndi owona.’”

Mat. 9:35: “Yesu anayendayenda m’mizinda yonse ndi m’midzi, namaphunzitsa . . . nalalikira uthenga wabwino wa ufumuwo, nachiritsa nthenda iriyonse ndi zofooka zonse.” (Mwa kugwirizanitsa kuchiritsa kotero ndi kulalikidwa kwa Ufumu, Yesu anapereka kuwonedweratu kwapasadakhale kosangalatsa kwa zimene iye adzachitira anthu mkati mwa Kulamulira kwake kwa Zaka Chikwi.)

2 Akor. 4:13, 16: “Ifenso tikhulupirira . . . Chifukwa chake sitifooka; koma ungakhale umunthu wathu wakunja [thupi lathu lanyama] uvunda, wamkati mwathu ukonzedwa kwatsopano [kapena kupatsidwa nyonga yatsopano] tsiku ndi tsiku.” (Tingakhale tikulefuka kuthupi. Koma kuuzimu tikupangidwa atsopano pamene tikupitirizabe kulimbikitsidwa ndi malonjezo amtengo wapatali a Mulungu.)

Wonaninso Luka 7:20-23.

Kwa anthu otayikiridwa ndi okondedwa awo mu IMFA—

Yes. 25:8, 9: “Iye wameza imfa kunthaŵi yonse; ndipo Ambuye Mulungu adzapukuta misozi pankhope zonse. . . . Ndipo adzanena tsiku limenelo, Tawonani, uyu ndiye Mulungu wathu; tamlindirira iye, adzatipulumutsa; uyu ndiye Yehova, tamlindirira iye, tidzakondwa ndi kusekerera m’chipulumutso chake.”

Yoh. 5:28, 29: “Musazizwe ndi ichi, kuti ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira, amene adachita zabwino, kukuuka kwa moyo; koma amene adachita zoipa kukuuka kwa kuweruza.”

Yoh. 11:25, 26: “Yesu anati kwa iye, ine ndine kuuka ndi moyo; wokhulupirira ine angakhale amwalira adzakhala ndi moyo; ndipo yense wakukhala ndi moyo, nakhulupirira ine sadzamwalira nthaŵi yonse. Kodi ukhulupirira ichi?”

Sal. 146:5, 9: “Wodala munthu amene . . . chiyembekezo chake chiri pa Yehova Mulungu wake. . . . Agwiriziza mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye.” (Panthaŵi ino Mulungu ali ndi nkhaŵa yachikondi yoteroyo kwa oferedwa.)

Wonaninso Luka 7:11-16; 8:49-56.

Kwa anthu oyang’anizana ndi CHIZUNZO chifukwa cha kuchita chifuniro cha Mulungu—

Sal. 27:10: “Pakuti wandisiya atate wanga ndi amayi wanga, koma Yehova anditola.”

1 Pet. 4:16: “Koma akamva zoŵaŵa ngati Mkristu asachite manyazi; koma alemekeze Mulungu m’dzina iri.”

Miy. 27:11: “Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.” (Mwa kukhulupirika timapereka yankho lonena za chinenezo chonama cha Satana chakuti palibe munthu wovutika kwambiri adzapitirizabe kutumikira Mulungu.)

Mat. 5:10-12, NW: “Achimwemwe ali awo amene azunzidwa chifukwa cha chilungamo, popeza kuti ufumu wakumwamba uli wawo. Achimwemwe muli inu pamene anthu akutonzani ndi kukuzunzani ndi kukunenerani chinthu choipa chamtundu uliwonse monama chifukwa cha ine. Kondwerani ndi kulumpha chifukwa cha chisangalalo, popeza kuti mphotho yanu iri yaikulu m’mwamba; pakuti m’njira imeneyo iwo anazunza aneneri musanakhale inu.”

Mac. 5:41, 42: “Pamanepo [atumwi] ndipo anapita kuchokera kubwalo la akulu, nakondwera kuti anayesedwa oyenera kunyozedwa chifukwa cha dzinalo. Ndipo masiku onse, m’kachisi ndi m’nyumba, sanaleka kuphunzitsa ndi kulalikira Kristu Yesu.”

Afil. 1:27-29: “Chokhachi, mayendedwe anu ayenere uthenga wabwino wa Kristu . . . osawopa adani m’kanthu konse, chimene chiri mwa iwowa chisonyezo cha chiwonongeko, koma kwa inu cha chipulumutso ndicho cha kwa Mulungu; kuti kwapatsidwa kwa inu kwaufulu chifukwa cha Kristu, sikukhulupirira kwa iye kokha, komatunso kumva zoŵaŵa chifukwa cha iye.”

Kwa otaya mtima chifukwa cha CHISALUNGAMO—

Sal. 37:10, 11: “Katsala kanthaŵi ndipo oipa adzatha psiti: inde, udzayang’anira mbuto yake, nudzapeza palibe. Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”

Yes. 9:6, 7: “Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala papheŵa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu Wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa Mtendere. Za kuenjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha pampando wachifumu wa Davide, ndi pa ufumu wake, kuukhazikitsa, ndi kuuchirikiza ndi chiweruziro ndi chilungamo, kuyambira tsopano ndi kumkabe nthaŵi zonse. Changu cha Yehova wa makamu chidzachita zimenezi.”

Dan. 2:44: “Masiku a mafumu aja Mulungu wakumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka kunthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse, nudzakhala chikhalire.”

Wonaninso Yesaya 32:1, 2; 2 Petro 3:13.

Kwa opanikizika kwambiri ndi MAVUTO AZACHUMA—

Yes. 65:21, 22: “Iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzawoka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zake. Iwo sadzamanga ndi wina kukhalamo; iwo sadzawoka, ndi wina kudya . . . adzasangalala nthaŵi zambiri ndi ntchito zamanja awo.”

Sal. 72:8, 16: “Adzachita [Mfumu Yaumesiya] ufumu kuchokera kunyanja kufikira kunyanja, ndi kuchokera ku Mtsinje kufikira kumalekezero adziko lapansi. M’dzikomo mudzakhala dzinthu zochuluka pamwamba pa mapiri.”

Mat. 6:33, NW: “Pamenepo, pitirizani, kufunafuna choyamba ufumu ndi chilungamo chake, ndipo zinthu zina zonsezo [zofunika za moyo] zidzawonjezeredwa kwa inu.”

Aroma 8:35, 38, 39: “Adzatisiyanitsa ndani ndi chikondi cha Kristu? Nsautso kodi, kapena kupsinjika mtima, kapena kuzunza, kapena njala, kapena usiŵa, kapena zowopsa kapena lupanga kodi? Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu ziripo, ngakhale zinthu zirinkudza, ngakhale zimphamvu, ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chirichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chiri mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.”

Wonaninso Ahebri 13:5, 6.

Kwa anthu olefuka chifukwa cha ZOPHOPHONYA za iwo eni—

Sal. 34:18: “Yehova ali pafupi ndi iwo amtima wosweka, apulumutsa iwo amzimu wolapadi.”

Sal. 103:13, 14: “Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuwopa iye. Popeza adziŵa mapangidwe athu; akumbukira kuti ndife fumbi.”

Neh. 9:17: “Inu ndinu Mulungu wokhululukira, wachisomo, ndi wansoni, wolekereza, ndi wochuluka chifundo.”

2 Pet. 3:9, 15: “Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa. Ndipo yesani kulekerera kwa Ambuye wathu chipulumutso.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena