Nyimbo 222
Yang’ananibe Maso Anu Pamphotho!
1. Pomwe akhungu apenya
Ndipo ogontha amvanso,
Pamene madzi abwino
Adzayenda m’chipululu,
Wopuŵala adzadumpha,
Okondedwa sadzafanso—
Udzawonatu nthaŵiyo,
Poyang’anabe pamphotho.
2. Wosalankhula ’lankhula,
Wokalamba ku’nyamata,
Pomwe dziko litulutsa
Chuma, zabwino nzosatha
Pomveka nyimbo za ana,
Padzakhalatu mtendere,
Ndi akufa adzauka,
Poyang’anabe pamphotho.
3. Mmbulu ndi mwana wankhosa,
Mwana wang’ombe pamodzi,
Mwana adzatsogolera,
Ndipo zonsezidzamvera.
Pamene mantha, misozi,
Ndi kupweteka zichoka,
M’lungu agaŵira zonse,
Poyang’anabe pamphotho.