Nyimbo 180
Bukhu la Mulungu—Chuma
1. Pali Bukhu, lamasamba ambiri,
Libweretsa mtendere kwa anthu.
Malingaliro ake ngamphamvudi;
Lichititsa ‘akhungu’ kuwona.
Bukhulo ndi Baibulo loyera.
Linalembedwa mouziridwa,
Ndi anthu okonda Yehova M’lungu,
Mzimu wake unawathandiza.
2. Analemba cholembedwa chowona,
Za chilengedwe chake chonsecho.
Anenanso za ungwiro wa munthu
Ndi kutayika kwa Paradaiso.
Anena za mngelo wina amene
Anapandukira Ufumuwo.
Ndi kutsogoza anthu muuchimo,
Koma Yehova adzalakika.
3. Tikhalatu ndi moyo muchimwemwe.
Ufumu wa Mulungu wayamba.
Yehova wapatsa chipulumutso
Kwa onse omadza kwa iye yo.
Mbiriyi timaipeza m’bukhulo;
Simafanananso ndi golidi.
Ipatsa chiyembekezo choposa;
Imaposatu mbiri zonsezo.