-
Nkukhaliranji Woyamikira?Nsanja ya Olonda—1998 | February 15
-
-
samanena ngakhale liwu losavutalo lakuti “zikomo.” Kuyamikira kukupitirizabe kuloŵedwa m’malo ndi mzimu wa “ine choyamba.” Mkhalidwe umenewu ndiwo chimodzi mwa zizindikiro za masiku otsiriza. Mtumwi Paulo anachenjeza kuti: “Uyenera kudziŵa kuti m’masiku otsiriza nthaŵi zizadzala ndi ngozi. Anthu adzakhala odzikonda okha kwadzaoneni . . . Iwo adzakhala osayamika mpang’ono pomwe.”—2 Timoteo 3:1, 2, Phillips.
Nthaŵi zina, kusyasyalika kumaloŵa m’malo mwa kuyamikira. Mawu oyamikira amachokera mumtima popanda kufuna kupindulapo kanthu. Komabe, kusyasyalika, kumene nthaŵi zambiri kumakhala kwaukathyali ndiponso kokokomeza, kungachokere pacholinga chobisika cha kufuna kukwezedwa kapena kupezerapo zinthu zina zaumwini. (Yuda 16) Kuwonjezera pa kunyenga munthu amene akuuzidwa zimenezo, kusyasyalika kotero kumakhala chipatso cha kunyada ndi kudzitukumula. Choncho, ndani angafune kusyasyalikidwa mwaukathyali? Koma kuyamikira kwenikweni kumatsitsimuladi moyo.
Munthu wosonyeza kuyamikira amapindula ndi kuchita zimenezo. Chikondi chimene amakhala nacho chifukwa chokhala woyamikira kuchokera pansi pa mtima chimamthandizira kukhala ndi chimwemwe ndi mtendere. (Yerekezerani ndi Miyambo 15:13, 15.) Ndiponso popeza kuti ndi mkhalidwe wabwino, kuyamikira kumamtetezera kuti asakhale ndi malingaliro oipa monga mkwiyo, nsanje, ndi kuipidwa.
“Khalani Akuyamika”
Baibulo limatilimbikitsa kukulitsa mzimu woyamikira. Paulo analemba kuti: “M’zonse yamikani; pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu cha kwa inu, mwa Kristu Yesu.” (1 Atesalonika 5:18) Ndiponso Paulo analangiza Akolose kuti: “Mtendere wa Kristu uchite ufumu m’mitima yanu, . . . ndipo khalani akuyamika.” (Akolose 3:15) Masalmo ambiri ali ndi mawu oyamikira, zimene zikusonyeza kuti kuyamikira kochokera mumtima ndi mkhalidwe wabwino waumulungu. (Salmo 27:4; 75:1) Ndithudi, Yehova Mulungu amakondwera pamene tisonyeza kuyamikira pazinthu za tsiku ndi tsiku.
Koma kodi ndi zinthu zotani m’dziko lino losayamika zimene zimachititsa kuti kukulitsa mzimu woyamikira kukhale kovuta kwa ife? Kodi tingausonyeze motani mzimu woyamikira pamoyo watsiku ndi tsiku? Mafunso ameneŵa adzayankhidwa m’nkhani yotsatira.
-
-
Kulitsani Mzimu WoyamikiraNsanja ya Olonda—1998 | February 15
-
-
Kulitsani Mzimu Woyamikira
DOKOTALA wina m’Boma la New York apulumutsa moyo wa Marie atadwala kwadzaoneni. Koma Marie wazaka 50 sayamikira dokotalayo kapena kumlipira ngongole yake. Kumeneku ndiko kusayamikira!
Baibulo limasimba kuti nthaŵi ina, Yesu ataloŵa m’mudzi wina, anakumana ndi amuna khumi odwala matenda osautsa kwambiri a khate. Iwo anafuula ndi mawu aakulu kwa iye kuti: “Yesu, Mbuye, mutichitire chifundo.” Yesu anawauza kuti: “Pitani, kadzionetseni nokha kwa ansembe.” Odwala khatewo anamvera malangizo ake, ndipo adakali paulendowo, iwo anayamba kuona ndi kumva kuti akukhalanso athanzi.
Asanu ndi anayi ochiritsidwa matenda a khate anapitiriza ulendo wawo. Koma wakhate mmodzi, Msamariya, anabwerera kukafunafuna Yesu. Wochira matenda a khate ameneyu anatamanda Mulungu, ndipo atampeza Yesu, anagwa pamapazi ake, namthokoza. Poyankha Yesu anati: “Kodi sanakonzedwa khumi? Koma ali kuti asanu ndi anayi aja? Akubwera kulemekeza Mulungu sanapezeka mmodzi kodi, koma mlendo uyu?”—Luka 17:11-19.
Funsolo lakuti: “Koma ali kuti asanu ndi anayi aja?” lili phunziro lofunika kwambiri. Mofanana ndi Marie, akhate asanu ndi anayiwo anali ndi chofooka chachikulu kwambiri—sanasonyeze chiyamikiro. Kusayamikira kotero nkofala kwambiri lerolino. Kodi chifukwa chake nchiyani?
Chochititsa Chenicheni cha Kusayamikira
Kwenikweni, munthu amakhala wosayamikira chifukwa cha dyera. Talingalirani za makolo athu oyamba aumunthu, Adamu ndi Hava. Yehova anawalenga ndi mikhalidwe yaumulungu ndipo anawapatsa zonse zofunikira kuti akhale achimwemwe, kuphatikizapo mudzi wonga munda wokongola, malo angwiro owazinga, ndi ntchito yopindulitsa ndiponso yokhutiritsa. (Genesis 1:26-29; 2:16, 17) Komabe, atakopeka ndi zonena za Satana zokhudza ubwino wawo, onse aŵiriwo monga banja anakhala osamvera ndipo anaipidwa ndi kuoloŵa manja kwa Yehova.—Genesis 3:1-5; Chivumbulutso 12:9.
Lingaliraninso za anthu a m’Israyeli wakale, amene Mulungu anawasankha kukhala chuma chake chapadera. Makolo onse achiisrayeli ayenera kuti anayamikira kwambiri usiku wa pa Nisani 14, 1513 B.C.E.! Pausiku wosaiŵalikawo, mngelo wa Mulungu anapha “ana oyamba onse m’dziko la Aigupto” koma anapitirira nyumba za Aisrayeli zolembedwa bwino zizindikiro. (Eksodo 12:12, 21-24, 30) Ndipo atalanditsidwa kwa gulu lankhondo la Farao pa Nyanja Yofiira, “Mose ndi ana a Israyeli anaimbira Yehova nyimbo” ndi mitima yodzala ndi kuyamikira.—Eksodo 14:19-28; 15:1-21.
Komabe, milungu ingapo yokha atatuluka m’Igupto, ‘khamu lonse la ana a Israyeli linadandaula.’ Iwo anakhala osayamikira mwamsanga chotani nanga! Iwo anayamba kudandaula kuti ‘sakukhala pamiphika ya nyama, kudya mkate chokhuta,’ zinthu zimene anali kuchita ku Igupto, dziko la ukapolo wawo. (Eksodo 16:1-3) Ndithudi, dyera limatsutsana ndi kukulitsa chiyamikiro ndi kuchisonyeza.
Pokhala mbadwa za Adamu wochimwayo, anthu onse amabadwa ndi dyera linalake ndiponso ndi mkhalidwe wina wosafuna kuyamikira. (Aroma 5:12) Kusayamikira kulinso mbali ya mzimu wadyera umene ukulamulira anthu a m’dziko lino. Monga mpweya umene timapuma, mzimu umenewo uli paliponse, ndipo umatikhudza. (Aefeso 2:1, 2) Choncho, tifunikira kukulitsa mkhalidwe woyamikira. Kodi tingazichite motani zimenezi?
Kusinkhasinkha Nkofunika Kwambiri!
Dikishonale yotchedwa Webster’s Third New International Dictionary imatanthauzira kuyamikira kuti ndiko “kukhala wothokoza: kukonda ndiponso kukhala waubwenzi kwa munthu wooloŵa manja, zimene zimasonkhezera kumchitira chabwino mombwezera.” Munthu sangakhudzike mtima ndipo nthaŵi yomweyo nkusakhudzikanso mtima atangofuna monga kuti ndi makina; kukhudzika mtima kumayenera kuyamba mwachibadwa mumtima. Kuyamikira sindiko kungosonyeza mwambo kapena khalidwe labwino; kumachokera mumtima.
Kodi tingaphunzire motani kukhala woyamikira kuchokera pansi pa mtima? Baibulo limanena kuti nthaŵi zambiri kukhudzika mtima kwathu kumadalira pa zimene timakonda kuganizira. (Aefeso 4:22-24) Kuphunzira kuyamikira kumayamba pamene tisinkhasinkha moyamikira pa zinthu zosonyeza kukoma mtima zimene timalandira. Mogwirizana ndi zimenezi, Dr. Wayne W. Dyer, amene amagwira ntchito ya zathanzi la malingaliro, anati: “Sungakhudzike mtima usanaganizire zinazake choyamba.”
Mwachitsanzo, tiyeni tinene za kuyamikira chilengedwe chotizinga. Mutayang’ana kuthambo kodzaza nyenyezi usiku pamene kulibe mitambo, kodi mumamva bwanji pa zimene mukuona? Mfumu Davide anafotokoza mmene anazizwira kuti: “Pakuona ine thambo la kumwamba lanu, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika, munthu ndani kuti mumkumbukira? Ndi mwana wa munthu kuti mucheza naye?” Ndiponso usiku kuli kopanda phokoso, nyenyezi zinalankhula kwa Davide, ndipo anasonkhezeredwa kulemba kuti: “Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo lionetsa ntchito ya manja ake.” Kodi nchifukwa ninji Davide anakhudzika mtima kwambiri ndi thambo la nyenyezi? Iye akudziyankhira kuti: “Zija mudazichita ndilingirirapo; ndikamba pandekha za ntchito ya manja anu.”—Salmo 8:3, 4; 19:1; 143:5.
Nayenso mwana wa Davide, Solomo, anali kudziŵa kufunika kwa kuganiza za kudabwitsa kwa zinthu zachilengedwe. Mwachitsanzo, ponena za ntchito ya mitambo yamvula yogwetsa madzi padziko lathu lapansili, iye analemba kuti: “Mitsinje yonse ithira m’nyanja, koma nyanja yosadzala; komwe imukira mitsinjeyo, komweko ibweranso.” (Mlaliki 1:7) Zimatero kuti mvula ndi mitsinje zikadzaza madzi padziko lapansi, madzi amenewo amachoka m’nyanja ndi kusandukanso mitambo. Kodi dzikoli likanakhala lotani chipanda kuyeretsa ndi kusandulika kwa madzi kumeneku? Solomo ayenera kuti anayamikira chotani nanga pamene anaganizira zinthu zimenezi!
Munthu woyamikira amaonanso kuti unansi wake ndi achibale, mabwenzi, ndi anzake ngwofunika kwambiri. Kukoma mtima kwawo kumamkopa. Pamene alingalira moyamikira za chifundo chawo, amayamikira kuchokera pansi pa mtima.
Kutchula Mawu Oyamikira
Mawu akuti “zikomo” ngosavuta chotani nanga! Kutchula mawu amenewo nkosavuta mpang’ono pomwe. Ndiponso pamakhala mpata waukulu wotchulira mawuwa. Mawu akuti Zikomo otchulidwa mwachikondi kuchokera pansi pa mtima ngotsitsimula chotani nanga kwa munthu amene watitsegulira chitseko kapena amene watola ndi kutipatsira chinthu chimene tagwetsa! Kumva mawu amenewo kungapangitse ntchito ya wogulitsa m’sitolo kapena ya woperekera zakudya palesitilanti kapena ya wopereka makalata kukhala yopepuka ndiponso yopindulitsa kwambiri.
Kutumiza makhadi oyamikira ndi njira yabwino yosonyezera kuti mukuyamikira kukoma mtima kwa ena. Makhadi ambiri opezeka m’masitolo amafotokoza malingaliro amenewo m’njira yosangalatsa kwambiri. Koma kodi sikungakhale kwachikondi kusonyeza malingaliro anu aumwini mwa kulembaponso mawu ena oyamikira ndi dzanja lanu? Ndipo ena amasankha ngakhale kusagwiritsira ntchito khadi, natumiza kalata yolemba okha!—Yerekezerani ndi Miyambo 25:11.
Mwinanso, oyenera kuyamikiridwa kwambiri ndi awo oyandikana nafe kwambiri panyumba. Baibulo limanena za mkazi wabwino kuti: ‘Mwamuna wake amtama.’ (Miyambo 31:28) Kodi mwamuna akamayamikira mkazi wake kuchokera pansi pa mtima sizimapangitsa panyumba kukhala pamtendere ndiponso anthuwo kukhala okhutira? Ndiponso kodi mwamuna samakondwera kufika panyumba ndi kulandira moni wachikondi ndi woyamikira kuchokera kwa mkazi wake? Masiku ano, ukwati umakhala ndi mavuto ambiri, ndipo mavutowo akachuluka, anthu amakwiya msanga. Wokonda kuyamikira sachedwa kulolera ndipo zinthu zokwiyitsa amazinyalanyaza nakhululukira mosavuta.
Achinyamata nawonso afunikira kukumbukira kumayamikira makolo awo kuchokera pansi pa mtima. Inde, makolo ngopanda ungwiro, koma chimenecho sichingakhale chifukwa chosakhalira woyamikira pazimene akuchitirani. Chikondi ndi chisamaliro chimene apereka kuyambira pamene munabadwa sichingagulidwe ndi ndalama. Ngati akuphunzitsani chidziŵitso cha Mulungu, muli ndi chifukwa chinanso chokhalira woyamikira.
“Ana ndiwo cholandira cha kwa Yehova,” limatero Salmo 127:3. Choncho makolo ayenera kupeza mpata woyamikirira ana awo m’malo mowakwiyitsa chifukwa cha zophophonya zawo zing’onozing’ono. (Aefeso 6:4) Ndipotu makolo ali ndi mwaŵi waukulu chotani nanga wothandiza achinyamata amene akuwasamalira kukulitsa mzimu woyamikira.—Yerekezerani ndi Miyambo 29:21.
Kuyamikira Mulungu
Yehova Mulungu ndiye Mpatsi wa “mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro.” (Yakobo 1:17) Makamaka mphatso ya moyo ndiyo yofunika koposa, popeza kuti zonse zimene tili nazo kapena zimene tingafune kuchita zingakhale zopanda pake ngati tataya moyo. Malemba amatilimbikitsa kukumbukira kuti “chitsime cha moyo chili ndi [Yehova Mulungu].” (Salmo 36:5, 7, 9; Machitidwe 17:28) Kuti tikhale ndi mtima woyamikira Mulungu, tifunikira kusinkhasinkha pa zimene amatigaŵira mooloŵa manja zimene zimachirikiza moyo wathu wakuthupi ndi wauzimu. (Salmo 1:1-3; 77:11, 12) Mtima umenewu udzatisonkhezera kusonyeza kuyamikira m’mawu ndiponso mwa zochita zathu.
Pemphero ndiyo njira ina yodziŵikiratu imene tingasonyezere Mulungu kuti timamuyamikira. Wamasalmo Davide anati: “Inu, Yehova, Mulungu wanga, zodabwiza zanu mudazichita nzambiri, ndipo zolingirira zanu za pa ife; palibe wina wozifotokozera Inu; ndikazisimba ndi kuzitchula, zindichulukira kuziŵerenga.” (Salmo 40:5) Ifenso tifunikira kusonkhezereka ngati iyeyo.
Davide anatsimikizanso mtima kusonyeza Mulungu chiyamikiro chake mwa mawu ake kwa ena. Iye anati: “Ndidzayamika Yehova ndi mtima wanga wonse; ndidzaŵerengera zodabwiza zanu zonse.” (Salmo 9:1) Kulankhula kwa ena ponena za Mulungu, kufotokoza malingaliro athu mwa kugaŵana nawo choonadi cha m’Mawu ake, mwina ndiko njira yabwino koposa yomsonyezera chiyamikiro chathu. Ndipo zimenezi zidzatithandiza kuyamikira kwambiri mbali zinanso za moyo.
“Wopereka nsembe yachiyamiko andilemekeza Ine; ndipo kwa iye wosunga mayendedwe ake ndidzamuonetsa chipulumutso,” Yehova akutero. Khalanitu ndi chimwemwe chimene chimadza mwa kusonyeza chiyamikiro chanu chochokera pansi pa mtima kwa iye.—Salmo 50:23; 100:2.
[Chithunzi patsamba 7]
Moyo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. Wonjezeranipo malingaliro anu aumwini
-