-
MpatukoKukambitsirana za m’Malemba
-
-
Mose ndi Aroni, nati, Dzipatuleni pakati pa khamu lino kuti ndiwathe m’kamphindi.”
Sikokha kuti iwo amakana chikhulupiriro chowona koma iwo “amamenya” atsamwali awo oyambawo, akumagwiritsira ntchito chisulizo chapoyera ndi njira zina kudodometsa ntchito yawo; zoyesayesa za ampatuko amenewa zalunjikitsidwa pa kugwetsa, osati kumanga
Mat. 24:45-51: “Ndani kodi ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake anamkhazika woyang’anira banja lake, kuwapatsa zakudya panthaŵi yake? . . . Koma kapolo woipa akanena mumtima mwake, Mbuye wanga wachedwa; nadzayamba kupanda anzake, nadya ndi kumwa pamodzi ndi oledzera, mbuye wa kapoloyo adzafika tsiku losamuyembekezera iye, ndi nthaŵi yosadziŵa iye, nadzamdula, nadzaika pokhala pake ndi anthu onyenga.”
2 Tim. 2:16-18: “Koma peŵa nkhani zopanda pake; pakuti adzapitirira kutsata chisapembedzo, ndipo mawu awo adzanyeka chironda; a iwo ali Humenayo ndi Fileto; ndiwo amene adasokera kunena za chowonadi, ponena kuti kuuka kwa akufa kwachitika kale, napasula chikhulupiriro cha ena.”
Kodi Akristu okhulupirika akalandira ampatuko, kaya mwa kucheza nawo kapena mwa kuŵerenga mabukhu awo?
2 Yoh. 9, 10: “Yense wakupitirira, wosakhala m’chiphunzitso cha Kristu, alibe Mulungu; . . . munthu akadza kwa inu, wosatenga chiphunzitso ichi, musamlandire iye kunyumba, ndipo musamlankhule.”
Aroma 16:17, 18: “Ndipo ndikudandaulirani, abale, yang’anirani iwo akuchita zopatutsana ndi zophunthwitsa, kosalingana ndi chiphunzitsocho munachiphunzira inu; ndipo potolokani kwa iwo. . . . ndi mawu osalaza ndi osyasyalika kusokeretsa mitima ya osalakwa.”
Kodi chivulazo chowopsa chirichonse chingadze kuchokera m’kukhutiritsa chidwi cha munthuwe ponena za maganizo a ampatuko?
Miy. 11:9, NW: “Wampatuko abweretsa chiwonongeko pa munthu mnzake ndi mkamwa mwake.”
Yes. 32:6: “Wopusa adzanena zopusa, ndi mtima wake udzachita mphulupulu, kuchita zoipitsa, ndi kunena za Yehova molakwira, kusoŵetsa konse mtima wanjala, ndi kulepheretsa chakumwa cha waludzu.” (Yerekezerani ndi Yesaya 65:13, 14.)
Kodi mpatuko ngwaupandu motani?
2 Pet. 2:1: “Amene adzaloŵa nayo mtseri mipatuko yotaikitsa, nadzakana Ambuye amene adawagula, nadzadzitengera iwo okha chitayiko chakudza msanga.”
Yobu 13:16, NW: “Wampatuko sadzafika pamaso pake [pa Mulungu].”
Aheb. 6:4-6: “Sikutheka kuwakonzanso, atembenuke mtima, iwo amene anawonetsedwa panthaŵi yake, nalaŵa mphatso yakumwamba, nakhala olandirana naye mzimu woyera, nalaŵa mawu okoma a Mulungu, ndi mphamvu ya nthaŵi irinkudza, koma anagwa m’chisokero [“ngati panthaŵiyo achita mpatuko,” RS]; popeza adzipachikiranso okha Mwana wa Mulungu, namchititsa manyazi poyera.”
-
-
MtandaKukambitsirana za m’Malemba
-
-
Mtanda
Tanthauzo: Chiwiya chimene Yesu Kristu anaphedwerapo chimanenedwa ndi ambiri m’Dziko Lachikristu kukhala mtanda. Liwulo likuchokera ku liwu Lachilatini lakuti crux.
Kodi nchifukwa ninji mabukhu a Watch Tower amasonyeza Yesu ali pamtengo manja ali pamwamba pa mutu wake mmalo mwa pamtanda wodziŵika?
Liwu Lachigiriki lotembenuzidwa “mtanda” m’matembenuzidwe amakono ambiri a Baibulo (“mtengo wozunzirapo” mu NW) ndiro stau·rosʹ. M’Chigiriki chakale, liwuli linatanthauza mzati, kapena mlongoti. Pambuyo pake linadzagwiritsiridwa ntchito kukhala mtengo wonyongera wokhala ndi thabwa lopingasa. The Imperial Bible-Dictionary limavomereza zimenezi, kumati: “Liwu Lachigriki la mtanda, [stau·rosʹ], moyenerera limatanthauza mtengo, mzati, mlongoti, kapena mtengo wonyongera pamene chinthu chirichonse chingakoloŵekedwe, kapena chimene chingagwiritsiridwe ntchito kukhomerapo [kuchinga] chigawo cha malo. . . . Ngakhale pakati pa Aroma crux (kuchokera kumene liwu lathu lakuti mtanda latembenuzidwako)
-