Nyimbo 49
Mulungu Wamkulu, Yehova!
1. M’lungu Wamkulu, Wamwambamwamba,
Tikukuimbirani, Tiyenda m’njira zanu.
Ndinu Atate, Mfumu, Kalonga.
Tiri ndi mangawa nanu kosatha.
O Mulungu, ndinu wabwino ndithu.
Mutithandize kutumikira.
Tilemekezetu dzina lanulo,
ndi kutumikirabe mokhutira.
Inu ndinutu wopatsa moyo.
Munatipatsa zonse.
2. M’lungu Wamkulu, Wamphamvuyonse,
Tikondwa m’ntchito yanu, Pochita ntchito yathu.
Mulitu Nsanja, Mphamvu yathudi.
Tikudalirani ndi mtima wonse.
O Mulungu, ndinu wachikondidi.
M’katithandiza sitidzalakwa.
Tiumirire ku zifuno zanu
Ndi kutumikira inu, nokhanu.
Mulitu linga, Chikopa chathu.
Timakudalirani.
3. M’lungu Wamkulu, Mbusa, Mlangizi,
Mumatiyang’anira, Mumatidera nkhaŵa.
Mpulumutsidi, Ndi woombola.
Tingadze kwa inu mumapemphero.
O Mulungu, ndinu wokoma mtima.
Titonthozedwa moyenerera.
Timalemekeza dzina lanulo
Mudzakhala monga momwe mufuna.
Mbuye Yehova, Palibe wina,
kusiyapo nokhanu.