-
ArmagedoKukambitsirana za m’Malemba
-
-
tsopano kuti lipindulitse makolo ndi ana omwe. Kodi sikukakhala kwanzeru kwa makolo kulondola njira imene ikachititsa ana awo kukhala owonedwa mwachiyanjo ndi Mulungu tsopano ndi pa Armagedo pomwe?
Kodi chikondi cha Mulungu chimaswedwa mwa kuwonongedwa kwa oipa?
2 Pet. 3:9: “Ambuye . . . aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.”
Luka 18:7, 8: “Kodi Mulungu sadzachitira chilungamo osankhidwa ake akumuitana usana ndi usiku, popeza aleza nawo mtima? Ndinena ndi inu, adzawachitira chilungamo posachedwa.”
2 Ates. 1:6: “Nkolungama kwa Mulungu kubwezera chisautso kwa iwo akuchitira inu [atumiki ake] chisautso.”
Kodi nkotheka kukhala mu mkhalidwe wauchete?
2 Ates. 1:8, NW: “Amadzetsa kulipsira pa awo amene [mwa kudzisankhira] samadziŵa Mulungu ndi awo amene samamvera mbiri yabwino yonena za Ambuye Yesu.”
Mat. 24:37-39: “Monga masiku a Nowa . . . iwo sanadziŵa kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa munthu.”
Mat. 12:30: “Iye wosakhala pamodzi ndi ine akana ine, ndi iye wosasonkhanitsa pamodzi ndi ine amwazamwaza.”
Yerekezerani ndi Deuteronomo 30:19, 20.
Kodi nchisonkhezero chayani chimene chikukankhira amitundu kumkhalidwe wa padziko lonse umene udzachititsa kumenyana ndi Mulungu?
Chiv. 16:13, 14, NW: “Ndinawona mawu atatu onyansa ouziridwa amene anawonekera ngati achule amene atuluka mkamwa mwa chinjoka [Satana Mdyerekezi; Chiv. 12:9] ndi mkamwa mwa chirombo ndi mkamwa mwa mneneri wonyenga. Iwo, kunena zowona, ali mawu ouziridwa ndi ziwanda ndipo amachita zizindikiro, ndipo iwo amapita kwa mafumu a dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu, kuwasonkhanitsira pamodzi ku nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.”
Yerekezerani ndi Luka 4:5, 6; 1 Yohane 5:19; ndiponso Machitidwe 5:38, 39; 2 Mbiri 32:1, 16, 17.
-
-
AyudaKukambitsirana za m’Malemba
-
-
Ayuda
Tanthauzo: Monga momwe akugwiritsidwira ntchito mofala lerolino, mawuwa akusonya kwa anthu a mbadwa Zachihebri ndi ena amene atembenuzidwira ku Chiyuda. Baibulo limasonyanso chenicheni chakuti pali Akristu amene ali Ayuda mwauzimu ndi amene amapanga “Israyeli wa Mulungu.”
Kodi Ayuda achibadwidwe lerolino ali anthu osankhidwa a Mulungu?
Chimenecho ndicho chikhulupiriro cha Ayuda ambiri. Encyclopaedia Judaica (Jerusalem, 1971, Vol. 5, danga 498) imati: “ANTHU OSANKHIKA, malongosoledwe odziŵika anthu Achiisrayeli osonyeza unansi wapadera ndi wosayerekezereka kwa mulungu wachilengedwe chonse. Lingaliro limeneli lakhala lalikulukulu m’mbiri yonse ya ganizo Lachiyuda.”—Wonani Deuteronomo 7:6-8; Eskodo 19:5.
Ochuluka m’Dziko Lachikristu ali ndi malingaliro ofanana. Chigawo cha “Chipembedzo” cha Journal and Constitution (January 22, 1983, p. 5-B) ya Atlanta inasimba kuti: “Mosiyana ndi ziphunzitso za matchalitchi za zaka mazana ambiri zakuti Mulungu ‘anatemberera anthu ake Israyeli’ ndi kuloŵedwa mmalo ndi ‘Israyeli watsopano,’ iye [Paul M. Van Buren, wophunzitsa Zaumulungu pa Yunivesite ya Temple mu Philadelphia] akunena kuti tsopano matchalitchi akutsimikizira kuti ‘pangano pakati pa Mulungu ndi anthu Achiyuda nlamuyaya. Kusintha kwa ganizo kozizwitsa kumeneku kwapangidwa ndi Aprotesitanti ndi Akatolika, kumbali zonse ziŵiri za Atlantic.’” The New York Times (February 6, 1983, p. 42) inawonjezera kuti: “‘Pali chokondweretsa ponena za kuyenera kwa uthenga wabwino ndi Israyeli ndi chikhulupiriro chakuti chirichonse chimene Aisrayeli achita chiyenera kuchirikizidwa, chifukwa chakuti Mulungu ali kumbali ya Israyeli,’ anatero Timothy Smith, profesala wa zaumulungu pa Yunivesite
-