Nyimbo 196
Odzipatulira a Yehova
1. Palitu mtundu wina,
Wodzipereka m’moyo.
Umamvera Yehova,
Umabweretsa nkhosa.
2. Khamu lawonekera.
Nlokondedwa ndi Mbusa.
Liri lobatizidwa,
Iye akulifupa.
3. Amamka nalalika,
Molimba mtima ndithu.
Ndi awo otsalira,
Alitu ngati ‘mame.’
4. “Kagulu kankhosa” ndi
“Nkhosa zina” zidala.
Zimatsanzira Kristu,
Nazikondwetsa M’lungu.