-
Khalani ‘m’Mudzi Wopulumukirako’ Nimukhale ndi Moyo!Nsanja ya Olonda—1995 | November 15
-
-
20. Kuti atetezereke kwa Wolipsa mwazi, kodi aja okhala m’mudzi wophiphiritsira wopulumukiramo ayenera kuchita chiyani?
20 Kuti atetezereke kwa wolipsa mwazi, anthu opha anzawo mwangozi anafunikira kukhala m’mudzi wopulumukiramo ndi kusadutsa malire a mabusa ake. Bwanji nanga za awo amene ali m’mudzi wophiphiritsira wopulumukiramo? Kuti apulumuke kwa Wolipsa mwazi wamkulu, iwo ayenera kusatuluka m’mudziwo. Inde, afunikira kupeŵa zinthu zokopa zimene zingawapititse kumalire a mabusa, titero kunena kwake. Ayenera kusamala kuti sakulola chikondi cha dziko la Satana kukhala mumtima mwawo. Zimenezi zingafune pemphero ndi khama, koma mpamene miyoyo yawo imadalira.—1 Yohane 2:15-17; 5:19.
-
-
Milungu Yachikazi ya Kubala ndi ya NkhondoNsanja ya Olonda—1995 | November 15
-
-
Milungu Yachikazi ya Kubala ndi ya Nkhondo
PANTCHITO ya kufukula za m’mabwinja ku Ebla, Syria, chifanizo chosonyeza Ishtar, mulungu wachikazi wa Chibabulo wa kubala ndi wa nkhondo, chinapezedwa. Katswiri wa za m’mabwinja Paolo Matthiae akuchifotokoza kukhala “chizindikiro chachitali chokhala ndi chithunzithunzi cha kulambira chosonyeza wansembe wachikazi wophimba kumaso ataimirira patsogolo pa fano limodzi la mulungu . . . ndi mutu wake womamatira ku mzati wautali.”
Chopezekacho nchapadera, popeza fanolo nlakuchiyambi kwa zaka za zana la 18 B.C.E. Malinga ndi Matthiae, chimenechi chimapereka “umboni wotsimikiza” wakuti kulambira Ishtar kunakhalapo kwa zaka 2,000.
Kulambira Ishtar kunayamba mu Babulo ndipo m’zaka mazana zotsatirapo kunafala mu Ufumu wonse wa Roma. Yehova analamula Aisrayeli kuchotsa kanthu kalikonse ka chipembedzo chonyenga m’Dziko Lolonjezedwa, koma popeza analephera kuchita motero, kulambira kwa Astaroti (mulungu wa Chikanani mnzake wa Ishtar) kunakhala msampha kwa iwo.—Deuteronomo 7:2, 5; Oweruza 10:6.
Ngakhale kuti Ishtar ndi mnzake Astaroti saliponso, makhalidwe amene anaimira—chisembwere ndi chiwawa—nzofala. Tingafunse kaya chitaganya chamakono chiridi chosiyana kwambiri ndi anthu akale amenewo amene analambira milungu yachikazi imeneyi ya kubala ndi ya nkhondo.
-