Nyimbo 56
Pitirizanibe Molimba Mtima
1. Yemwe ali wokhulupirika,
Sadzakhala ndi mantha,
Achita umboni molimba mtima,
Kuti Ufumu wadza.
(Korasi)
2. Chikhulupiro chisonkhezera;
Chikondi chithandiza.
Changu kwa Mfumu chitikangalitsa;
Ndipo dyera lichoke.
(Korasi)
3. Yehova ndiwamphamvu munkhondo,
Amatilimbikitsa
Mpaka Armagedo iwonongadi
Dongosolo lakale.
(KORASi)
Tiyenitu. Molimbika.
Cho’nadi chitsogoze.
Ati Yehova: “Ndidzakulimbitsa;
Menyera chowonadi.”