Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Rahabi—Anayesedwa Wolungama ndi Ntchito za Chikhulupiriro
    Nsanja ya Olonda—1993 | December 15
    • Israyeli akawononge Akanani chifukwa cha machitachita awo oipa, ndi dalitso lake pa Rahabi ndi pachilakiko cha Yeriko, zimapereka umboni wakuti azondiwo sanachite chisembwere.​—Levitiko 18:24-30.

      Bwanji za mawu osokeretsa a Rahabi kwa olondola azondiwo? Mulungu anavomereza njira yakeyo. (Yerekezerani ndi Aroma 14:4.) Iye anadziika pangozi kotero kuti atetezere atumiki a Mulungu, akumasonyeza umboni wa chikhulupiriro chake. Pamene kuli kwakuti kunama kovulaza nkoipa m’maso mwa Yehova, munthu sali woumirizika kuvumbula chidziŵitso chowona kwa anthu ena amene ali osachiyenerera. Ngakhale Yesu Kristu sananene zonse kapena kuyankha mwachindunji pamene kuchita motero kukanadzetsa ngozi yosafunikira. (Mateyu 7:6; 15:1-6; 21:23-27; Yohane 7:3-10) Mwachionekere, njira ya Rahabi yosocheretsa adindo amene anali adani iyenera kulingaliridwa motero.

      Mfupo ya Rahabi

      Kodi Rahabi anafupidwa motani chifukwa cha kusonyeza chikhulupiriro? Kupulumutsidwa kwake mkati mwa chiwonongeko cha Yeriko kunalidi dalitso lochokera kwa Yehova. Pambuyo pake, anakwatiwa ndi Salimoni (Salima), mwana wa kalonga wa m’chipululu Nasoni wa fuko la Yuda. Monga makolo a Boazi wowopa Mulungu, Salimoni ndi Rahab anagwirizanitsa mzera wa mbadwa umene unafikira kwa Mfumu Davide wa Israyeli. (1 Mbiri 2:3-15; Rute 4:20-22) Mwatanthauzo kwambiri, Rahabi amene anali wadama kaleyo ndimmodzi wa akazi anayi otchulidwa ndi Mateyu m’mzera wobadwira wa Yesu Kristu. (Mateyu 1:5, 6) Limeneli ndidalitso lotani nanga lochokera kwa Yehova!

      Ngakhale kuti sanali Mwisrayeli ndipo poyambapo wadama, Rahabi ali chitsanzo chapadera cha mkazi amene anasonyeza ndi ntchito zake kuti anakhulupirira Yehova kotheratu. (Ahebri 11:30, 31) Mofanana ndi ena, mwa amene ena a iwo aleka moyo wadama, iye adzalandira mfupo inanso​—kuukitsidwa kwa akufa ndi kukhala ndi moyo m’dziko lapansi laparadaiso. (Luka 23:43) Chifukwa cha chikhulupiriro chake chochirikizidwa ndi ntchito, Rahabi anavomerezedwa ndi Atate wathu wakumwamba wachikondi ndi wokhululukirayo. (Salmo 130:3, 4) Ndipo chitsanzo chake chabwino kwambiricho chimapereka chilimbikitso kwa onse okonda chilungamo kuti ayembekezere Yehova Mulungu kudzawapatsa moyo wosatha.

  • Kusunga Diso Lathu Lili “la Kumodzi” m’Ntchito Yaufumu
    Nsanja ya Olonda—1993 | December 15
    • Kusunga Diso Lathu Lili “la Kumodzi” m’Ntchito Yaufumu

      GERMAN Democratic Republic (G.D.R.), kapena dziko limene linadziŵika kukhala East Germany, linali litangofikitsa kumene zaka zake zapakati. Kukhalapo kwake kwazaka 41 kunatha pa October 3, 1990, pamene dera lake, pafupifupi la ukulu wofanana ndi Liberia kapena chigawo cha Tennessee mu United States, linagwirizanitsidwa ndi Federal Republic of Germany, amene anali kutchedwa West Germany.

      Kugwirizanitsidwa kwa mbali ziŵirizo za Germany kwatanthauza masinthidwe ochuluka. Chimene chinalekanitsa maiko aŵiriwo chinali, osati malire okha, komanso kusiyana kwa malingaliro. Kodi zonsezi zinatanthauzanji kwa anthu a kumeneko, ndipo ndimotani mmene moyo wasinthira kwa Mboni za Yehova?

      Wende, kusintha kwa zinthu m’November 1989 kumene kunapangitsa

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena