Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • “Kusakaza Kochitidwa Kudzakhala Kwakukulu Kwambiri”
    Nsanja ya Olonda—1987
    • “Kusakaza Kochitidwa Kudzakhala Kwakukulu Kwambiri”

      NKHONDO YADZIKO 1 inatenga mbali yaikulu ya miyoyo ya anthu ndi katundu. Kodziwika bwino pang’ono, ngakhale kuli tero, kuli kusakaza kumene nkhondo inachita ku chithunzi cha amishonale a Dziko la Chipembedzo mu Africa. Malinga ndi mishonale wa Chikatolika Francis Schimlek mu bukhu lake Medicine Versus Witchcraft, mbiri ya kusakaza kwa dziko lonse kumeneku “kunali monga chivomezi, kunjenjemera kwake kumene kunamveka kufikira ku mishoni yomalizira ya mu Africa ku nkhalango. . . . Athenga a Kristu anachititsidwa manyazi, ndipo Akristu Akuda anazizwitsidwa.”

      Nchifukwa ninji chiri tero? Schimlek akugwira mawu mishonale Albert Schweitzer pamene akulongosola: “Ife tiri, tonse a ife, ozindikira kuti Anthu Akuda ambiri akuzizwa kwambiri ponena za funso lakuti kodi chingakhale chotheka motani kuti azungu, amene anabweretsa Uthenga Wabwino wa Chikondi, tsopano akuphana wina ndi mnzake, ndi kumataya malamulo a Ambuye Yesu. Pamene iwo afunsa funsoli kwa ife timakhala opanda thandizo. . . . Ndikuwopa kuti kusakaza kochitidwa kudzakhala kwakukulu kwambiri

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—1987
    • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

      ◼ Mose anauza a Israyeli kuti “zinthu zovumbuluka nza ife ndi ana athu kosatha.” (Deutronomo 29:29) Kodi “zinthu zimenezo zovumbuluka“ zingaphatikizepo kuwala komwe kukuperekedwa pa Mawu a Mulungu mkati mwa masiku ano omaliza?

      Ayi, sichingakhale cholondola kunena kuti kumvetsetsa kwa maulosi komwe tapatsidwa mkati mwa masiku ano otsiriza kuli pa mlingo umodzimodzi ndi “zinthu zovumbuluka“ zomwe Mose anali kulongosola.

      Malinga ndi nkhani ya mawu a Mose, “zovumbuluka“ zomwe iye anali kulankhula ponena za izo zinayenera kuchita ndi pangano la Chilamulo. (Deutronomo 29:25) Mose anasonyeza kuti “zinthu zovumbuluka“ zimenezi zinali ndi mathayo. Kulephera kukhala ndi moyo kulinga ku mathayo amenewa kungapangitse Yehova kulanga anthu ake.

      Pangano la lamulo, ngakhale kuli tero, linali vumbulutso lochokera kwa Yehova Mulungu. Ilo linatsatizidwa ndi zivumbulutso zina kwa makolo, kwa Nowa, ndi kubwerera m’mbuyo kwa Adamu. Mose anagwiritsidwa ntchito kulemba zinthu zovumbuluka kufika ku nthawi yake, ndipo zinasungidwa kaamba ka ife mu mabukhu asanu oyambirira a Baibulo. Pambuyo pake, monga mmene nkhani ya “Zinthu Zovumbulutsidwa Nzathu” (Nsanja ya Olonda, November 1, 1986) inalongosolera, “zinthu zovumbulutsidwa“ zimenezi zinabwera kuphatikizapo chidziwitso cholembedwa mu Baibulo.​—2 Timoteo 3:16.

      Chotero, Baibulo liri ndi [“zonenedwa zopatulika NW] za Mulungu zinthu zovumbulutsidwa ndi iye. (Aroma 3:2) Pamene Ayuda achibadwa anatsimikizira kukhala osakhulupirika, Akristu odzozedwa anakhala athenga a “zinthu zovumbulutsidwa“ zimenezi, ndipo mpingo Wachikristu unakhala “mzati ndi mchirikizo” wa iwo. (1 Timoteo 3:15; 1 Akorinto 4:1) Chotero, ziwalo za mpingo umenewo lerolino moyenerera zingafuule mawu a Mose, kuti “zinthu zovumbuluka nzathu.”

      Lerolino, Yehova waika kuwala kwambiri pa “zinthu zovumbuluka“ zimenezi. Monga kunanenedwera ndi Danieli, anthu a Yehova ‘afunafuna’ m’Mawu ouziridwa, ndipo ’chidziwitso chenicheni chakhala chochuluka.’(Danieli 12:4) Chotero, ife tsopano timadziwa chizindikiritso cha “nkhosa zina.” (Yohane 10:16) Timazindikiranso “khamu lalikulu.” (Chivumbulutso 7: 9-17) Timawona kukwaniritsidwa kwa fanizo la nkhosa ndi mbuzi. (Mateyu 25:31-46) Zinthu zoterozo zavumbulidwa, kapena kudziwikitsidwa, kwa ife osati mu lingaliro la “zinthu zovumbuluka“ monga zalembedwera m’Mawu ouziridwa a Yehova.

      Chotero, sichingakhale cholondola kuika kupita patsogolo kumeneku mwa kumvetsetsa pa mlingo wofanana ndi zivumbulutso zouziridwa zomwe zimapanga “zinthu zovumbuluka“ zolembedwa mu Baibulo. M’malo mwake, kupyolera mu kuphunzira kosamalitsa kwa Baibulo, anthu a Yehova mwapemphero afuna kumvetsetsa kulondola kwa “zinthu zovumbuluka“ zimenezo. Yehova, kupyolera mwa mzimu wake woyera, wapereka kumvetsetsa kumeneku mu nthawi yake.

      Baibulo limatiuza ife kuti “mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbanda kucha, kunkabe kuwala kufikira usana woti mbe.”(Miyambo 4:18) Kuwonjezeka kwa kuwala kumene Yehova akupereka pa “zinthu zovumbuluka“ kumasonyeza kuti “tsiku“ limenelo likuyandikira ndi kutsimikizira kuti dalitso lake liri pa mpingo Wachikristu lerolino.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena