Musaiŵale Cholinga cha Ufulu Umene Mulungu Wakupatsani!
1 Yehova ndi Mulungu waufulu. Ndipotu ndife odala zedi kutumikira Mulungu waufulu. Monga atumiki a Yehova, timakhala olemera mwauzimu chifukwa timatsogozedwa ndi mzimu wa Mulungu, kapena mphamvu yake yogwira ntchito. Mtumwi Paulo ananena kuti: “Ambuye ndiye Mzimuyo; ndipo pamene pali Mzimu wa Ambuye pali ufulu.” (2 Akor. 3:17) Ndithudi, tonsefe tinali muukapolo tisanapeze chidziŵitso cholondola cha Mawu a Mulungu, Baibulo. Chaka chilichonse anthu okonda choonadi miyandamiyanda amamasulidwa kuukapolo ndiponso kuziphunzitso zachipembedzo chonyenga ndi miyambo, ndipo amadzionera okha mawu a Yesu olembedwa pa Yohane 8:32 amene amati, “choonadi chidzakumasulani.” Popeza tsopano sindifenso akapolo a zikhulupiriro zachipembedzo chonyenga, koma monga atumiki a Yehova tili ndi mwayi woyenda m’njira yopapatiza imene imatsogolera kumoyo wosatha. (Mat. 7:13, 14) Tili aufulu popeza sitiopa mizimu ya anthu akufa chifukwa tsopano tikudziŵa choonadi cha zimene zimachitika kwa okondedwa athu akufa. Chifukwa cha chidziŵitso cholondola cha Mawu a Mulungu, timadziŵa kuti posachedwapa malonjezo onse abwino kwambiri onena za paradaiso amene Mulungu analonjeza adzakwaniritsidwa, pompano padziko lapansi. Kodi mudzapitiriza kugwiritsa ntchito mwanzeru ufulu wanu wopatsidwa ndi Mulungu? Ili ndi funso lofunika kwambiri limene tonsefe tiyenera kudzifunsa ndipo tiona chifukwa chake tiyenera kutero.
2 Chirimikani pa Ufulu Wanu Wopatsidwa ndi Mulungu: Baibulo limafotokoza mmene Satana Mdyerekezi akumvera pakalipano popeza tikukhala m’masiku otsiriza. Limatchula Satana monga, “wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kam’tsalira kanthaŵi.” (Chiv. 12:12) M’Baibulo iyenso amatchulidwa kukhala monga mkango wobuma, umene ukuyendayenda kufunafuna wina um’likwire. (1 Pet. 5:8) Kodi Yehova akutiuza chiyani pamenepa? Timaphunzira kuti Satana angachite chilichonse chimene angathe, ndiponso kugwiritsa ntchito aliyense amene akufuna, kuti tigulitse ufulu wathu n’cholinga chakuti tikhalenso akapolo a Satana. Ndithudi! Zimenezo n’zimene Satana akufuna kwa ife. Pa Agalatiya 5:1 mtumwi Paulo anakumbutsa Akristu odzozedwa kuti, “Kristu anatisandutsa mfulu, kuti tikhale mfulu; chifukwa chake chirimikani, musakodwenso ndi goli la ukapolo.” Tangolingalirani mawuwo akuti, kukodwanso monga akapolo m’njira zoipa za Satana! Pamene Baibulo ligwiritsa ntchito mawu akuti, “chirimikani”—limatanthauza kuti (1) tiyenera kukhala okhulupirika kwa Yehova mwa kupempha chitsogozo chake pamene tikufuna kusankha zinthu zoyenera kuchita tsiku lililonse, (2) komanso kupeŵa kuchita nawo miyambo iliyonse imene imachirikiza Satana ndi ziwanda.
3 Kodi ndi miyambo ina iti imene imachirikiza Satana ndi ziwanda zake? Ili ndi funso lofunika kwambiri chifukwa m’madera ambiri m’Malaŵi muno anthu amakhulupiriradi kuti miyambo ina imatetezeradi kuzinthu zovulaza ndi matenda. Ndipo chifukwa chakuti achibale athu ena si atumiki a Yehova, n’zotheka kuti ameneŵa angakulimbikitseni kwambiri kuchita nawo miyambo ndi “nkhani zachabe zimene zimaipitsa chimene chili choyera ndi zimene akazi okalamba amasimba.” (1 Tim. 4:7, NW) Tiyeni tione miyambo ina imene ‘imaipitsa chimene chili choyera’ yomwe ingatitayitse unansi wathu wabwino ndi Yehova ngakhale ngati titaichita mobisa. Choyamba, kodi Yehova amaliona motani khalidwe lopempha ziwanda kuteteza munthu kumatenda?
4 Kodi Baibulo Limanena Chiyani za Asing’anga: Baibulo limavumbula kuti zaka zambiri zam’mbuyomo kulambira mizimu ndi kuchita matsenga kunali kofala m’mayiko monga Igupto, Babulo ndi Kanani. (Eks. 7:10-12; Deut. 18:14; Yes. 47:1, 12, 13) Choncho, sizodabwitsa, kuti pamene Yehova Mulungu anamasula mtundu wa Israyeli ku ukapolo m’Igupto n’kuwaloŵetsa m’dziko la Kanani anapeza anthu akumeneko ali pakalikiliki m’zamizimu. Kodi Yehova Mulungu anapatsa atumiki ake lamulo loti chiyani? Anawauza mosabisa kuti anayenera kulambira iye yekha basi. (Eks. 20:3-6) Pachifukwa chimenecho Mulungu anachenjeza Aisrayeli kuti: “Musamatembenukira kwa obwebweta, kapena anyanga; musawafuna, ndi kudetsedwa nawo.”—Lev. 19:31.
5 Yehova Mulungu analangiza Aisrayeli kuti adzataya madalitso ake komanso miyoyo yawo ngati samvera lamulo lake loletsa kulambira mizimu koteroko. (Lev. 20:6, 27) Kenako, Mulungu anagogomezeranso kunyansidwa kwake ndi makhalidwe okhudza kulambira mizimu yosaoneka, monga nyanga ndi kupenduza. (Deut. 18:9-12) Kodi izi sizomveka bwino komanso kodi sizikusonyezeratu mmene Mulungu Wamphamvuyonse amaonera asing’anga ndi kulambira kwawo mizimu yosaoneka? Mogwirizana ndi Mawu ake ouziridwa, Yehova Mulungu amadana ndi machitidwe onse onga ameneŵa mosasamala kanthu kuti akuchitika m’njira yotani kapena kuti akuchitika m’dziko liti. Ndipo chifukwa cha chikondi chake, iye akutipatsa machenjezo ameneŵa kuti tisadzavutike ndi mavuto amene miyamboyi mosapeneka ingabweretse.
6 Pamatenda: Pamatenda, anthu ena ayesa madokotala ndi zipatala zingapo koma osachira. Izi zingakhale choncho mwina chifukwa chakuti chipatala chili kutali n’kumene amakhala kapena chifukwa chakuti chipatala chilibe mankhwala ena alionse. Zikatero, ena angaone kuti ndi bwino kupita ku mankhwala achikuda, kutanthauza kuti kwa munthu amene amadziŵa mankhwala azitsamba. Ambiri a madokotala ameneŵa amagwiritsa ntchito zitsamba ndi zinthu zina zachilengedwe, zimene paizozokha sizovulaza. Koma vuto lagona pakuti asing’anga kapena madokotala achikuda ameneŵa angaloŵetsemo kukhulupirira mizimu m’kugwiritsa ntchito kwawo zitsamba ndi mankhwala ena. M’Baibulo, mawu akuti “kukhulupirira mizimu” monga mmene alili mu New World Translation pa Chivumbulutso 21:8 achokera ku liwu lachigiriki lakuti phar·ma·kiˈa, limene kwenikweni limatanthauza “mankhwala.” Izi zili chifukwa chakuti m’nthaŵi zakale anthu ambiri okhulupirira mizimu ankagwiritsa ntchito mankhwala m’miyambo imene ankachita.
7 Ochiritsa angakhulupirire mizimu m’kuchiritsa kwawo mwa kupereka nsembe (nkhuku kapena chiŵeto chimene munthu wodwalayo wapereka), mwinanso mwa kugwiritsa ntchito matsenga, kapena malodza. M’dziko lina la kumadzulo kwa Afirika, munthu wina anauzidwa kukatenga mankhwala a dzino azitsamba kwa mkazi wina wa fuko lake. Pom’patsa mankhwalawo, mkaziyo anamuuza mwamunayo kuti asayang’ane mankhwalawo. Mwamunayo atafunsa chifukwa chake ananena choncho, mkazi uja anayankha kuti mankhwalawo ‘atha mphamvu’ akawayang’ana. Koma kodi mtera kapena mankhwala ena alionse angadziŵe bwanji kuti ‘akuyang’anidwa’? Kodi zinthu zimenezi zili ndi maso? Ndithudi zilibe. Choncho n’zodziŵikiratu kuti wochiritsayo ankakhulupirira kuti magulu amizimu akagwira ntchito pa mankhwalawo, ndipo akuwapatsa mphamvu yamatsenga.
8 Madokotala ena achikuda anganene kuti amalemekeza malamulo a Mulungu oletsa kukhulupirira mizimu, koma pamene zenizeni n’zakuti amachita matsenga m’zochita zawo. Angagwiritse ntchito thope kapena zitsamba pochiritsa. Koma, pochotsa thopelo, amaikako kanthu kena, mwina mwala kapena nsanza, ndiyeno amati chimenecho ndiye chinayambitsa matendawo ndipo achichotsa m’thupi.
9 Taŵerenga kale mmene Mulungu Wamphamvuyonse amawaonera anthu amene amachita matsenga ndi nyanga kuti ‘amam’nyansa.’ (Deut. 18:10-12) Nthaŵi zambiri madokotala achikuda amagwiritsa ntchito miyambo ndi kupereka nsembe kupempha ‘milungu’ kapena mizimu. Ndiyeno, ngati madokotala achikuda ena akuuzani kuti mubweretse nkhuku kapena mbuzi ya nsembe, kodi ndiye kuti zikutanthauzanji? Kodi nyamayo ikaperekedwa nsembe kwa ndani kwenikweni?—1 Akor. 10:20-22.
10 Madokotala achikuda ena amapereka zingwe zoteteza zimene agogo amamangirira ana m’chiuno, pamkono, pakhosi kapena m’miyendo. Zingwe zimenezi amakhulupirira kuti zili ndi mphamvu yapadera. Mwachitsanzo, chingwe chimene amatungirimo mikanda chomangidwa m’chiuno mwa mwana wamkazi amati chidzam’chititsa kukhala wopatsa chikoka cha kugonana akadzakula kukhala mayi. Kapena chingwe chimene madokotala achikuda amapereka, chimene amachimanga m’chiuno mwa mwana wamwamuna kapena wamkazi amati chimateteza mwanayo kuti asadwale chifukwa cha chigololo chimene mmodzi wa makolo ake anachita. Chingwe chomangidwa m’khosi amati chimateteza kuti matenda asaloŵe paliwombo la mwana. Baibulo limatiuzanso mmene zimam’nyansira Yehova kugwiritsa ntchito zingwe zimenezi.—Deut. 7:25, 26.
11 Kodi tingati Yehova angaone kuvala chingwe monga chinthu chosavulaza ngati amadana ndi anthu okhulupirira mizimu amene amapanga zingwe zimenezi? Ndithudi ayi! Komanso, Mawu a Mulungu amatiuza momveka bwino mmene Yehova amadanirana ndi zingwe “zoteteza.” Ponena za chinthu chilichonse chokhudza kulambira konyenga kapena china chilichonse chochokera kwa anthu okhulupirira mizimu, Mulungu analamula kuti: ‘Pasamamatire padzanja panu kanthu ka chinthu choti chiwonongeke; kuti Yehova aleke mkwiyo wake waukali.’ (Deut. 13:12-17) Kuvala zingwe zoteteza kudzangokuitanirani ziwanda kuti zikuvulazeni, ndiponso mukudziitanira mkwiyo wa Yehova.
12 Nanga bwanji ngati tayesa njira zonse zoyenera kuti tichire koma sizikuthandiza? Baibulo limatiuza kuti: “Um’senze Yehova nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza: Nthaŵi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.” (Sal. 55:22) Pempherani kwa iye, osati kuti akuchiritseni mozizwitsa, koma kuti mukhale ndi nzeru kuti musankhe mankhwala abwino ndi oyenera, chofunika koposa, kuti mukhalebe wathanzi ndi wolimba mwauzimu, komanso kuti mupitirizebe kulimbitsa chikhulupiriro ndi kukhalabe wachimwemwe, mulimonse mmene nyengo ya matenda anu kapena ukulu wa matenda anu ungakhalire. Mungaikizenso ana anu kwa Yehova. Iye ndi amene anawapatsa moyo. Iyenso angawasunge, koma osati mwa njira ya zinthu ngati mankhwala otsirika kapena zingwe, nsembe, ndi miyambo ina.
13 Timadziŵa kuti mwa anthu amene amakhulupirira mizimu, pali ochiritsa ndi asing’anga omwe nawonso amadwala ndi kufa pazifukwa zosiyanasiyana. Ngakhale atumiki oona a Mulungu ndi ana awo amene sakhulupirira mizimu, kaŵirikaŵiri amadwala. Ngakhale adwale matenda opanda mankhwala, ali ndi chiyembekezo chabwino kwambiri chimene chingawachirikize. Amadziŵa kuti Yehova Mulungu ali ndi nthaŵi yake imene adzachotsa matenda onse ndi imfa. Chotero onse amene ali okhulupirika kwa Mulungu adzalandira makonzedwe opatsa moyo, ochitiridwa chithunzi ndi “mtsinje wa madzi a moyo” umene m’mphepete mwake muli mitengo yomwe masamba ake ‘akuchiritsa nayo amitundu.’ (Chiv. 22:1, 2) Chotero, ngakhale titafa, tingadalire mawu a Yesu akuti: “Iye amene afuna kupulumutsa moyo wake adzautaya: koma iye amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine, adzaupeza.” (Mat. 16:25) M’malo moyesa kusunga miyoyo yathu mwakuchita machitidwe odetsa a kukhulupirira mizimu, tingadalire mphamvu ya Mulungu Wamphamvuyonse ndi kukhulupirira kuti adzatiukitsa kwa akufa mwakutiukitsira kumoyo m’dongosolo lake latsopano lathanzi.
14 Pamene Wina Wamwalira: M’madera ena mu Afirika kuphatikizapo m’Malaŵi muno, munthu akamwalira n’chizoloŵezi kulondera maliro. Achibale ndi mabwenzi amasonkhana panyumba imene kwachitika malirowo kapena kubanja lofedwalo. Kumakhala kulira, kuimba nyimbo, ndi kuimba ng’oma, kusonkha moto panyumba ya munthu wakufayo, kumwa ndi kuchita zinthu zina malinga ndi miyambo yakumaloko. Nthaŵi zina wakufayo, amam’sambitsa ndi kum’mveka zovala zabwino zomwe ankazikonda kwambiri ndi kum’goneka pamalo amene mabwenzi ndi achibale amandondozana kukaona nkhope komaliza wakufayo asanakamuike m’manda. Komabe, nthaŵi zambiri, ndi bwino kukaika maliro mwamsanga. Ngakhale kuti malirowo adzaikidwa tsiku lotsatira, palibe chifukwa chokonzera dongosolo lolondera malirowo. Mwakamodzikamodzi, anthu aŵiri kapena atatu atha kulondera mtembowo usiku kuopera nyama zamthengo kapena zoopsa ngati zimenezi, koma izi ziyenera kusiyana ndi zimene anthu amati kulondera maliro. Nthaŵi zambiri kulondera maliro kumachitika chifukwa chokhulupirira kuti mfiti n’zimene zimachititsa imfayo, ndipo kuti amene wachita zimenezo atha kubwera pa mtembowo usiku. Palibiretu chifukwa chimene gulu lalikulukulu la anthu liyenera kuchezera pamaliro, kumaimba, kuchema ndiponso kumamwa.
15 Kuti zimenezi zisachitike, ngati n’kotheka n’kwabwino zedi kuchita mwambo wamaliro mwamsanga, achibale osakhulupirira amene angafune kuti titsate njira zachikunja asanafike. Mwachitsanzo, ngati munthu wamwalirira kuchipatala, n’kwabwino kungochokera kumeneko kupita naye kumanda, osayamba mwapita naye kunyumba. Yesu anaikidwa m’manda mwa njira imeneyi—kungochoka pamtengo wozunzirapo kukaikidwa m’manda.
16 Mnzathu kapena wachibale akamwalira n’kwachibadwa kumva chisoni. Yesu anamva chisoni ngakhale kulira kumene pamene bwenzi lake Lazaro anamwalira. (Yoh. 11:33, 35) Komabe, kulira kwenikweni koti munthu alidi n’chisoni kumasiyana ndi kulira komanso kuchema kumene kumachitika pamaliro ambiri m’madera ena. N’kwachibadwa kulira, ngakhale kufika pobuma pamene wokondedwa wamwalira. (2 Sam. 1:11, 12) Komabe, kulira ndi kubuma koopa kukwiyitsa mizimu yosaoneka, kapena chifukwa choopa achibale ena, n’kosemphana ndi Mawu a Mulungu. Nthaŵi zambiri mawu amene amanena akamachema ndi kuimba amapereka pemphero kapena pembedzero kwa munthu wakufayo kapena makolo ena akale. Ndithudi, ena amalondera maliro chifukwa choopa kwambiri akufa. Choncho pamene kuli kwakuti sikulakwa munthu woopa Yehova kupita kumaliro, ndibwino kukumbukira uphungu wakuti “patukani, . . . ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka.” (2 Akor. 6:17) Tingapeze njira zosonyezera chisoni chathu ndi kupereka chitonthozo chenicheni popanda kuchita nawo mbali iliyonse yokhudza kulambira mizimu. Komanso, anthu a Yehova sayenera kugonjetsedwa ndi chisoni, popeza ali ndi chiyembekezo cha chiukiriro.—1 Ates. 4:13.
17 N’zoona kuti miyambo yokhudza akufa, maliro ndiponso zomwe achibale amaletsedwa zimasiyana kwambiri malinga ndi zikhulupiriro ndi miyambo yakumaloko. Koma nthaŵi zambiri, amakhulupirira kuti anthu akufa amaona amoyo, ndipo amachita miyambo yambiri yosemphana ndi Mawu a Mulungu. Mtumiki woona wa Mulungu sangafune kudetsedwa ndi zinthu zimenezi. M’madera ena mu Afirika, pakatha chaka munthu atamwalira, amachita mwambo mwapadera n’cholinga ‘chobwezera kachiŵiri munthu wakufayo kunyumba.’ Amakhulupirira kuti paimfa mzimu supita nthaŵi yomweyo ku ‘dziko la mizimu’ koma kuti umakhala usakugwira ntchito mpaka nthaŵi imene mwambo wamaliro utachitika kachiŵiri m’pamene umaloŵa ku ‘dziko la mizimu.’ M’madera ena, nthaŵi zambiri pamaphedwa nyama ndipo pamakhala zakumwa pamaliropo kuperekera nsembe kwa makolo amene anamwalira kalekale.
18 Komabe, chofunika kwambiri n’chimene Mawu a Mulungu amanena za machitidwe ameneŵa. Mwachitsanzo, Salmo 106:28, 29, limanena za Aisrayeli osakhulupirika amene anayamba kulambira konyenga komanso ‘kudya nsembe za akufa.’ Limasonyeza kuti “anam’kwiyitsa” Mulungu mwa zochita zimenezi ndipo sanawayanjenso. Taphunzira kale m’Baibulo kuti pamene munthu wafa, Mulungu yekha ndiye angapangitse munthuyo kukhalanso ndi moyo m’njira ya chiukiriro.
19 Khalani tcheru! “Mdani wanu mdyerekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire.” (1 Pet. 5:8) N’kwapafupi kugonja ndi mavuto n’kuvala mankhwala aang’ono monga njirisi. Koma amene akufuna kuyanjidwa ndi Mulungu adzakumbukira kuti Yehova ali “Mulungu wansanje.” (Eks. 20:4-6) Safuna kulambira konyenga kozikidwa pa kunama komanso sadzadalitsa mtumiki wake aliyense ngati ali ‘ofunda’ ndi malamulo ake.—Chiv. 3:16.
20 Kusamalira Manda: M’madera ena m’dziko muno, miyambo yosamala manda ili yofala. Kodi Akristu amaona motani nkhani yosamalira manda? Pangakhale zifukwa zambiri zimene anthu amasamalirira manda. Mwachitsanzo, (1) chingakhale chifukwa choopa moto kuloŵa m’mandamo. Komanso, (2) chingakhale chifukwa chakuti manda amaonedwa monga mudzi wa anthu akufa. Ngati sasamalidwa bwino, akufa angavulaze anthu amene sakusamala mudzi wawowo. Kwa anthu ena, imakhala njira yosangalatsira makolo awo akufa. Makolo akale ankasamala za mmene manda akuonekera. (Gen. 35:20) Manda osasamalidwa angatibweretsere chitonzo monga alambiri a Yehova. Komanso, ndi nkhani yaumwini kusankha kupita kumanda ndi kukakumbukira za munthu amene anaikidwa kumeneko. Koma Mkristu safunika kuchita kuika tsiku la zimenezo. Zinthu zimenezo zingachitike tsiku lina lililonse. Monga mmene ˈsitifunikira Khirisimasi kuti tipereke mphatso, sitifunikanso kuika masiku okaonera manda. M’njira iliyonse sitifuna kufanana ndi Babulo Wamkulu kapena anthu ena amene amalankhula ndi akufa, kuwapatsira zakudya kapena kupereka zakudya monga nsembe polemekeza akufa. Anthu ochita zimenezi ndi amene Yesu anawatchula kuti “akufa” mwauzimu, popeza amasamalira kwambiri nkhani zokhudza kuika maliro, manda, ndi makolo amene anamwalira kalekale. Choncho kwa ife mawu awa adakali oona: “Leka akufa aike akufa a eni okha; koma muka iwe nubukitse mbiri yake ya Ufumu wa Mulungu.”—Luka 9:60.
21 Chotero, n’zodalira chikumbumtima cha Mkristu aliyense ngati angasamalire nawo manda ngati zimenezo sizikuloŵetsamo zinthu zosemphana ndi mfundo zachikhalidwe za Baibulo. Baibulo limadana ndi njira iliyonse yokhulupirira mizimu ndiponso makhalidwe olambira mizimu. Ilo limavumbulanso kuti akufa sadziŵa kanthu kalikonse. Chotero, chochitika chilichonse chofuna kusangalatsa anthu akufa chili chotsutsana ndi chifuno cha Mulungu kwa ife. (Deut. 18:9-12; Mlal. 9:4-6, 12) Pakhoza kukhala nkhani ndi mikhalidwe yambiri. Chofunika ndicho kudzifunsa tokha mmene Yehova amaonera nkhaniyo. Ngati tim’pempha nzeru m’pemphero, adzatithandiza kuzindikira njira yabwino ndi yanzeru. (Yak. 1:5) Amuna akulu mumpingo adzasangalala kukusonyezani mfundo zachikhalidwe za Baibulo pankhaniyi zotithandiza kusankha zochita mwanzeru. Khalidwe lathu labwino pankhani zimenezi n’lofunika.
22 Yamikirani Ufulu Wanu Wopatsidwa ndi Mulungu: Kutsatira mwaukapolo miyambo yopanda pake ya anthu, yochokera pa “maphunziro [oipa] a ziwanda” (1 Tim. 4:1) sikudzetsa chimwemwe. Chotsatira chake chingakhale kukondedwa kwanthaŵi yochepa ndi anthu amene amachita “ntchito zakufa.” (Aheb. 6:1) Komabe, tsogolo la otsatira onse a Satana ndi ziwanda zake n’lodziŵikiratu—imfa yosatha. (Mat. 25:46) Kodi simukufuna kupitiriza ufulu umene munapatsidwa pa kudzipatulira kwanu ndi ubatizo? Ndithudi—yamikirani ufulu wanu wopatsidwa ndi Mulungu ndipo kondwerani mwa Mulungu wachipulumutso chanu. Pemphero lathu likhaletu longa la Davide amene anapemphera kuti, “Munditsogolere m’choonadi chanu, ndipo mundiphunzitse; pakuti Inu ndinu Mulungu wa chipulumutso changa.”—Sal. 25:5.
[Bokosi patsamba 6]
Mwachidule—Makhalidwe Enieni Amene Mulungu Amam’nyansa
◼ Kuvala njirisi
◼ Kum’meta mwana mpala n’cholinga chom’teteza kumatenda
◼ Kukalondera maliro ndi cholinga chokachezera usiku wonse kunyumba yamaliro
◼ Kumwa mankhwala apadera pamaliro amene amati amaletsa mzimu wa munthu wakufayo kudwalitsa a m’banja lake
◼ Kumeta tsitsi pakatha masiku atatu wachibale atamwalira
◼ Kulira kapena kubuma pamaliro chifukwa choopa kukhumudwitsa mizimu yosaoneka
◼ Kukatenga mankhwala azitsamba kwa munthu wodziŵika kuti amachita zamizimu
◼ Kusamalira manda kokhudza zamizimu.