Nyimbo 45
Pemphero la Chiyamiko
1. Yehova wachisomo m’tamidwe,
Kwa inu Mfumu tikweza mawu,
Tifika kwa inu Womva pempho,
Kuti inu mutisamalire.
Zolakwa zivumbula kufo’ka;
Mutikhululukire machimo.
Ndi mwazi wa Kristu tinagudwa.
Tikhumba kuphunzitsidwa nanu.
2. Achimwemwe ndioitanidwa
Mubwalo lanu lolangizira.
Mawu anu nchitsogozo chathu.
Tidzakondwa ndi ubwino wanu.
Mphamvu yanu njowopsa kwambiri,
Idzathetsa mavuto adziko.
Titama Ufumu wanu M’lungu.
Tiulalike sudzalephera.
3. Mupereketu chisangalalo;
Dziko lonse lilambire inu.
Ufumu wanu uli wabwino,
Udzachotsa imfa ndi zovuta.
Kristu adzachotsadi zoipa.
Chilengedwe chidzasangalala.
Tiimbetu momuyamikira:
“Tamani Yehova, Mfumu yathu!”