Nyimbo 66
Mphamvu ya Kukoma Mtima
1. Tiyamikira Mulungu
Ka’mba ka chifundo
Kwa anthu osayenera,
Monga tikudziŵa.
Nkana ngwamphamvu wamkulu,
Alingalira koposa.
Chifundo chimatikoka
Ku chikhulupiro.
2. Yesu pophunzitsa mawu
Anali wofatsa,
Mwachifundo naphunzitsa,
Odzichepetsawo.
Chiphunzitso mwachikondi,
Chinatsitsimula moyo,
Kuti ochimwa alape
Namke kwa Mulungu.
3. Tibale zipatso izi
Atero Mulungu,
Kuti tifanane nawo
Mulungu ndi Kristu.
Pokumana ndi mavuto,
Mosakayika tipeza
Kuti mankhwala’ke ali
M’kukhala wofatsa.
4. Tidzachitatu bwinodi
Ngati tadziŵatu
Kuti chifundo nchamphamvu
Ndipo chosathadi!
Onse amadalitsidwa
Olandira ndi opatsa.
Mwachifundo titamanda,
M’lungu wotisunga.