“Sitingathe Ife Kuleka Kulankhula”
1 Yesu Kristu akuyang’anira mosamalitsa ntchito yolalikira. (Mat. 28:20; Marko 13:10) Ngakhale kuti pali anthu olengeza mwachangu pafupifupi 6,000,000 amene akuchitira umboni m’mayiko 234, sitiyenera kuganiza kuti tamaliza kuchitira umboni. Mpaka Mulungu adzanene kuti ntchito yatha, “sitingathe ife kuleka kulankhula” za zinthu zimene taphunzira.—Mac. 4:20.
2 Dalirani Mzimu wa Mulungu: Satana amagwiritsa ntchito ziyeso zazikulu n’cholinga choti atifooketse. (Chiv. 12:17) Matupi athu opanda ungwiro enieniŵa amatibweretseranso mavuto ambiri. Zinthu ngati zimenezi zingachotse malingaliro athu pantchito yofunika kwambiri ya kulalikira. Komabe, ngati timakhulupirira Yehova, mzimu wake udzatithandiza kugonjetsa zododometsa zina zilizonse.
3 Mpingo wachikristu wa m’zaka za zana loyamba utazunzidwa koopsa, abale anapempha Mulungu kuti awathandize kupitiriza kulankhula mawu ake molimba mtima. Yehova anayankha pemphero lawo. Anawasonkhezera ndi mzimu wake ndipo anawapatsa changu ndi mphamvu zofunikira kuti apitirize kulalikira. Chotsatira chake n’chakuti, sanaleka kulalikira molimba mtima uthenga wabwino.—Mac. 4:29, 31; 5:42.
4 Musachite Mantha ndi Nkhani Zokhumudwitsa: Malingaliro ofala kapena nkhani zabodza zofalitsidwa zingatichititse mantha. Komabe, kumbukirani mawu olimba mtima amene Petro ndi atumwi ena ananena kwa Sanihedirini, opezeka pa Machitidwe 5:29-32. Gamaliyeli, monga mphunzitsi wa Chilamulo anavomereza kuti, ntchito ya Mulungu singaimitsidwe. Siichitika mwa mphamvu yathu. Mulungu ndi amene amachirikiza ntchito yaikulu imeneyi, ndipo iye yekha ndiye angaikwaniritse!—Zek. 4:6.
5 Tiyeni tsiku lililonse tipemphe Yehova kuti atipatse mzimu wake kuti utithandize kulengeza mwachangu uthenga wabwino. Tinenetu, monga ananenera Yeremiya, kuti uthenga wa Ufumu uli ngati moto wotentha m’mafupa athu. (Yer. 20:9) Sitingakhale chete!