Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 6/1 tsamba 20-25
  • Pitirizani Kuchenjeza za Ntchito Yachilendo ya Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pitirizani Kuchenjeza za Ntchito Yachilendo ya Yehova
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Kama Wafupika”
  • Chochita Chodabwitsa cha Yehova
  • Chenjezo la Kachitidwe ka Yehova
  • ‘Tulukani Mmenemo’
  • “Mzimu wa Yehova Udzambalira Iye”
  • Pobisalira Pawo—Bodza!
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kodi Yerusalemu Ankaimira Matchalitchi Amene Amati ndi a Chikhristu?
    Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
  • Zidakwa Zauzimu—Kodi Ndizo Yani?
    Nsanja ya Olonda—1991
Nsanja ya Olonda—1991
w91 6/1 tsamba 20-25

Pitirizani Kuchenjeza za Ntchito Yachilendo ya Yehova

‘Yehova adzauka monga m’phiri la Perazimu, nadzakwiya monga m’chigwa cha Gibeoni.’​—YESAYA 28:21.

1, 2. Kodi ndintchito yachilendo yotani imene Yehova anaichita chifukwa cha anthu Ake m’tsiku la Davide?

CHOCHITIKA chodabwitsadi! Ntchito yachilendo koposa! Ichi nchimene Yehova anachita chifukwa cha anthu ake m’nthaŵi zakale m’zaka za zana la 11 B.C.E. Ndipo chochita chodabwitsachi chinali chitsanzo cha ntchito yachilendo koposapo imene iye watsala pang’ono kuichita posachedwa mtsogolomu. Kodi chochitika chamakedzanacho chinali chotani? Mwamsanga pambuyo pakuikidwa kwa Davide monga mfumu m’Yerusalemu, Afilisti apafupipo anaukira, ndipo chimenechi chinautsa chochitika chodabwitsa cha Yehova. Choyamba, Afilisti anayamba kufunka m’chigwa cha Refaimu. Davide anafunsa Yehova chomwe akachita ndipo analangizidwa kukamenyana nawo. Pokhala kuti anamvera mawu a Yehova, Davide anagonjetsa kotheratu gulu lamphamvu la Afilisti pa Baalaperazimu. Koma Afilistiwo sanakuvomereze kugonjetsedwako. Mofulumira anabwereranso kukasakaza ndi kufunkhanso m’chigwa cha Refaimu, ndipo Davide anapemphanso chitsogozo kwa Yehova.

2 Panthaŵiyi iye anauzidwa kunka ndi asirikali ake kumbuyo kwa Afilisti. Yehova anati: ‘Pakumva iwe kuwayula ku nsonga za mkandankhuku, pomwepo fulumiratu, pakuti pamenepo Yehova watuluka pamaso pako kukakantha khamu la Afilisti.’ Ndipo chimenecho nchomwe chinachitika. Davide anayembekezera kufikira Yehova atamveketsa kuwayula ku nsonga za mkandankhuku​—mwinamwake mogwiritsira ntchito mphepo yamphamvu. Mofulumira, Davide ndi makamu ake ankhondo anasokoloka mobisalamo ndi kuukira ndi kusakaza Afilisti osokonezekawo, akumawagonjetsa mwa kuwapha kwakukulu. Mafano achipembedzo amene Afilisti anawasiya ali ponseponse pabwalo lomenyanira nkhondolo anasonkhanitsidwa ndi kuwonongedwa.​—2 Samueli 5:17-25; 1 Mbiri 14:8-17.

3. Kodi nchifukwa ninji chochita chodabwitsa cha Yehova chinali chofunika chisamaliro kwa Ayuda a m’tsiku la Yesaya, ndipo nchifukwa ninji chiyenera kukhala chofunika chisamaliro kwa Chikristu Chadziko lerolino?

3 Iyi inali ntchito yachilendo, chochita chodabwitsadi, chochitidwa ndi Yehova motsutsana ndi Afilisti ndi chifukwa cha mfumu yake yodzozedwa. Chochita chapadera chimenechi nchofunika chisamaliro kwenikweni chifukwa chakuti mneneri Yesaya anachenjeza kuti Yehova akachita chinthu chodabwitsa ndi champhamvu motsutsana ndi zidakwa zauzimu za Yuda. Chifukwa chake, atsogoleri achipembedzo osakhulupirika a m’tsiku la Yesaya anafunikira kuzindikira. Chikristu Chadziko lerolino chiyeneranso kuzindikira chifukwa chakuti chimene chinachitika kwa Yuda chinali chitsanzo cha tsoka la Chikristu Chadziko lobwera mtsogolomu.

“Kama Wafupika”

4, 5. (a) Kodi ndimotani mmene Yesaya anafotokozera mopereka chithunzi mkhalidwe wopanda chitonthozo wa atsogoleri achipembedzo a m’tsiku lake? (b) Kodi nchiyani chimene chachititsa mkhalidwe wopanda chitonthozo wa Chikristu Chadziko lerolino?

4 Choyamba, Yesaya anavumbula chenicheni chakuti mapangano a ndale zadziko amene zidakwa zauzimu zakalezo zinadaliramo anali chinyengo, bodza. Kenaka iye anafotokoza mopereka chithunzi mkhalidwe wopanda chitonthozo wa awo oyembekezera m’bodza limenelo. Iye anati: ‘Kama wafupika, munthu sangatambalale pamenepo; ndi chofunda chachepa, sichingamfikire.’ (Yesaya 28:20) Munthu akatambalala pa kama wamfupi miyendo yake imapitirira kukhala pamphepo. Kumbali ina, ngati iye apinda maondo ake kuti alingane ndi kama wamfupiyo, chofunda chimakhala chaching’ono kwambiri ndipo mbali yaikulu ya thupi lake imakhalabe panja pamphepo. Mosasamala kanthu za zimene angachite, mbali ina ya thupi lake ikhalabe pamphepo.

5 Kunena mophiphiritsira, uwu ndiwo unali mkhalidwe wa anthu a m’tsiku la Yesaya omwe anaika chikhulupiriro chawo pobisalira pabodza. Ulinso mkhalidwe wopanda chitonthozo wa awo amene lerolino aika chikhulupiriro pobisalira pabodza pa Chikristu Chadziko. Iwo ali panja pamphepo, kunena kwake titero. Ino sindiyo nthaŵi yakufunafuna kakhalidwe kabwino m’makonzedwe adziko kaamba ka mtendere ndi chisungiko. Poyandikira machitidwe achiweruzo cha Mulungu, zigwirizano ndi olamulira andale zadziko sizidzapereka mkhalidwe wachitonthozo kwa Chikristu Chadziko.

Chochita Chodabwitsa cha Yehova

6. Kodi ndimotani mmene Yehova akachitira motsutsana ndi Yuda, ndipo ndimotani mmene adzachitira motsutsana ndi Chikristu Chadziko?

6 Pokhala atafotokoza mopereka chithunzi mkhalidwe wopanda chitonthozo wa Yerusalemu wosakhulupirika wa m’tsiku lake​—ndi wa Chikristu Chadziko chosakhulupirika chamakono​—Yesaya anapitirizabe kunena kuti: ‘Yehova adzauka monga m’phiri la Perazimu, nadzakwiya monga m’chigwa cha Gibeoni; kuti agwire ntchito yake, ntchito yake yachilendo, ndi kuti achite chochita chake, chochita chake chachilendo.’ (Yesaya 28:21) Inde, Yesaya anachenjeza, posachedwapa Yehova adzauka monga mmene anachitira pa Baalaperazimu. Koma panthaŵiyi iye adzachita motsutsana ndi anthu ake osakhulupirika, ndipo akachita motero mofanana ndi chigumula cha madzi owopsa otulukira pa m’ng’alu wa damu limene likugumuka. Pangano la Yerusalemu ndi imfa likawoneka kukhala lachabechabe. Mwanjira yofananayo, Yehova adzachitapo kanthu posachedwapa motsutsana ndi Chikristu Chadziko, ndipo chidzapeza kuti mapangano ake onse oledzeretsa ndi dziko lino ngachabechabe. Gulu lake lalikululo lidzaswedwa ndipo nzika zake zidzabalalitsidwa. Milungu yake yonyenga idzatenthedwa kotheratu.

7. Kodi nchifukwa ninji zifuno za Yehova kulinga kwa Yuda zinatchedwa ‘zodabwitsa’ ndi ‘zachilendo’?

7 Kodi nchifukwa ninji Yesaya akutcha kachitidwe ka Yehova kameneka motsutsana ndi Yerusalemu kukhala ntchito yodabwitsa ndi yachilendo? Eya, Yerusalemu anali likulu la kulambira kwa Yehova ndi mzinda wa mfumu yodzozedwa ya Yehova. (Salmo 132:11-18) Motero, iye anali asanawonongedwepo. Kachisi wake sanatenthedwepo. Nyumba yachifumu ya Davide, panthaŵi ina yokhazikitsidwa m’Yerusalemu, siinalandidwepo. Zinthu zoterozo zinali zosaganizirika. Kunali kwachilendo kwenikweni kuti Yehova akalingalira za kulola zinthu zoterozo kuchitika.

8. Kodi Yehova anapereka chenjezo lotani la ntchito yake yachilendo yobwerayo?

8 Komatu Yehova anapereka chenjezo lokwanira kupyolera mwa aneneri ake kuti zinthu zozizwitsa zikachitika. (Mika 3:9-12) Mwachitsanzo, mneneri Habakuku, yemwe anakhala ndi moyo m’zaka za zana lachisanu ndi chiŵiri B.C.E., anati: ‘Penyani mwa amitundu, penyetsetsani, nimudabwe kwakukulu, pakuti ndichita ntchito masiku anu, imene simudzavomereza chinkana akufotokozerani. Pakuti tawonani, ndiukitsa Akasidi, mtundu uja woŵaŵa ndi wa liŵiro, wopitira pa chitando cha dziko lapansi, kuloŵa m’malo mosati mwawo, mukhale mwawo mwawo. Ali owopsa, achititsa mantha, chiweruzo chawo ndi ukulu wawo zituluka kwa iwo eni.’​—Habakuku 1:5-7.

9. Kodi Yehova anakwaniritsa motani chenjezo lake motsutsana ndi Yerusalemu?

9 Mu 607 B.C.E., Yehova anakwaniritsa chenjezo lake. Pokhala analola magulu ankhondo Achibabulo kudza motsutsana ndi Yerusalemu, iye anawalola kuwononga zonse ziŵiri mzinda ndi kachisi. (Maliro 2:7-9) Ndiponso, iye analolanso kuti Yerusalemu awonongedwe kachiŵiri. Chifukwa ninji? Eya, pambuyo pa zaka 70 za ukapolo, Ayuda olapa anabwerera ku dziko lakwawo, ndipo m’kupita kwanthaŵi kachisi wina anamangidwa m’Yerusalemu. Komabe, kachiŵirinso, Ayudawo anamsiya Yehova. M’zaka za zana loyamba C.E., Paulo anagwira mawu a Habakuku nauza Ayuda a m’tsiku lake, akumawachenjeza kuti ulosiwo ukakhalanso ndi kugwiritsiridwa ntchito mtsogolo. (Machitidwe 13:40, 41) Yesu iyemwini anachenjeza mwachindunji kuti Yerusalemu ndi kachisi wake akawonongedwa chifukwa cha kusoŵa chikhulupiriro kwa Ayuda. (Mateyu 23:37–24:2) Kodi Ayuda a m’zaka za zana loyambawo analabadira? Ayi. Mofanana ndi makolo awo, iwo anakana kwa mtu wagalu chenjezo la Yehova. Chifukwa chake, Yehova anachitanso ntchito yake yodabwitsa. Yerusalemu ndi kachisi wake anawonongedwa mu 70 C.E. kupyolera mwa magulu ankhondo Achiroma.

10. Kodi ndimotani mmene Yehova adzachitira motsutsana ndi Chikristu Chadziko mtsogolo posachedwapa?

10 Pamenepa, kodi munthu aliyense angaganizirenji kuti Yehova sadzachita chinthu chofananacho m’nthaŵi yathuyi? Chenicheni nchakuti, iye adzakwaniritsa chifuno chake ngakhale kuti chikuwonekera kukhala chodabwitsa ndi chachilendo kwa okaikira. Nthaŵi ino chandamale cha kachitidwe kake chidzakhala Chikristu Chadziko, chimene, mofanana ndi Yuda wakale, chimati chimalambira Mulungu koma chakhala chachinyengo mopanda chiyembekezo. Kupyolera mwa Davide wake Wamkulu, Kristu Yesu, Yehova adzatsikira “Afilisti” a Chikristu Chadziko pa ola limene iwo sadzaliyembekezera. Iye adzachita ntchito yake yachilendo ku mlingo wakufafaniziratu zidutswa zotsalira za dongosolo lachipembedzo la Chikristu Chadziko.​—Mateyu 13:36-43; 2 Atesalonika 1:6-10.

Chenjezo la Kachitidwe ka Yehova

11, 12. Kodi ndimotani mmene Mboni za Yehova zachenjezera za kubwera kwa ziweruzo za Yehova?

11 Kwa zaka zambiri Mboni za Yehova zachenjeza za kachitidwe kachiweruzo kakudzako ka Yehova. Izo zasonyeza kuti kuwonongedwa kwa Yerusalemu ndi kachisi wake mu 607 B.C.E. ndiponso mu 70 C.E. kunali machenjezo aulosi a chimene chidzachitika kwa Chikristu Chadziko. Ndiponso, izo zasonyeza kuti Chikristu Chadziko, chifukwa cha mpatuko wake, chakhala mbali ya ulamuliro wadziko wa chipembedzo chonyenga, Babulo Wamkulu. Chifukwa cha ichi, ziweruzo za Mulungu pa Babulo Wamkulu zidzaperekedwa makamaka pa Chikristu Chadziko, popeza kuti ndicho mbali yaliŵongo lalikulu koposa m’gulu la Satana.​—Chibvumbulutso 19:1-3.

12 Mboni za Yehova zaloza ku ulosi wa Baibulo wochenjeza kuti panthaŵi yake ya Yehova, mabwenzi andale zadziko a Babulo Wamkulu adzamtembenukira. Pophiphiritsira ameneŵa monga nyanga khumi za chirombo chofiira, Chibvumbulutso chikuchenjeza motere: ‘Ndipo nyanga khumi udaziwona, ndi chirombo, izi zidzadana ndi mkazi wachigololoyo [Babulo Wamkulu], nizidzamkhalitsa wabwinja wausiwa, nizidzadya nyama yake, nizidzampsereza ndi moto.’ (Chibvumbulutso 17:16) Chikristu Chadziko chachipembedzo chidzapserezedwa ndi kuwonongedwa pamodzi ndi zipembedzo zonyenga zonse. Aka kadzakhala kachitidwe kodabwitsa ka Yehova, ntchito yake yachilendo ya m’tsiku lathu.

13. Kodi ndimotani mmene machitidwe kulinga ku machenjezo a Yehova afananira ndi zimene Yesaya anayang’anizana nazo?

13 Pamene Mboni za Yehova zipereka chenjezo la tsoka likudzalo, izo kaŵirikaŵiri zimayang’anizana ndi kusekedwa konyodola. Anthu amadabwa kuti izo zimaganiza kuti ziri ndani pomanena zinthu zoterozo. Chikristu Chadziko chimawoneka kukhala chosatekeseka, chokhazikika bwino lomwe. Eya, ena amalingalira kuti mathayo ake awongokeradi. Maboma amene anali kuchitsendereza posachedwapa achipatsa ufulu waukulu wakuchita zinthu. Kwenikweni, Chikristu Chadziko chiyenera kulabadira uphungu wa Yesaya wakuti: ‘Tsono musakhale amnyozo, kuti nsinga zanu zingalimbe; pakuti Ambuye, Yehova wa makamu, wandimvetsa za chiwonongeko chotsimikizidwa padziko lonse lapansi.’​—Yesaya 28:22; 2 Petro 3:3, 4.

14. Kodi ndimotani mmene nsinga za Chikristu Chadziko zikulimbiralimbira ndi kuning’irabe?

14 Kwakukulukulu, Chikristu Chadziko chidzapitirizabe kumachita motsutsana ndi Mfumu ndi Ufumu wake. (2 Atesalonika 2:3, 4, 8) Komabe, panthaŵi imodzimodziyo, nsinga zake zidzalimbiralimbira ndi kuning’irabe. M’mawu ena, chiwonongeko chake chidzakhala chotsimikizirika kwenikweni. Yehova sadzasintha chosankha chake chakuwononga Chikristu Chadziko monga momwe sanasinthire chosankha chake chakulola kuwonongedwa kwa Yerusalemu ndi kachisi wake mu 607 B.C.E.

‘Tulukani Mmenemo’

15. Kodi ndinjira yothaŵira yotani imene iri yotseguka kwa anthu owongoka mtima?

15 Kodi ndimotani mmene munthu aliyense angathaŵire tsoka la Chikristu Chadziko? Kalelo m’masiku a Israyeli, Yehova anatumiza aneneri ake okhulupirika kuwaitana anthu owongoka mtima kubwerera ku kulambira koyera. Lerolino, iye wautsa Mboni zake, tsopano zomwe ziri mamiliyoni, kaamba ka chifuno chimodzimodzicho. Izo zimavumbula mopanda mantha mkhalidwe wakufa mwauzimu wa Chikristu Chadziko. Mwakuchita motero, iwo amamveketsa mokhulupirika zilengezo zonga mliri za kuwombedwa kwa malipenga aungelo a pa Chibvumbulutso mitu 8 ndi 9. Ndiponso, izo zalengeza mwakhama kuchonderera kolembedwa pa Chibvumbulutso 18:4 uku: ‘Tulukani mmenemo, anthu anga; . . . kuti mungalandireko ya miliri yake.’ “Yake” wonenedwa panopa ndiye Babulo Wamkulu, ulamuliro wadziko lonse wa chipembedzo chonyenga, umene chiŵalo chake chofunika kwambiri ndicho Chikristu Chadziko.

16. Kodi mamiliyoni athaŵa mwanjira yanji kuchoka ku chipembedzo chonyenga?

16 Chiyambire 1919, ndipo makamaka chiyambire 1922, khamu lomakulakula la ofatsa, ovomereza kuchonderera kumeneko, amthaŵa Babulo Wamkulu. Poyamba mazana, kenaka zikwi makumi, ndipo tsopano mamiliyoni achoka ku chipembedzo chonyenga, makamaka Chikristu Chadziko, ndipo athaŵira ku kulambira koyera. (Yesaya 2:2-4) Iwo amadziŵa kuti kokha mwakuchoka ku Babulo Wamkulu ndipamene angapeŵe kukanthidwa ndi miliri yake, imene idzathera m’chiwonongeko chake pamene nthaŵi ifika yakuti Yehova achite ntchito yake yachilendo.

17, 18. Kodi ndimotani mmene Yehova wakhalira korona wa ulemerero ndi wokongola kwa anthu ake?

17 Mneneri Yesaya akufotokoza mkhalidwe wachimwemwe wa awo omwe atenga kaimidwe ka kulambira koyera. Iye akuti: ‘Tsiku limenelo Yehova wa makamu adzakhala korona wa ulemerero, ndi korona wokongola kwa anthu ake otsala: ndipo adzakhala mzimu wa chiweruziro kwa oweruza milandu, ndi mphamvu kwa iwo amene abweza nkhondo pachipata.’​—Yesaya 28:5, 6.

18 Chifukwa cha kukhulupirika kwawo ku chowonadi, Yehova akukhala korona wa ulemerero wosatha kaamba ka ziŵalo zodzozedwa za gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Ichi chakhala chowona makamaka chiyambire 1926. M’chakacho, kope la January 1 la The Watch Tower linagogomezera kufunika kwa kulemekeza dzina la Yehova m’nkhani yochititsa chidwi yokhala ndi mutu wakuti “Who Will Honor Jehovah? [Kodi Ndani Adzalemekeza Yehova?]” Chiyambire pamenepo, Akristu odzozedwa abukitsa dzinalo padziko lonse kuposa ndi kalelonse. Mu 1931 iwo anazindikiridwa kukhaladi ndi Yehova mwakutenga dzina lakuti Mboni za Yehova. Ndiponso, khamu lalikulu la nkhosa zina latulukanso m’Chikristu Chadziko ndi Babulo Wamkulu yense. Magulu aŵiriŵa atenga dzina la Mulungu. Kodi chotulukapo chakhala chiyani? Yehova iyemwini​—mmalo mwa ufulu wautundu wosakhalitsa​—wakhala korona wa ulemerero ndi wokongola pa anthu pafupifupi mamiliyoni anayi m’maiko ndi zisumbu za m’nyanja zoposa 212. Ndi ulemerero wotani nanga umene iwoŵa ali nawo wakuchitira umboni dzina la Mulungu wamoyo yekha wowona!​—Chibvumbulutso 7:3, 4, 9, 10; 15:4.

“Mzimu wa Yehova Udzambalira Iye”

19. Kodi ndani yemwe akukhala pachiweruzo, ndipo ndimotani mmene Yehova wakhalira mzimu wa chiweruzo cholungama kwa iye?

19 Kwa Yesu, ‘wokhala pachiweruzoyo,’ Yehova wakhala ‘mzimu wa chiweruzo.’ Pamene Yesu anali padziko lapansi, iye anakana kulakidwa ndi mzimu woledzeretsa wa zigwirizano zadziko. Lerolino, monga Mfumu yoikidwa pampando wachifumu ndi Yehova, iye wadzazidwa ndi mzimu woyera, umene umamtsogoza kupanga zosankha zolinganizika, zomvekera. Mwa Yesu ulosi wakwaniritsidwa wakuti: “Ndipo mzimu wa Yehova udzambalira iye mzimu wanzeru ndi wakuzindikira, mzimu wa uphungu ndi mphamvu, mzimu wakudziwa ndi wakuopa Yehova.” (Yesaya 11:2) Indedi, kupyolera mwa Yesu, Yehova ‘adzayesa chiweruziro chingwe chowongolera, ndi chilungamo chingwe cholungamitsira chiriri.’ (Yesaya 28:17) Pamene kuli kwakuti adani oledzera mwauzimu adzafafanizidwa m’chiwonongeko, chiweruzo cholungama chidzachitidwa ku dzina loyera la Yehova ndi uchifumu wake wachilengedwe chonse.

20, 21. Kodi mawu a Yesaya 28:1-22 amakuyambukirani m’njira yanji?

20 Pamenepo, nditanthauzo lalikulu chotani nanga limene ulosi umenewu wa Yesaya mutu 28 uli nalo kwa ife lerolino! Ngati tipeŵa zidakwa zauzimu za Chikristu Chadziko ndi kumamatira ku kulambira koyera, tidzatetezeredwa pamene Yehova achita kachitidwe kake kodabwitsa ndi ntchito yake yachilendo. Ha, timasangalala motani nanga kudziŵa ichi! Ndipo ndife achimwemwe chotani nanga polingalira kuti pamene zinthuzi zichitika, aliyense adzakakamizika kudziŵa kuti Yehova wa makamu wachita mokomera anthu ake okhulupirika ndi kaamba ka kulemekezeka kwake mwa Yesu Kristu!​—Salmo 83:17, 18.

21 Motero Akristu enieni onse apitirizebe mopanda mantha kuchenjeza za kachitidwe kodabwitsa ka Yehova. Iwo aumiriretu m’kunena za ntchito yake yachilendo. Pamene akutero, alengezetu kwa onse kuti chiyembekezo chathu chosagwedezeka chiri mu Ufumu wa Mulungu wokhala pansi pa Mfumu yake yoikidwa. Changu chawo, kutsimikiza mtima, ndi kukhulupirika ziwonjezere chitamando chosatha cha Mulungu wathu wamphamvuyonse, Yehova.​—Salmo 146:1, 2, 10.

Kodi Mungakumbukire?

◻ Kodi nchifukwa ninji Chikristu Chadziko chiri mumkhalidwe wopanda chithonthozo?

◻ Kodi chifuno cha Yehova chinali chotani kulinga kwa Yerusalemu, ndipo nchifukwa ninji ichi chinali ‘chodabwitsa’ ndi ‘chachilendo’?

◻ Kodi ndinjezo lotani limene Mboni za Yehova zafalitsa ponena za Chikristu Chadziko, ndipo kodi izo zayang’anizana ndi kachitidwe kotani?

◻ Kodi ndimotani mmene anthu angathaŵire tsoka la Chikristu Chadziko?

[Chithunzi patsamba 24]

Yehova adzabwerezanso kachitidwe kake kodabwitsa, panthaŵiyo motsutsana ndi Chikristu Chadziko

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena