Nyimbo 80
Kuyenda m’Dzina la Mulungu Wathu
(Mika 4:5)
1. Mfumu yammwamba Yehova wathu,
Chikondi chanu titamanda’nu.
Mukhululuka; mwapatsa moyo.
Mbuye, tikhala muntchito yanu.
2. Adani athu apanga gulu.
Mwa milungu yonyenga anyada.
Itinyansadi; tilalikira
Tiyenda mwa Ya ndi kupemphera.
3. Ku Betelehemu kudza Mfumu,
Mbusa apulumutsa ndi mphamvu.
Mwachimwemwedi, Otsalirawo,
Atamanda kulambira kwanu.
4. Idzani titumikiretu Ya.
Tidzaphunzire; chifuno chake.
Lupanga nkondo zidzachotsedwa.
Mwachimwemwe tidzamtumikira.