Nyimbo 163
Chipatso cha Mzimu
1. Zipatso za mzimu wa M’lungu
Ife tonse titulutse,
Kuti timlemekeze iye,
Adzatipatsatu moyo.
Nthaŵi zonse tisonyezetu
Chikondi chaumulungu
Sangalalani nthaŵi zonse,
Chimwemwe chipatsa mphamvu.
2. Tikhale ndi mtendere wa Ya
Tikhalenso muumodzi.
Kuleza mtima nkofunika,
Kuti tipilire zonse.
Chifundo chidzetsa zabwino!
Chichititsa ena kumva,
Ubwino umatithandiza
Kugaŵana chimwemwecho.
3. Chipatso cha chikhulupiro
Chipatsa nyonga nchifuno.
Kudekha kulidi kwabwino!
Kumathetsa mikangano.
Kudziletsa nkofunikanso,
Kuti tisatayiketu.
Mwa kubala zipatso izi,
Tidzayanjidwa ndi M’lungu.