Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/01 tsamba 8
  • Kodi Mumasangalala Kuyenda ndi Ena mu Ulaliki?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mumasangalala Kuyenda ndi Ena mu Ulaliki?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
km 6/01 tsamba 8

Kodi Mumasangalala Kuyenda ndi Ena mu Ulaliki?

1 Kodi muganiza kuti kuyenda ndi ena mu ulaliki n’kopindulitsa? Yesu anatero. Ngakhale kuti zotuta zinali zochuluka ndipo antchito anali oŵerengeka, iye anatumiza ophunzira 70 m’munda, ali “aŵiriaŵiri.” Onseŵa anasangalala kwambiri polalikira “kumudzi uliwonse, ndi malo alionse kumene ati afikeko mwini”!—Luka 10:1, 17; Mat. 9:37.

2 N’kolimbikitsa kuyenda ndi ena mu ulaliki. Enafe ndife amanyazi ndipo kumativuta kufikira anthu osawadziŵa. Kukhala ndi wina kungatipatse mphamvu kulankhula Mawu a Mulungu molimba mtima. Tikakhala ndi wina, sikungakhale kovuta kugwira ntchitoyo monga taphunzirira. (Miy. 27:17) Munthu wanzeru anati: “Aŵiri aposa mmodzi.”—Mlal. 4:9.

3 N’kwabwino kuyenda ndi ofalitsa komanso apainiya osiyanasiyana. Mwa amene mtumwi Paulo anali kuyenda nawo mu utumiki panali Barnaba, Sila, Timoteo ndi Yohane Marko. Anapindula kwambiri polalikira pamodzi. Zingakhalenso motero lerolino. Kodi munayendapo mu ulaliki ndi amene wakhala m’choonadi nthaŵi yaitali? Papita nthaŵi tsopano chikhazikitsireni makonzedwe akuti apainiya athandize ena. Ngati ndinu mpainiya kodi mwadzipereka kuthandiza nawo pulogalamu imeneyi? Kodi mwavomera kuti mpainiya akuthandizeni? Ngati ndi choncho, yesetsani kwambiri kuyenda ndi mpainiya ameneyo nthaŵi zonse mu utumiki wakumunda kuti mupindule ndi maluso ake. Mwa kutero mudzaphunzira malingaliro ena abwino omwe adzakuthandizani kusintha. Ndiyeno, mungathe kuthandiza ofalitsa atsopanoko m’choonadi ndi zina mwa zimene mwaphunzirazo. Zimenezi zidzaŵathandiza kukhala ogwira mtima kwambiri ndiponso osangalala kwambiri mu utumiki wawo.

4 Kodi panopa muli ndi phunziro la Baibulo? Ngati muli nalo, bwanji osauza mkulu kapena woyang’anira dera kukachititsa nanu? Zimathandiza, ophunzira Baibulo athu akadziŵana ndi oyang’anira. Ngati mukuwopa kuchititsa phunziro pali mkulu, mwinamwake mkuluyo angafune kuchititsa inuyo mukungoonerera. Pambuyo pake, masukani kum’funsa malingaliro a mmene mungathandizire wophunzira wanuyo kupita patsogolo mofulumira.

5 Khalani wolimbikitsa pamene mukuyenda ndi ena mu ulaliki. Nenani ndemanga zabwino za gawolo. Osajeda anzanu kapena kuŵiringula za makonzedwe a mpingo. Ikani maganizo anu pa utumiki ndi madalitso a Yehova. Ngati mutero, inu ndi anzanuwo mudzabwerera kunyumba muli olimbikitsidwa mwauzimu.

6 Mikhalidwe yanu ingachititse kuti kuyenda ndi abale ndi alongo ena mu utumiki nthaŵi zonse kukhale kovuta. Komabe, ngati n’kotheka, konzani nthaŵi yoyenda ndi winawake mu utumiki. Nonse mudzapindula!—Aroma 1:11, 12.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena