-
Mafunso Ochokera kwa OŵerengaNsanja ya Olonda—1992 | August 1
-
-
Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Kodi pa Yobu 1:8 tiyenera kumvapo kuti m’nyengo imene Yobu anakhala ndi moyo, anali munthu yekha wokhulupirika kwa Yehova?
Ayi. Lingaliro limenelo silikulungamitsidwa ndi Yobu 1:8, amene amati:
“Ndipo Yehova anati kwa Satana, Kodi wawonerera mtumiki wanga Yobu? Pakuti palibe wina wonga iye m’dzikomo, munthu wangwiro ndi wowongoka, wakuwopa Mulungu ndi kupeŵa zoipa.” Mulungu anapereka malongosoledwe ofananawo pa Yobu 2:3, akumafunsa Satana kuti: “Kodi wawonerera mtumiki wanga Yobu? Pakuti palibe wina wonga iye m’dzikomo, munthu wangwiro ndi wowongoka, wakuwopa Mulungu, ndi kupeŵa zoipa.”
Bukhu la Yobu lenilenilo limasonyeza kuti Yobu sanali munthu yekha wamoyo amene Mulungu anavomereza monga wokhulupirika. Kuyambira Yobu m’chaputala 32, timaŵerenga za Elihu. Ngakhale kuti anali mnyamata, Elihu anawongolera kawonedwe ka zinthu kolakwa ka Yobu nalemekeza Mulungu wowona.—Yobu 32:6–33:6, 31-33; Yobu 35:1–36:2.
Ndiponso, mawu a Mulunguwo akuti ‘panalibe wina wonga Yobu m’dzikomo’ ayenera kutanthauza kuti Yobu kwakukulukulu anali wapadera monga munthu wolungama. Mwachiwonekere Yobu anakhalako m’nyengo yapakati pa imfa ya Yosefe m’Igupto ndi kuyamba kwa utumiki wa Mose monga mneneri wa Mulungu. M’nyengoyo namtindi wa Aisrayeli anali kukhala m’Igupto. Palibe chifukwa cholingalirira kuti onsewo anali osakhulupirika ndi osavomerezeka kwa Mulungu; mwinamwake panali ambiri amene anakhulupirira Yehova. (Eksodo 2:1-10; Ahebri 11:23) Komabe, palibe aliyense wa iwo amene anachita mbali yaikulu, yofanana ndi ya Yosefe, ndiponso olambira amenewo sanali apadera ponena za kulambira kowona, monga momwe Mose anakhalira potsogoza mtundu wa Israyeli kutuluka mu Igupto.
Komabe, kumalo ena kunali mwamuna waumphumphu wapadera. “Panali munthu m’dziko la Uzi, dzina lake ndiye Yobu; ndipo munthuyu anali wangwiro ndi wowongoka, wakuwopa Mulungu ndi kupeŵa zoipa.”—Yobu 1:1.
Chotero Yehova anakhoza kutchula Yobu monga chitsanzo chachiwonekere kapena chodziŵika bwino cha chikhulupiriro ndi kudzipereka. Mofananamo, olemba Baibulo Ezekieli ndi Yakobo polankhula za kale anasankha Yobu kukhala wopereka chitsanzo cha chilungamo ndi chipiriro.—Ezekieli 14:14; Yakobo 5:11.
-
-
Msonkhano Wapachaka—October 3, 1992Nsanja ya Olonda—1992 | August 1
-
-
Msonkhano Wapachaka—October 3, 1992
MSONKHANO WAPACHAKA wa ziŵalo za Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania udzachitidwa pa October 3, 1992, pa Nyumba Yamsonkhano ya Mboni za Yehova, 2932 Kennedy Boulevard, Jersey City, New Jersey. Msonkhano woyambirira wa ziŵalo zokha udzakhalako pa 9:30 a.m, wotsatiridwa ndi msonkhano wapachaka wa onse pa 10:00 a.m.
Ziŵalo za bungwe la Corporation ziyenera kudziŵitsa Ofesi ya Mlembi tsopano zakusintha kulikonse kwa makeyala awo olandirira makalata kumene kungakhale kutachitika mkati mwa chaka chapitacho kotero kuti zikalata zanthaŵi zonse zoperekera chidziŵitso ndi zikalata zoponyera mavoti zikawafikire mwamsanga pambuyo pa August 1.
Zikalata zoponyera mavoti, zomwe zidzatumizidwa kwa ziŵalo limodzi ndi chidziŵitso cha msonkhano wapachaka, ziyenera kubwezedwa kotero kuti zifikire Ofesi ya Mlembi wa Sosaite osati pambuyo pa August 15. Chiŵalo chirichonse chiyenera kulemba ndi kubweza mwamsanga chikalata chake choponyera voti, akumanena kuti kaya adzafika iye mwini pamsonkhanopo kapena ayi. Chidziŵitso choperekedwa pachikalata choponyera voti chirichonse chiyenera kukhala chotsimikizirika pamfundo imeneyi, popeza kuti ndicho chimene chidzagwiritsiridwa ntchito kudziŵira amene adzafikapo iwo eni.
Tikuyembekezera kuti programu yonse, kuphatikizapo msonkhano wokambitsirana ntchito ndi malipoti, zidzamalizidwa podzafika 1:00 p.m. kapena mwamsanga pambuyo pake. Sipadzakhala programu yamasana. Chifukwa chakuchepa kwa malo, ofikapo adzaloledwa kokha ngati ali ndi tikiti. Palibe makonzedwe amene adzapangidwa a kulunzanitsa msonkhano wapachakawu ndi malo ena mwa nsambo za telefoni.
-