Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • “Inu Mumachita Zimene Mulungu Amafuna”
    Nsanja ya Olonda—1999 | January 15
    • “Inu Mumachita Zimene Mulungu Amafuna”

      MWA kumvera olamulira adziko “chifukwa cha Ambuye” Akristu akhoza ‘kusimbidwa [monga] ochita zabwino.’ (1 Petro 2:13-15) Zimenezi zinachitika m’mbuyomu kwa Mboni za Yehova ku South Africa pamsonkhano wawo wachigawo umene unachitikira m’holo ya pakoleji.

      Patsiku loyamba la msonkhanowu, apolisi apakolejiyi anali okonzeka kuthana ndi nthumwi zaukali ndi zosamvera, monga mmene zinali kukhalira pamisonkhano ina. Popeza anali asanakhalepo ndi Mboni za Yehova, anaona zodabwitsa!

      Monga ntchito yawo yachitetezo ya masiku onse, apolisiwo ankasecha galimoto lililonse loloŵa ndi lotuluka pagetipo. Anadabwa kwambiri pamene anapatsidwa moni mosangalala, modekha ndi mwaulemu mosasamala kanthu kuti anali kuwachedwetsa. Panalibe ndi munthu mmodzi yemwe wokana kusechedwa, kukangana nawo, ndi kuwatukwana. “Kusiyana ndi alendo ena,” anatero ofesala wa apolisiwo, “inu muli ndi mzimu wodzichepetsa komanso ulemu umene tonse timafuna.”

      Pamene mkulu wa apolisiwo anaona kusavuta kwa Mboni za Yehovazo, analamula kuti si kofunikanso kuti apitirize kusecha galimotozo “popeza muli ndi khalidwe labwino kwambiri,” anatero. Choncho, galimoto lililonse lokhala ndi pepala lolembedwa “JW” (Mboni za Yehova) linali kuloledwa kuloŵa osalisecha nkomwe.

      Msonkhanowo utatha, mkulu wa apolisiwo ananena kuti akuyembekeza kudzaonanso Mbonizo pamalopo. “Sitinaonepo anthu akhalidwe ngati inu,” anatero. “Inu mumachita zimene Mulungu amafuna.” Kuyamikidwa kumeneku ndi chifukwa china chomwe Akristu oona ‘amakhalira ndi mayendedwe okoma,’ kuti anthu ‘akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zawo zabwino.’​—1 Petro 2:12.

  • Kodi Mungafune Kukuchezerani?
    Nsanja ya Olonda—1999 | January 15
    • Kodi Mungafune Kukuchezerani?

      Ngakhale m’dziko lino lodzala ndi mavuto, mungapeze chimwemwe mwa kukhala ndi chidziŵitso cholongosoka cha Baibulo chonena za Mulungu, Ufumu wake, ndi chifuniro chake chabwino kwambiri kwa anthu. Ngati mungafune kudziŵa zambiri kapena kuti wina aziphunzira nanu Baibulo panyumba panu kwaulere, lemberani ku Watch Tower, Box 30749, Lilongwe 3, Malawi, kapena ku adiresi yoyenera pa maadiresi osonyezedwa patsamba 2.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena