Zimene Tingachite Tikafunikira Chithandizo cha Mankhwala cha Mwamsanga
1 Mneneri Yesaya analosera za nthaŵi imene palibe amene adzanena kuti: “Ine ndidwala.” (Yes. 33:24) Komabe, pamene tikali m’dongosolo la zinthu lino, tikukhala m’nthaŵi zowawitsa zovuta kuchita nazo. (2 Tim. 3:1) Anthu a Yehova akupeza mavuto amene anthu enanso akupezana nawo, monga ngozi ndi matenda. Kodi tingatani ngati tikufunika chithandizo cha mankhwala cha mwamsanga?
2 Tikadwala kapena wina m’banja lathu akadwala, timafuna chithandizo cha mankhwala chabwino kwambiri chimene chingapezeke. Ngati tipita kuchipatala, nthaŵi zambiri tingapeze chithandizo chimene tikufuna. Komabe, ngati tachita ngozi kapena ngati ali matenda aakulu ofuna thandizo la mwamsanga, madokotala angatiuze kuti tifunika kulandira magazi. Mboni za Yehovafe timasala magazi chifukwa cha chikumbumtima chathu chophunzitsidwa Baibulo. (Mac. 15:28, 29) Munthu sangati ‘akusala magazi’ pamene akuvomera kumuika magazi a munthu wina. Anthu a Yehova sangavomerenso kulandira magazi awo omwe, amene dokotala waachotsa ndi kuwasunga m’firiji asanachite opaleshoni ndiyeno n’kuwabwezera m’thupimo pochita kapena atamaliza opaleshoniyo. A zamankhwala amati kumeneku ndiko kusunga magazi opaleshoni isanachitike. Ndife olimba pa nkhani imeneyi ndipo sitimasintha.—Lev. 17:13.
3 N’chifukwa chiyani nthaŵi zambiri madokotala ndi anthu ena ogwira ntchito ya zachipatala amanena kuti ayenera kuika magazi? Nthaŵi zambiri, amachita zimenezo chifukwa amaganiza kuti imeneyo ndi njira yabwino kwambiri imene angathandizire odwala.
4 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti samafuna kuthandiza Mboni za Yehova? Ayi. Dokotala kapena nesi angakhulupirire kwambiri kuti kuika magazi n’kofunika kwabasi, ndipo angalimbikitse wodwala kuti alandire magazi. Chifukwa chiyani? Mwina amaganiza kuti wodwalayo wasankha molakwika pokana kulandira magazi. Motero, poganiza kuti mwina wodwalayo kapena abale ake sakudziŵa kufunika koika magazi, nthaŵi zambiri amaona kuti ayenera kufotokoza kufunika kochita zimenezi. Mwina angaumirire mfundo yawoyo. Nthaŵi zambiri, cholinga chawo pochita zimenezi chimakhala chabwino, chifukwa amafuna kuthandiza odwala. Ndiponso, mwina zingatheke kuti sakudziŵa kuti Mboni za Yehova zimavomera chithandizo china cha mankhwala. Mwina anamva mphekesera yakuti Mboni za Yehova sizilandira mankhwala alionse. Motero, ngati tingawafotokozere maganizo athu, nthaŵi zambiri amadabwa kudziŵa kuti Mboni za Yehova zambiri chikumbumtima chawo chimawalola kulandira zinthu zina zoloŵa m’malo mwa magazi ndiponso mitundu ina ya kuika magazi a munthu wodwala yemweyo. (Onani w00-CN 10/15 tsamba 30 Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga.)
5 Madokotala ndi manesi amaona kuti ndi udindo wawo kuthandiza odwala, ndipo ambiri amakhala okonzeka kulemekeza zikhulupiriro za odwala, makamaka zikakhala zachipembedzo. Apa mpamene tifunika kugwiritsa ntchito nzeru za Mulungu. Nthaŵi zina tingaganize kuti dokotalayo akudana nafe pamene akutiumiriza kuti tilandire magazi. Komabe, nthaŵi zambiri sikuti amachita zimenezi chifukwa chakuti akudana nafe. Monga mmene tanenera, dokotala angaganize kuti malinga ndi mmene zinthu zilili panthaŵiyo, chithandizo cha mankhwala chabwino kwambiri chimene angapereke ndicho kuika magazi. Komabe, zimenezi sizikutanthauza kuti sangamvetsere malingaliro athu. Nthaŵi zambiri, ngati timufotokozera kuti tikufuna kuti atithandize ndiponso kuti tili okonzeka kutsatira malangizo ake, ndi kuti tikufuna mankhwala ena oloŵa m’malo mwa magazi, adzamvetsera ndi kuyesa kutithandiza. Kumbukirani kuti tikapita kuchipatala ndi matenda a kayakaya, tisadabwe ngati ogwira ntchito zachipatala akutiuza kuti tifunika kulandira magazi. Ndipotu, nthaŵi zambiri tiziyembekezera zimenezo. Chifukwa chiyani? Nthaŵi zambiri chifukwa chake n’chakuti akufuna kutithandiza. Choncho, m’malo mochoka m’chipatalamo akangonena kuti atiika magazi, ndibwino kufotokoza maganizo athu mofatsa ndiponso mwaulemu. Ngati manesi kapena madokotala aang’ono sakutimvetsa, kungakhale bwino kulankhula ndi dokotala wamkulu, nthaŵi zambiri angathe kutimvetsa.
6 Apa mpamene pali ntchito yaikulu. Kodi tingathe kufotokoza mofatsa maganizo athu kwa dokotala kapena nesi? Mmene zateremu, tinene chiyani? Kumbukirani kuti sitikuyesa kutsimikizira dokotalayo kuti ndife olondola, kapena kumuumiriza kuti agwirizane ndi maganizo athu pankhani ya kuikidwa magazi. Tikungofuna kuti dokotalayo atithandize komabe alemekeze chikhulupiriro chathu chachipembedzo. Nthaŵi zambiri, ngati tifotokoza chikhulupiriro chathu tingapeŵe kukangana.
7 Kodi tingatani ngati nesi akutiuza kuti tibwerere kwathu chifukwa tikukana kuti atiike magazi? Yesetsani kupeŵa kukangana. Ngati mukuona kuti palibe amene akukumvetserani, pemphani kuti muonane ndi dokotala wamkulu. Nthaŵi zina zimenezi zingathandize. Ngati zimenezi zakanika, yesani kuuza akulu a mumpingo wanu amene angathe kuthandiza. Ngati iwo sangathe kuthandiza ngakhale atayesetsa motani, angadziŵitse mmodzi mwa abale a m’Komiti Yolankhulana ndi Chipatala ya m’dera lanu. Abale ameneŵa angadziŵe dokotala kapena chipatala chomwe n’chodzipereka kuthandiza Mboni za Yehova molemekeza zikhulupiriro zathu. Ndiponso, ngati mukudziŵa kuti mudzapita kuchipatala kuti akachite opaleshoni yaikulu, n’kwanzeru kudziŵitsa mmodzi mwa akulu a mu mpingo wanu. Iwo angayang’anire mmene zinthu zikuchitikira. Ndiyeno, angakhale okonzeka kufunsa Komiti Yolankhulana ndi Chipatala yomwe ili pafupi kuti iwapatse malangizo ngati patakhala vuto lililonse.
8 Chimodzi mwa zinthu zofunika kwambiri kuchita ndicho kuyenda nthaŵi zonse ndi khadi la Chidziŵitso kwa Dokotala/Chommasula ku Mlandu. N’zodabwitsa kudziŵa kuti abale athu ambiri mpaka pano satenga khadili akamayenda, ngakhale kuti timalandira malangizo ambiri pankhani imeneyi. Komabe, sitifunika kuchita zinthu monyanyira tikatenga khadili. Tisachite kuliika kunja kwa zovala zathu nthaŵi zonse, ngati kuti kukana kuikidwa magazi ndiko chiphunzitso chachikulu cha Mboni za Yehova. Tisamachite zimenezi.
9 Ngozi ndi matenda n’zinthu zovutitsadi maganizo. Tikulakalakatu kudzakhala m’nthaŵi imene mneneri Yesaya analosera! (Yes. 33:24) Komabe, monga momwe taonera, pali zambiri zimene tingachite pakali pano kuti anthu adziŵe zimene timakhulupirira komanso tisalole kuzisiya.