Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/01 tsamba 6
  • Kulimbitsa Banja

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulimbitsa Banja
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
km 9/01 tsamba 6

Kulimbitsa Banja

1 Banja ndi chinthu chofunika kwambiri kwa anthu. Kale, banja likatha makamaka chifukwa cha makhalidwe oipa a makolo kapena a ana, maufumu ankatha mphamvu. Zimenezi zinachitikira maufumu a Girisi ndi Roma. Monga mukudziŵa, zochitika padziko masiku ano zikufanana ndi za m’nthaŵi ya Nowa ndi Loti, kuti chiwawa ndi chisembwere n’zofala padziko lonse.—Gen. 6:2b, 5, 11-13; 18:20; 19:5, 13; Luka 17:26-30.

2 Popeza tikukhala mu nthaŵi ya makhalidwe oipa ndi ya zochitika zosinthasintha, kodi makolo achikondi angatetezere motani moyo wauzimu wa banja lawo? Chimodzi mwa zinthu zimene angagwiritse ntchito kuteteza banja ndicho phunziro la banja la Baibulo lokhazikika. Makolo amene amadera nkhaŵa za tsogolo la ana awo adzayesetsa kuchititsa phunziro la Baibulo mlungu uliwonse mogwiritsa ntchito mabuku a “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.”—Mat. 24:45-47.

3 N’kofunika kuti mitu ya mabanja izionetsetsa kuti onse m’banjamo amene amadziŵa kuŵerenga ali ndi Baibulo lawolawo ndi buku lothandizira kuphunzira Baibulo limene akugwiritsira ntchito pa phunziro la banja. Kuchita zimenezi kudzathandiza kuti onse amene alipo ayendere nanu limodzi ndi kuyankha zomveka. Onetsetsani kuti mwaitanitsa mabuku amene mukuwafuna kudzera ku mpingo wanu. Mtumiki wa mabuku ndi mlembi azionetsetsa kuti atumiza mwamsanga oda ya mabuku ya mpingo ya mwezi ndi mwezi ku ofesi ya Sosaite.

4 Monga takhala tikunenera, n’kwabwino kusankha nkhani zophunzira pa phunziro la banja zogwirizana ndi mavuto a banjalo. Kungakhale kwabwino kuphunzira Nsanja ya Olonda yomwe mukaphunzire ku msonkhano wampingo, kapena kungakhalenso kwabwino zedi kuphunzira nkhani za m’buku la Kukambitsirana zonena za mavuto amene ana amapezana nawo kusukulu. Mungachite chimodzimodzi ndi nkhani zina za mu buku la Achichepere Akufunsa. Mutu wa banja ungachite bwino kudziŵa zinthu zimene zikuchitikira ana ake ku sukulu kuti athe kusankha zimene zingakhale bwino kuziphunzira pa phunziro la banja. Ndiponso azimvetsera zimene mkazi wake angamuuze pankhani ya zimene zimachitika ku sukulu, popeza kuti nthaŵi zambiri mayi ndi amene amakhala pafupi ndi anawo ndipo angadziwe zimene zili m’maganizo ndi m’mitima mwawo.

5 Nthaŵi zonse, chimene chimavuta mutu wa banja ndicho kuchititsa phunziro losangalatsa ndi lokomera ana. Afunika kukhala tcheru kudziŵa momwe ana ngakhale aang’ono kwambiri akuchitira, kuti azidziŵa kuti onse akumvetsera komanso kupindula ndi nkhani zauzimu zimene akukambirana. Kukumbukira kuti ali ndi ana aang’ono kudzam’thandiza kuchititsa phunziro lalifupi, kapena kuphunzira pang’onopang’ono kangapo pamlungu, popeza ana aang’ono nthaŵi zambiri satha kumvetsera kwa nthaŵi yaitali.

6 Inde, phunziro la banja lokhazikika limathandiza kwambiri kulimbitsa banja mwauzimu. Nthaŵi zonse mutu wa banja uzitsogolera kukambirana nkhani zauzimu pa banja, koma osati kamodzi kokha pamlungu. Kumbukirani kuti m’nthaŵi ya Israyeli wakale, anthu a Mulungu analimbikitsidwa kuti nthaŵi zonse azilingalira za Yehova ndi zimene watichitira. (Deut. 11:18, 19) Mitu ya mabanja ikagwira ntchito yawoyi ndi mtima wonse ndiponso ikalimbikira kutsatira malangizo a m’Baibulo okhudza kuphunzitsa ana, mabanja olimba adzabala mipingo yolimba. Mipingo yolimba imapanga ubale wolimba wa padziko lonse umene nthaŵi zonse umatamanda dzina la Yehova.—Sal. 150:6.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena