Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/01 tsamba 3-4
  • Kodi Mumaloŵa mu Utumiki Wakumunda Nthaŵi Zonse?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mumaloŵa mu Utumiki Wakumunda Nthaŵi Zonse?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
km 9/01 tsamba 3-4

Kodi Mumaloŵa mu Utumiki Wakumunda Nthaŵi Zonse?

1 Mfumu Davide inazindikira kuti “zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo lionetsa ntchito ya manja ake.” Choncho, pamene dzuŵa, mwezi ndi nyenyezi zigwira ntchito imene Mulungu pozilenga ankafuna kuti zizigwira, zimapereka ulemerero ndi ulemu kwa Mlengi.—Sal. 19:1.

2 Kodi zolengedwa zopanda moyo zimenezi zimatamanda Yehova kangati? Davide akupitiriza kunena kuti: “Usana ndi usana uchulukitsa mawu, ndipo usiku ndi usiku uonetsa nzeru.” Chotero zinthu za kumwamba zimenezi zimalemekeza Mulungu Wamphamvuyonse mosalekeza, nthaŵi zonse.—Sal. 19:2.

3 Kodi dzuŵa limalankhula? Kodi mwezi umaimba nyimbo yokoma? Kodi nyenyezi zimalankhula mawu enieni otamanda Yehova? Ayi. Zinthu zopanda moyo zimenezi sizilankhula, monga mmene Davide akupitirizira kunena kuti: “Palibe chilankhulidwe, palibe mawu; liwu lawo silimveka.”—Sal. 19:3.

4 Mavesi oyambirira a Salmo 19 ameneŵa amanena za ulemerero ndi chitamando zomwe zinthu zosalankhula za kumwamba zimabweretsa kwa Mlengi. Zilibe mawu, sizilankhula. Koma sizileka kupereka umboni wa mphamvu ndi ukulu wa Yehova mwa kugwira ntchito zawo mokhulupirika ndiponso nthaŵi zonse.

5 Tsopano, lingalirani izi: anthu amalankhula. Choncho, kuli bwanji amuna ndi akazi, anyamata ndi atsikana, kodi sangagwiritse ntchito luso lawo la kulankhula potamanda Mlengi wawo? (Sal. 148:12, 13) Ndipo kodi anthu ayenera kulankhula kangati potumikira Yehova? Ndithudi, monga mmene dzuŵa, mwezi ndi nyenyezi zimachitira! N’zoonadi, anthu ayenera kutamanda Mlengi wawo nthaŵi zonse, mosalekeza.

6 Choncho, monga atumiki a Yehova, kodi tingafune kuti mwezi uzitha osalankhulako zotamanda Yehova? Malipoti akusonyeza kuti n’zimene ena amachita. M’mwezi wa May, mu mpingo wina wa ofalitsa 82, ofalitsa 34 okha ndi amene anapereka malipoti! Mu mpingo wina wa ofalitsa 87 ofalitsa 50 okha ndi amene anapereka malipoti, kuphatikizapo apainiya othandiza 6 ndi apainiya okhazikika 9. Mpingo wina uli ndi ofalitsa 118 koma ofalitsa 65 okha ndi amene anapereka malipoti, kuphatikizapo apainiya othandiza aŵiri ndi apainiya okhazikika 8. Tikuganiza kuti tingagwiritse ntchito kwambiri apainiya kuthandiza ena m’mipingo yotereyi.

7 Kodi n’chifukwa chiyani pali vuto limeneli lopereka malipoti modumphadumpha? Kodi chingakhale chifukwa chakuti mpingo sunaitanitse mafomu a lipoti la mwezi ndi mwezi la (S-4)? Kapena kodi chingakhale chifukwa chakuti akulu sakumbutsa abale kapena kuwathandiza kupereka malipoti mwezi uliwonse? Kodi n’chifukwa chakuti mlembi amasunga mafomu a malipoti onse kunyumba kwake osabweretsa mafomuwa ku Nyumba ya Ufumu pamapeto a mwezi? Sizoona kuti ofalitsa ambiri saloŵa mu utumiki wakumunda mwezi uliwonse. Ayenera kuti amaloŵa mu utumiki koma sapereka malipoti a ntchito yawo.

8 Kodi tingathetse bwanji vuto limeneli? Choyamba, mipingo izionetsetsa kuti yaitanitsa ku Sosaite mafomu a malipoti. Ndiyeno mwezi uliwonse, ochititsa maphunziro a buku a mpingo aziona kuti wofalitsa aliyense m’gulu lawo walandira fomu ya lipoti ndi kuwalimbikitsa kukaika malipoti awo mu bokosi la malipoti ku Nyumba ya Ufumu. Ochititsa maphunziro a buku ena ndi alembi ena kumapeto kwa mwezi amaima pakhomo pa Nyumba ya Ufumu ndi kumapatsa wofalitsa aliyense akamaloŵa kapena kutuluka mu Nyumba ya Ufumu fomu ya malipoti. Kodi zimenezi sizingathandize pampingo wanu? Woyang’anira dera akayendera mpingo wanu, aziona ngati zinthu tatchula m’ndime ino zikuchitika ndipo ngati mpingowo ufunika kuwongolera azinena zimenezo mu lipoti limene amasiyira akulu.

9 Mwa kutsatira malingaliro ameneŵa tidzapereka lipoti lolondola lakuti abale ndi alongo athu, akugwiritsa ntchito nthaŵi yawo kulemekeza Atate wathu wakumwamba nthaŵi zonse ndiponso mokhulupirika monga zimachitira zinthu zakumwamba. Ndiponso akuwapatsa anthu oona mtima mwayi wophunzira za Yehova. Tidzasonyeza kuti timakonda Yehova ndi mtima wathu wonse, nzeru zathu zonse, mphamvu zathu zonse, moyo wathu wonse, ndiponso kuti timawakondadi anansi athu.—Mat. 22:37-39.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena