Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Chikumbutso (Mgonero wa Ambuye)
    Kukambitsirana za m’Malemba
    • Mboni za Yehova zimasunga Chikumbutso pambuyo pa kuloŵa kwadzuŵa pa Nisani 14, mogwirizana ndi kuŵerenga kwa kalendala Yachiyuda imene inali yofala m’zaka za zana loyamba. Tsiku Lachiyuda limayamba pa kuloŵa kwadzuŵa ndipo limapitirira kufikira kuloŵa kwadzuŵa kwatsiku lotsatira. Chotero Yesu anafa patsiku limodzimodzilo lakalendala Yachiyuda limene anayambitsa Chikumbutso. Chiyambi cha mwezi wa Nisani chinali kuloŵa kwadzuŵa pambuyo pa mwezi wam’mwamba watsopano pafupifupi ndi nyengo ya kufanana kwa masana ndi usiku umene unawonekera m’Yerusalemu. Deti la Chikumbutso limakhalako masiku 14 pambuyo pa tsikulo. (Motero deti la Chikumbutso silingayenderane ndi la Paskha yosungidwa ndi Ayuda amakono. Chifukwa ninji? Kuyambika kwa miyezi yawo yakalendala kwalinganizidwa kuti kuyenderane ndi mwezi watsopano wowonekera m’mlengalenga, osati mwezi watsopano wowonekera m’Yerusalemu, umene ungakhaleko maora 18 mpaka 30 pambuyo pake. Ndiponso, Ayuda ambiri lerolino amasunga Paskha pa Nisani 15, osati pa 14 monga momwe anachitira Yesu mogwirizana ndi zimene zinafotokozedwa m’Chilamulo cha Mose.)

  • Chilengedwe
    Kukambitsirana za m’Malemba
    • Chilengedwe

      Tanthauzo: Chilengedwe, monga momwe chalongosoledwera m’Baibulo chimatanthauza kuti Mulungu Wamphamvuyonse analinganiza ndi kuchititsa chilengedwe kukhalako, kuphatikizapo anthu ena auzimu ndi mitundu yonse yaikulu ya zamoyo padziko lapansi.

      M’dziko lamakono, lasayansi limeneli, kodi nkwanzeru kukhulupirira chilengedwe?

      “Malamulo a chilengedwe chonse ngotsimikizirika kwambiri kotero kuti sitimakhala ndi vuto kumanga chombo cha m’mlengalenga kuulukira pamwezi ndipo tingalinganize nthaŵi ya kuulukayo motsimikizirika kwambirimbiri kufikira kukamphindi. Malamulo amenewa ayenera kukhala atakhazikitsidwa ndi munthu wina.”—Mawu ogwidwa kwa Wernher von Braun, amene anali ndi mbali yaikulu m’kutumiza opita kutali m’mlengalenga kumwezi a ku Amereka.

      Chilengedwe chakuthupi: Ngati munapeza koloko yosunga nthaŵi bwino koposa, kodi mukananena kuti inakhalapo yokha mwa kuuluka ndi kugwirizana kwa fumbi? Mwachiwonekere, munthu waluntha anaipanga. Pali “koloko” yodabwitsadi kwambiri. Maplaneti ozungulira dzuŵa lathu, ndiponso nyenyezi m’chilengedwe chonse, zimayenda paliŵiro limene liri lolunjika kwambiri kuposa makoloko ambiri olinganizidwa ndi kupangidwa ndi anthu. Khamu lanyenyezi mu limene maplaneti ozungulira dzuŵa lathu ali limaphatikizapo nyenyezi zoposa mabiliyoni 100, ndipo akatswiri odziŵa za m’mlengalenga amayerekezera kuti pali makamu a nyenyezi otero mabiliyoni 100 m’chilengedwe chonse. Ngati koloko iri umboni wa kulinganiza kwaluntha, koposa kotani nanga chilengedwe chachikulu kwambirimbiri ndi chocholoŵana! Baibulo limalongosola Mlinganizi wake monga “Mulungu wowona, Yehova, . . . Mlengi wakumwamba ndi Wamkulukulu wozifunyulula.”—Yes. 42:5, NW; 40:26; Sal. 19:1.

      Planeti Dziko Lapansi: Podutsa chipululu chamchenga chouma, ngati munafika panyumba yokongola, yokonzedwa bwino mwanjira iriyonse ndi yodzala ndi zakudya, kodi mukanakhulupirira kuti inafikapo yokha mwa kuphulika? Ayi; mukanazindikira kuti munthu wina wokhala ndi luntha lalikulu anaimanga. Eya, asayansi sanapezebe moyo pamaplaneti ena alionse ozungulira dzuŵa lathu kusiyapo padziko lapansi; umboni wopezeka ukusonyeza kuti enawo ngopanda moyo. Planeti limeneli, monga momwe bukhu lotchedwa The Earth limanenera, ndiro “chozizwitsa cha chilengedwe, malo apadera.” (New York, 1963, Arthur Beiser, p. 10) Iro liri pamtunda woyenereradi kuchokera kudzuŵa kaamba ka moyo wa anthu, ndipo limayenda paliŵiro loyenereradi kuti ligwidwe pozungulira. Mpweya, umene umapezeka kokha kuzungulira dziko lapansi wopangidwa ndi nsanganizo yoyenerera ya mpweya wochirikiza moyo. Modabwitsa, kuunika kuchokera kudzuŵa, kalaboni dayokosayidi wochokera mu mpweya, ndi madzi ndi zokumbidwa m’nthaka yachonde zimagwirizana kutulutsa chakudya cha zamoyo za padziko lapansi. Kodi zonsezi zinangochitika mwa kuphulika kwina kosalamulirika m’mlengalenga? Science News imavomereza kuti: “Kukuwonekera ngati kuti mikhalidwe yeniyeni imeneyi ndi kulondola sizikanachitika konse mwa malunji.” (August 24 ndi 31, 1974, p. 124) Kunena kwa Baibulo nkwanzeru pamene limafotokoza kuti: “Pakuti nyumba iriyonse iri naye wina woimanga; koma wozimanga zonse ndiye Mulungu.”—Aheb. 3:4.

      Ubongo wamunthu: Makompyutala amakono apangidwa pambuyo pa mafufuzidwe aakulu ndi uinjiniya wosamalitsa. Iwo “sanangokhalako mwa iwo okha.” Bwanji ponena za ubongo wamunthu? Mosafanana ndi ubongo wanyama iriyonse, ubongo wakhanda laumunthu umaŵirikiza nthaŵi zitatu mu ukulu mkati mwa chaka chake choyamba. Kuti umagwira ntchito motani kukali chikhalirebe chinsinsi chachikulu kwa asayansi. Mwa anthu, muli mlingo waukulu wobadwa nawo wa kuphunzira zilankhulidwe zocholoŵana, kuyamikira kukongola, kupanga nyimbo, kusinkhasinkha chiyambi cha moyo ndi tanthauzo lake. Dokotala wa opareshoni ya ubongo Robert White anati: “Ndimasiyidwa ndiri wopanda chosankha kusiyapo kuvomereza kukhalako kwa Waluntha Wamkulu, amene analinganiza ndi kupanga unansi wodabwitsa umene uli pakati pa maganizo ndi ubongo—chinthu chimene chiri chosayerekezeka kwambiri kunzeru za munthu.” (The Reader’s Digest, September 1978, p. 99) Kukula kwa chozizwitsa chimenechi kumayambira paselo laling’onong’ono logwirizanitsidwa ndi ubwamuna m’mimba. Mwachidziŵitso chapadera, wolemba Baibulo Davide anati kwa Yehova: “Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchowopsa ndi chodabwiza; ntchito zanu nzodabwiza; moyo wanga uchidziŵa ichi bwino ndithu.”—Sal. 139:14.

      Selo lamoyo: Selo limodzi lamoyo nthaŵi zina limatchedwa mpangidwe “wosacholoŵana” wa moyo. Koma cholengedwa chaselo limodzi chingagwire chakudya, kuchipukusa, kuchotsa zinyansi, kudzimangira nyumba ndi kuphatikizidwa m’machitachita a kukwerana. Selo lirilonse la thupi lamunthu layerekezeredwa ndi mzinda walinga, wokhala ndi boma lalikulu losungitsa bata, makina amagetsi opangira magetsi, mafakitale opanga maprotini, dongosolo locholoŵana lazamtengatenga, ndi alonda olamulira zololedwa kuloŵa. Ndipo thupi limodzi lamunthu lapangidwa ndi maselo ochuluka kufikira matriliyoni 100. Ha ngoyenerera chotani nanga mawu a Salmo 104:24 akuti: “Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonsezi mwanzeru”!

      Kodi Baibulo limapereka mpata wa lingaliro lakuti Mulungu anagwiritsira ntchito chisinthiko kutulutsa mitundu yosiyanasiyana ya zinthu zamoyo?

      Genesis 1:11, 12 imanena kuti maudzu ndi mitengo zinapangidwa kuti chirichonse chitulutse “monga mwa mtundu yake.” Mavesi 21, 24, 25 amawonjezera kuti Mulungu analenga zolengedwa za m’nyanja, zolengedwa zouluka ndi zinyama za pamtunda, iriyonse “monga mwa mtundu wake.” Panopa sipakupereka mpata wakuti mtundu waukulu umodzi usinthike kapena kusinthira kumtundu wina.

      Ponena za munthu, Genesis 1:26 ikusimba kuti Mulungu anati: “Tipange munthu m’chifanizo chathu, monga mwachikhalidwe chathu.” Chotero anali kudzakhala ndi mikhalidwe

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena