Nyimbo 165
Tamandani Ya Limodzi Nane!
1. Tamani Ya, Mfumu yathu.
Anthu onse amulemekeze.
Tidalitse dzina lake,
Uzani anthu za mphamvu yake.
Inde, nenani za mphamvu yake.
2. Tamani Ya. Wachifundo
Aleza mtima ndi ife tonse.
Wodabwitsa ndi wamkulu;
Zochita zake nzosangalatsa.
Inde, nzosangalatsa kwambiri.
3. Tamani Ya. Mgaŵiriyo
Apatsa chakudya kwa onsewo.
Alimbitsa ofooka.
Bwanji anthu samayamikira?
Inde, anthu ayamikiretu.
4. Tamani Ya, Ngwapafupi;
Kwa onse oitana amvera.
Awononga oipawo,
Adzasunga onse omkondawo.
Inde, adzasunga omkondawo.