Nyimbo 39
Gulu Lankhondo la Mulungu Likupita Patsogolo
1. Ankhondo a Mulungu;
Alidi amphamvu
Kutamanda Yehova,
Nasunga lamulo.
Ngakhale chinjokacho
Chilimbika nkhondo,
Mthunzi wa dzanja lake
M’lungu atisunga.
2. Njolimba nkhondo yathu
M’tsiku la Yehova.
Tilankhula molimba.
Tiwopsedwerenji?
Mwana wake ndi Ngwazi,
Amenyera bwino.
Ayamba kumenyako;
Tiyeni nayetu.
3. Tipita patsogolo;
M’lungu adzalaka.
Changu chisalephere,
Timlemekezetu!
Chilakiko chidzadi,
Mphotho yalonjezo
Idikira amphumphu,
Osatula chida.