Nyimbo 26
Kukwaniritsa Zofunika za Mulungu
1. Tidalirike kwa M’lungu,
Tiri kusunga umphumphu.
Kunyumba ndi nyumba timke
Kulalika za Yehova.
Monga Mboni ife timka
Kuŵatonthoza olira;
Kulemba pamphumi pawo,
Kuti apulumutsidwe.
2. Ngati tidzipenyerera,
Tidzaŵala mokwanira.
Moyo wosatha ndiwathu,
Poutchinjiriza mtima.
Ife tikalalikira,
Ambiri adzamva Mawu.
Powongola njira zathu,
Chimwemwe chidzakwanira.
3. Tithandizetu abale,
Ndiponso anansi athu,
Ndikukhala mumtendere,
Ndi otumikira M’lungu.
Tiyamikira kwambiri,
Gawo lakutumikira.
Mosalakwa tilisunge,
Kulemekeza Yehova.