Kuphunzira Pakati pa Anthu a Mulungu
1 M’masiku akale anthu ambiri a Mulungu anali ophunzira. Pafupifupi zaka 3,500 zapitazo, Mose analemba mabuku asanu oyambirira a Baibulo. Yoswa, yemwe analoŵa m’malo mwa Mose, analamulidwa kuŵerenga Malemba “usana ndi usiku” kuti ntchito imene Mulungu anamupatsa imuyendere bwino. Ndipo Mulungu analamula kuti mafumu a Israyeli, akaloŵa ufumu, azidzilembera kope la Chilamulo ndi kumaliŵerenga tsiku lililonse.—Yos. 1:8; Deut. 17:18, 19.
2 Yesu ankatha kuŵerenga mipukutu yonse youziridwa ya Malemba Achihebri m’masunagoge, kumene nthaŵi ina, anaŵerenga poyera ndi kunena kuti lembalo linali kunena za iye. Atumwi akenso anali ophunzira, ankagwira mawu ndi kutchula Malemba Achihebri kambirimbiri m’zinthu zimene analemba.—Luka 4:16-21; Mac. 17:11.
3 Anthu a Mulungu Lerolino: Yesu anauza otsatira ake ‘kuphunzitsa anthu a mitundu yonse, . . . kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene anawalamulira.’ Analoseranso kuti ‘uthenga wabwino wa ufumu ukalalikidwa padziko lonse lapansi.’ (Mat. 24:14; 28:19, 20) Monga Akristu a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, Mboni za Yehova lerolino zatsatira malangizo ameneŵa mwa kuphunzitsa ndi kulalikira mwachangu pogwiritsa ntchito pakamwa. Zafalitsanso uthenga wabwino wa Ufumu pogwiritsa ntchito mabuku. Anthu mamiliyoni padziko lonse lapansi alabadira uthengawu, n’kukhala ophunzira a Kristu. Pakati pawo pali amuna ndi akazi amene satha kuŵerenga kapena kulemba. Anthu osaphunzira ameneŵa sikuti ndi Akristu onyozeka—ambiri a iwo atumikira Mulungu mokhulupirika zaka zambiri, apirira pozunzidwa chifukwa cha chipembedzo, ndipo asonyeza kukonda Yehova mwa kusunga malamulo ake.—1 Yoh. 5:3.
4 Ambiri mwa anthu osaphunzira ameneŵa amalakalaka atamaŵerenga ndi kulemba, popeza amadziŵa kuti kuphunzira n’kofunika kwambiri kuti athe kuchita zambiri pa kulambira Mulungu. Pamisonkhano, amafuna kuti aziŵerenga nawo pamene Baibulo ndi mabuku achikristu akuŵerengedwa, ndipo amafuna kuŵerenga mawu a nyimbo kuti aziimba limodzi ndi abale ndi alongo awo auzimu. Kunyumba, amalakalaka kudzidyetsa okha ndiponso mabanja awo mwa kuphunzira Baibulo. Muutumiki, amalakalaka kuphunzitsa ena choonadi cha Mawu a Mulungu popanda kudalira wina kuwaŵerengera.
5 Kuphunzira Kuŵerenga: Posamalira vuto limeneli, Mboni za Yehova zakonza zothandiza kulimbikitsa kudziŵa kuŵerenga ndi kulemba kudzera m’mipingo yawo komanso kuphunzitsa munthu payekha. Padziko lonse, zaphunzitsa amuna ndi akazi osaŵerengeka. M’Malawi mokha muno, kuyambira mu September 2000 mpaka August 2002 Mboni za Yehova zathandiza anthu pafupifupi 2,070 kudziŵa kuŵerenga ndi kulemba.
6 Ndithudi, tiyenera kuyamikira mipingo imene ili ndi makalasi ophunzitsa anthu kuŵerenga ndi kulemba. Komabe, m’mipingo ina anasiya kuphunzitsa anthu kuŵerenga ndi kulemba. Kodi anachitiranji zimenezi? Kodi tsopano aliyense mu mpingomo amadziŵa kuŵerenga? Kodi ophunzira osadziŵa kuŵerenga ndi kulemba anagwa ulesi chifukwa chakuti amene anaikidwa kuti aziwaphunzitsa sabwera mokhazikika? Kodi akulu alingalira mofatsa nkhani yosankha mbale woyenera kwambiri kukhala mphunzitsi (kapena aphunzitsi, ngati pakufunika makalasi angapo)? Kodi mphunzitsi, ngakhale ali woyenerera, anagwa ulesi chifukwa ophunzira a m’kalasi mwake ankajombajomba? N’zoona kuti, nthaŵi zambiri, ngati munthu akufunadi kudziŵa kuŵerenga ndi kulemba amadzipereka kwambiri ndipo amayesetsa kuchita zonse zimene zakonzedwa zoti zimuthandize kuchita zimenezo.
7 Mipingo imene ikufunika kuthandiza anthu ena amene amapezeka pa misonkhano kudziŵa kuŵerenga ndi kulemba ikulimbikitsidwa kuyamba makalasi ameneŵa mwamsanga, pogwiritsa ntchito buku lakuti “Dziperekeni pa Kuŵerenga ndi Kulemba.” Abale ndi alongo oyenerera amene apatsidwa ntchito yophunzitsa ayenera kuŵerenga malangizo a patsamba 3 pamutu wakuti “Zokhudza Mphunzitsi.” Aphunzitsi ayenera kuŵerenga malangizo ameneŵa mosamala kwambiri asanayambe kuphunzitsa.
8 Makalasi ophunzitsa anthu kuŵerenga ndi kulemba ayenera kupitiriza. Musaleke kuphunzitsa mpaka onse ofuna kuthandizidwa atathandizidwa. Ndi bwino kuti mphunzitsi akhale ndi buku lolembamo mayina a anthu a m’kalasi yophunzira kuŵerenga ndi kulemba ndipo azisunga mayina a anthu amene amabwera nthaŵi zonse m’kalasimo. Izi zidzathandiza akulu kudziŵa mmene maphunzirowo akuyendera. Popeza ofesi ya nthambi ilinso ndi chidwi kwambiri ndi maphunziro a abale ndi alongo athu, oyang’anira madera pochezera mipingo azionanso mmene makalasi ophunzitsa anthu kuŵerenga ndi kulembaŵa akuyendera.
9 Mlengi wathu, Yehova Mulungu, mwachisomo anapatsa anthu luso la kuŵerenga ndi kulemba. Koma luso limeneli silimapezeka popanda khama. Mphoto yaikulu ya kudziŵa kuŵerenga ndi kulemba ndiyo kutha kutenga Mawu a Mulungu ndi kumvera langizo la Mulungu lakuti: “Ulingiriremo usana ndi usiku.”—Yos. 1:8.
[Bokosi patsamba 4]
Malangizo Ophunzitsira Anthu Achikulire Kuŵerenga ndi Kulemba
● N’kofunika kupangitsa wophunzira kukhala ndi chidwi. Kuyambira pa phunziro loyamba, gogomezerani phindu la kudziŵa kuŵerenga ndi kulemba, ndipo limbikitsani wophunzira kukhala ndi zolinga zoyenera zotenga nthaŵi yaitali ndiponso zotenga nthaŵi yochepa.
● Kuti apite patsogolo wophunzirayo ayenera kuphunzitsidwa maulendo angapo pamlungu. Kamodzi pamlungu sikokwanira. Wophunzira ayenera kukhala ndi ntchito yokachitira kunyumba asanayambe phunziro lina.
● Musafune kuti wophunzira azikwanitsa zinthu zochulukitsitsa kapena kumuphunzitsa zambirimbiri nthaŵi imodzi. Zimenezi zingamugwetse ulesi ndipo akhoza kuleka kuphunzira.
● Khalani wolimbikitsa ndi wansangala nthaŵi zonse. Munthu amadziŵa kuŵerenga ndi kulemba pang’onopang’ono. Wophunzira azikhutira ndi mmene akupitira patsogolo.
Limbikitsani wophunzirayo kugwiritsa ntchito mwamsanga zimene akuphunzira pamoyo wake wa tsiku ndi tsiku.
● Musatayire nthaŵi pankhani zina. Achikulire ndi anthu otanganidwa. Gwiritsani ntchito bwino nthaŵi yophunzira powaphunzitsa mfundo zofunika kwambiri.
● Nthaŵi zonse lemekezani wophunzira, m’patseni ulemu womuyenera. Musamuchititse manyazi kapena kumuchepetsa.
● Zindikirani mavuto a wophunzira aliyense. Wophunzira angalephere kuŵerenga zilembo zazing’ono chifukwa chakuti akufunikira magalasi. Wina angakhale ndi vuto la kusamva bwino ndipo pachifukwa chimenechi angamavutike kumva matchulidwe olondola a mawu.
● Wophunzira ayenera kuphunzira kulemba zilembo za alifabeti chilichonse pachokha asanayambe kulemba chikhukhuza. Kulemba chilembo chilichonse pachokha sikuvuta kuphunzira ndi kulemba, ndiponso zilembo zake zimafanana kwambiri ndi zija zosindikizidwa m’mabuku.
● Ngati pepala loonekera kuseri lilipo—njira yabwino yophunzitsira kulemba zilembo ndiyo youza wophunzira kudindira, poika pepala loonekera kuseri pamwamba pa zilembo ndi kumalemba pa pepala loonekera kuserilo mmene mwadutsa zilembozo. Angadindire chilembocho kangapo asanayese kuchilemba popanda kudindira.
● Kaŵirikaŵiri munthu amadziŵa msanga kuŵerenga kusiyana ndi kulemba. Musachedwe kuyamba kuphunzitsa kuŵerenga zatsopano ngati wophunzira akulephera kulemba zimene mwamuuza kukalembera kunyumba. Komabe, kumbukirani kuti zilembo zatsopano sizivuta kuziphunzira ndi kuzikumbukira ngati wophunzira ayesa kuzilemba.
● Ngakhale kuti wophunzira wachikulire akhoza kuchita ntchito yovuta ndi manja ake, kulemba ndi bolopeni kapena pensulo kungakhale kovuta ndi kogwetsa mphwayi. Musaumirire kuti azilemba zilembo zabwino kwambiri.