-
Ndandanda ya Misonkhano ya UtumikiUtumiki wa Ufumu—2003 | January
-
-
amene walandira magazini, ndi wina amene sanalandire—thirakiti lakuti Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo? Fotokozani mwachidule mmene tingachitire ulendo wobwereza kwa amene tinawagaŵira magazini ndi kuwasiyiranso thirakiti.—Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 2001, tsa. 4, ndime 10.
Mph. 12: Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo. Funsani mkulu amene watumikira Yehova modzichepetsa komanso mokhulupirika kwa zaka zambiri. (Aheb. 13:7) Kodi anaphunzira bwanji choonadi? Kodi anagonjetsa zopinga ziti kuti apitirize? Ndi zinthu ziti zimene Yehova watipatsa kapenanso chilimbikitso zimene zinam’thandiza kupita patsogolo? Kodi anachita chiyani pokalamira udindo mumpingo? (1 Tim. 3:1) Kodi cham’thandiza n’chiyani kusamalira maudindo ake mumpingo kwinaku akusamaliranso udindo wake kuntchito ndi m’banja? (1 Tim. 5:8) Nanga akuuona bwanji mwayi wake wothandiza ena mumpingo?
Mph. 18: “Ntchito Imene Imafunika Kudzichepetsa.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Pokambirana ndime 3, pemphani omvetsera anenepo maganizo awo a mmene tingachitire ngati wina m’gawo atinyodola kapena ali wachipongwe, wamakani, kapena waukali. Pokambirana ndime 4, phatikizanipo ndemanga za mu Nsanja ya Olonda ya November 15, 1990, tsamba 20, ndime 17.
Nyimbo Na. 133 ndi pemphero lomaliza.
-
-
ZilengezoUtumiki wa Ufumu—2003 | January
-
-
Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu January: Buku la Mankind’s Search for God, Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja, ndi Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza. February: Buku latsopano la Yandikirani kwa Yehova. March: Buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Tidzayesetse kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba.
◼ Oyang’anira madera adzayamba kukamba nkhani ya onse yatsopano yakuti “Kulanditsidwa ku Dziko la Mdima.” Adzayamba tsiku lililonse kuyambira February mpaka March 2.
◼ Mipingo ipange makonzedwe abwino odzachita Chikumbutso chaka chino Lachitatu, pa April 16, dzuŵa litaloŵa. Ngakhale kuti nkhani ingayambe mofulumira, musayendetse zizindikiro za Chikumbutso kufikira dzuŵa litaloŵa. Funsani odziŵa za nyengo kwanuko kuti mudziŵe nthaŵi yoloŵera dzuŵa m’dera lanu. Ngati mipingo ingapo imagwiritsira ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi, mpingo umodzi kapena yoposerapo ingapeze malo ena odzagwiritsira ntchito tsikuli madzulo. Tikupereka malingaliro akuti, ngati kungatheke mapulogalamu akatha pazipita mphindi zosachepera 40 ena asanayambe, kuti onse apindule mokwanira. M’pofunika kuganizira za kuchuluka kwa magalimoto ndiponso koimikako magalimotowa, komanso za kukatenga ndi kukasiya anthu. Bungwe la akulu liyenera kupanga makonzedwe okomera mpingowo.
◼ Mipingo iyenera kuitanitsa timapepala toitanira anthu ku Chikumbutso cha chaka cha mawa ikamatumiza Fomu Yofunsira Mabuku (S-14) yotsatira. Timapepalati tili m’Chichewa, m’Chingelezi, ndi m’Chitumbuka. M’chinenero chilichonse poitanitsa, kuchuluka kwake kukhale kwa m’ma 100, monga ma 100, 200, 300, choncho basi. Chonde khalani osamala poitanitsa zimenezi chifukwa si zogaŵa mwachisawawa ayi koma ndi za anthu achidwi okha.
-
-
Bokosi la MafunsoUtumiki wa Ufumu—2003 | January
-
-
Bokosi la Mafunso
◼ Kodi ndani ayenera kupereka zilengezo pa Msonkhano wa Utumiki?
Cholinga cha mbali imeneyi ya Msonkhano wa Utumiki ndicho kudziŵitsa mpingo zinthu zofunika pa utumiki wathu. Zilengezo zina zimakhala zongotikumbutsa zina ndi zina ndipo zimakhala zofanana mlungu ndi mlungu. Komabe, zilengezo zonse ziyenera kuŵerengedwa momveka bwino, ndipo si ziyenera kuperekedwa mosaikirapo mtima kapena mwamwambo.
Malinga ndi mmene zilengezo zina zimakhalira, zingafunike mkulu kuzipereka. Zikatere, umakhala udindo wa woyang’anira wotsogolera kukonza zoti mkulu woyenerera azipereke, ndipo mbale wina apereke zilengezo zina zimene zakonzedwa.
Ngati kalata imene ili ndi nkhani yokhudza mpingo ilinso ndi nkhani ina yokhudza akulu okha, mkulu ndiye ayenera kuŵerenga nkhani yokhudza mpingoyo. Makalata ena ochokera ku ofesi ya nthambi amene amakhala ndi malangizo a mpingo angakhale bwino atamaŵerengedwa ndi mkulu woyenerera. Makalata ngati amenewo angakhale okhudza ntchito yapadera yolemba makalata okhudza abale athu amene akuzunzidwa. Makalata ena angakhale ndi mfundo zambiri zokhudza zimene zimachitika m’gulu lathu monga maulendo a oyang’anira madera ndi misonkhano ikuluikulu.
Nthaŵi zina pangafunike kupereka chilengezo chofunika kwambiri chokhudza thanzi la mpingo, ndipo chilengezocho chiyenera kuperekedwa momveka bwino. Zingakhale bwino ngati zilengezo zotero zitamaperekedwa ndi mkulu.
Kaya olengezawo ndi akulu kapena atumiki otumikira, zilengezozo ziyenera kukhala zomveka bwino komanso zachidule. Kutsata mfundo zimenezi kudzathandiza kuti malangizo opita ku mpingo azimveka bwino ndi kuti onse azipita patsogolo mogwirizana.—Sal. 133:1; 1 Akor. 14:8, 9, 40.
-
-
Lipoti la Utumiki la SeptemberUtumiki wa Ufumu—2003 | January
-
-
Lipoti la Utumiki la September
Av. Av. Av. Av.
Chiŵerengero cha: Maola Mag. M.O. Maph.
Apai. Apad. 59 124.3 63.5 57.0 8.9
Apainiya 3,872 67.1 12.9 25.9 3.1
Apai. Otha. 2,519 47.4 10.0 15.6 2.2
Ofalitsa 45,958 10.3 3.3 3.8 0.6
PAMODZI 52,408 Obatizidwa: 772
-
-
Mmene Mungafalitsire Buku la Yandikirani kwa YehovaUtumiki wa Ufumu—2003 | January
-
-
Mmene Mungafalitsire Buku la Yandikirani kwa Yehova
◼ Baibulo lanu lili kumanja, nenani kuti: “Anthu ambiri okhulupirira Mulungu amafuna kuyandikana naye kwambiri. Kodi mumadziŵa kuti Mulungu amatipempha kuyandikira kwa iye? [Ŵerengani Yakobo 4:8.] Buku ili lakonzedwa kuti litithandize kuyandikira kwa Mulungu pogwiritsira ntchito Baibulo lathulathu.” Ŵerengani ndime 1 patsamba 16.
◼ Baibulo lanu lili kumanja, nenani kuti: “Lerolino, m’dziko muli kupanda chilungamo. Zinthu zili mmene afotokozera apa. [Ŵerengani Mlaliki 8:9b.] Ena amadabwa ngati Mulungu zimam’khudza n’komwe. [Ŵerengani ziganizo ziŵiri zoyambirira m’ndime 4 patsamba 119.] Mutu umenewu ukufotokoza chifukwa chake Mulungu walola kupanda chilungamo kwakanthaŵi.”
-