Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • be phunziro 24 tsamba 160-tsamba 165 ndime 1
  • Kusankha Bwino Mawu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kusankha Bwino Mawu
  • Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Nkhani Yofanana
  • Kukhala ndi Kalankhulidwe Kabwino Tsiku ndi Tsiku
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Kulankhula Mawu Okondweretsa a Choonadi
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Muzigwiritsa Ntchito Bwino Lilime Lanu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Muzilankhula Mawu “Olimbikitsa”
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
Onani Zambiri
Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
be phunziro 24 tsamba 160-tsamba 165 ndime 1

PHUNZIRO 24

Kusankha Bwino Mawu

Kodi muyenera kuchita motani?

Gwiritsani ntchito mawu osonyeza ulemu ndi kukoma mtima, osavuta kumva; mawu osiyanasiyana okometsa kalankhulidwe kanu, komanso opereka mphamvu yofunikira ndi okhudza mtima moyenerera. Gwiritsani ntchito mawu mogwirizana ndi galamala.

N’chifukwa chiyani kuli kofunikira?

Kumalemekeza uthenga umene mukufotokoza ndipo kumasonyeza mmene mukuwaonera anthu amene mukulankhula nawo. Kumathandiza anthu kulabadira zimene mukunena.

MAWU ndi zida zamphamvu zolankhulirana. Koma kuti mawu athu akwaniritse cholinga chathu, tiyenera kuwasankha mosamala. Liwu limene lingakhale loyenera pa chochitika china, lingakhalenso lokhumudwitsa pa chochitika china. Ngakhale mawu osangalatsa, ngati agwiritsidwa ntchito molakwa, amakhala “mawu oŵaŵitsa.” Kugwiritsa ntchito mawu mwa njira imeneyo kungakhale kusalingalira bwino, komanso kusaganizira ena. Mawu ena ali ndi matanthauzo aŵiri, tanthauzo lina lingakhale lokhumudwitsa kapena lonyoza. (Miy. 12:18; 15:1) Koma “mawu abwino”—mawu olimbikitsa—amasangalatsa mtima wa munthu amene mukulankhula naye. (Miy. 12:25) Ngakhale kwa munthu wanzeru, kupeza mawu oyenera kumalira khama. Baibulo limatiuza kuti Solomo anazindikira kufunika kofunafuna “mawu okondweretsa” ndi “mawu oona.”—Mlal. 12:10.

Zinenero zina zili ndi mawu otchulira munthu wamkulu kapena munthu waudindo. Zilinso ndi mawu ena otchulira mnzako kapena wina wocheperapo msinkhu. Munthu wonyalanyaza mawu aulemu amenewo amamuona kukhala wamwano. Si bwinonso kudzilemekeza wekha podzitchula ndi mawu amene anthu amalemekezera ena malinga ndi chikhalidwe chawo. Pankhani yolemekezana, Baibulo limapereka muyezo wapamwamba woposa lamulo la dziko lililonse kapena mwambo uliwonse. Limalimbikitsa Akristu ‘kuchitira ulemu anthu onse.’ (1 Pet. 2:17) Anthu amene kuchokera pansi pa mtima amalemekeza ena mwa njira imeneyi, amatha kulankhula ndi anthu a misinkhu yonse mowasonyeza ulemu wawo.

Inde, anthu ambiri amene si Akristu oona amakonda kunena mawu amwano ndi otukwana. Iwo amaona kuti mawu amwano kapena otukwana amapereka mphamvu pa zimene akunena. Kapenanso angamatchule mawu amenewo chifukwa chosadziŵa bwino chinenerocho. Ngati wina anali ndi chizoloŵezi cholankhula mawu otero asanaphunzire njira za Yehova, kungakhale kovuta kusiya chizoloŵezicho. Komabe n’zotheka kutero. Mzimu wa Mulungu umatha kuthandiza munthu kusintha malankhulidwe ake. Komabe, munthuyo ayenera kukhala ndi chidwi chofuna kudziŵa mawu ambiri abwino—mawu omveka okoma, mawu omangirira—ndi kumawagwiritsa ntchito nthaŵi zonse.—Aroma 12:2; Aef. 4:29; Akol. 3:8.

Kulankhula Kosavuta Kumva. Chinthu chofunika kwambiri pa kalankhulidwe kabwino n’chakuti kalankhulidweko kazikhala kosavuta kumva. (1 Akor. 14:9) Ngati omvera anu satha kumva bwino mawu amene mukunena, mumakhala ngati munthu wolankhula chinenero chachilendo.

Alipo mawu amene ali ndi tanthauzo lapadera kwa anthu ena malinga ndi ntchito yawo. Anthu amenewo amatha kugwiritsa ntchito mawu amenewo nthaŵi zonse pakati pawo. Koma ngati muwagwiritsa ntchito kwa anthu osadziŵa ntchitoyo, kulankhula kwanu kungakhale kosapindulitsa kwenikweni. Ngakhale pogwiritsa ntchito mawu ozoloŵereka, ngati muloŵerera m’kufotokoza mfundo zocholoŵana zosafunikira kwenikweni, omvera anu angangotembenuzira maganizo awo ku zinthu zina.

Wokamba nkhani wolingalira bwino amasankha mawu oti ngakhale anthu amene sanaphunzire kwambiri akhoza kumva mosavuta. Potsanzira Yehova, iye amalingaliranso “wosauka.” (Yobu 34:19) Ngati wokamba nkhani aona kuti n’kofunika kuti agwiritse ntchito liwu lina losazoloŵereka, aligwiritse ntchito pamodzi ndi mawu ena osavuta kuti tanthauzo lake limveke.

Mawu osavuta osankhidwa bwino ndiwo amamveketsa mfundo mwamphamvu. Masentensi afupiafupi komanso mawu osavuta ndiwo amamveka msanga. Tikhoza kuphatikizamonso masentensi otalikirapo apa ndi apo kuti kalankhulidwe kathu kamveke kachibadwa. Koma mukafika pamfundo zimene mukufuna kuti omvera anu akazikumbukire, nenani mawu ozoloŵereka ndi masentensi afupiafupi.

Mawu Osiyanasiyana ndi Olondola. Mawu abwino alipo ambirimbiri. M’malo mogwiritsa ntchito mawu amodzimodziwo nthaŵi zonse, gwiritsani ntchito mawu osiyanasiyana. Mukamatero, malankhulidwe anu azikhala okoma ndi atanthauzo. Koma kodi mungawonjezere motani nkhokwe yanu ya mawu, titero kukamba kwake?

Poŵerenga, chongani mawu alionse amene simukumvetsa bwino ndipo ayang’aneni mu mtanthauzira mawu ngati muli naye m’chinenero chanu. Sankhani angapo a mawuwo, ndipo chitani khama lowagwiritsa ntchito moyenerera. Samalani kuti muziwatchula molondola ndipo atchuleni m’nkhani zimene angamveke mosavuta, osati kungofuna kudzionetsera ayi. Kudziŵa mawu ambiri kudzakuthandizani kuti muzitha kusinthasintha mawu polankhula. Koma tichenjezane pano—ngati munthu atchula mawu molakwika kapena ngati anena mawu osayenera, ena angaganize kuti munthuyo sakudziŵa kwenikweni zimene akunena.

Cholinga chathu chofuna kudziŵira mawu ambiri ndicho kuphunzitsa ena, osati kudzionetsera kuti azitisirira ayi. Kulankhula mawu ovuta ndi ataliatali kumapangitsa anthu kungoganizira za wolankhulayo. Cholinga chathu chizikhala kupereka uthenga wofunikawo ndi kuti uzimveka wokoma kwa omverawo. Kumbukirani mwambi wa m’Baibulo wakuti: “Lilime la anzeru linena bwino zomwe adziŵa.” (Miy. 15:2) Kugwiritsa ntchito mawu abwino, mawu oyenerera osavuta kumva, kumachititsa kalankhulidwe kathu kukhala kotsitsimutsa ndi kolimbikitsa. Sikakhala kozizira ndi kosakoma.

Pamene mukuwonjezera nkhokwe yanu ya mawu, samalani kugwiritsa ntchito mawu oyenerera. Mawu aŵiri akhoza kukhala ndi tanthauzo lofanana, komanso angatanthauze zinthu zosiyanako pang’ono nthaŵi zina. Ngati muzindikira zimenezi, mudzakhoza kumveketsa bwinobwino zimene mukunena ndi kupeŵa kukhumudwitsa omvera anu. Mvetserani mosamala kwa anthu olankhula bwino. Ndipo amtanthauzira mawu ena amapereka liwu limodzi, kenako mawu ena ofanana nalo tanthauzo. Choncho, mukhoza kupeza mawu osiyanasiyana opereka ganizo limodzimodzi kapena losiyanako pang’ono. Zimenezi n’zothandiza kwambiri pamene mukufuna liwu loyenerera malinga ndi nkhani yake. Musanawonjezere mawu atsopano m’nkhokwe yanu ya m’maganizo, tsimikizani kuti mwadziŵa tanthauzo lake, matchulidwe oyenera, ndi pamene angakhale oyenera kuwagwiritsa ntchito.

Mawu olunjika amapereka chithunzi choonekera bwino kusiyana ndi mawu achisawawa. Wolankhula anganene kuti: “Panthaŵiyo, anthu ambiri anadwala.” Kapena anganene kuti: “Patangopita miyezi yochepa, itatha nkhondo yoyamba ya padziko lonse, anthu pafupifupi 21,000,000 anafa ndi nthenda ya Fuluwenza.” Si mwaona nanga kusiyana kwake, ngati wokambayo amveketsa bwino zimene akutanthauza ndi mawu akuti “panthaŵiyo,” “anthu ambiri,” ndi akuti “anadwala”! Koma kuti mulankhule mwa njira imeneyi muyenera kudziŵa zenizeni za nkhani yanu ndiponso kusankha mawu mosamala.

Kugwiritsa ntchito mawu oyenerera kungathandizenso kumveketsa mfundo msanga m’malo mozungulira ndi mawu. Kuchulukitsa mawu kumaphimba mfundo. Koma kulankhula mosavuta kumathandiza ena kumvetsa mfundo ndi kuzikumbukira. Kumathandizanso kumveketsa mfundo molondola. Kaphunzitsidwe ka Yesu Kristu kanali kabwino kwambiri chifukwa anagwiritsa ntchito mawu osavuta. Tengerani chitsanzo chake. (Onani zitsanzo zolembedwa pa Mateyu 5:3-12 ndi Marko 10:17-21.) Tamayesezani kulankhula momvekera bwino mwa kusankha mawu mosamala.

Mawu Opereka Mphamvu, Okhudza Mtima, ndi Opereka Bwino Chithunzi. Mmene mukuwonjezera nkhokwe yanu ya mawu, musamaganizire za mawu atsopano okha komanso mawu amene ali ndi makhalidwe akutiakuti. Mwachitsanzo, ganizirani za maverebu (aneni) amene amapereka mphamvu; maajekitivu (afotokozi) amene amapereka chithunzi; ndi mawu ena okhudza mtima, osonyeza chifundo, kapena chidwi.

Baibulo lili ndi zitsanzo zambiri za mawu atanthauzo oterowo. Kudzera mwa mneneri Amosi, Yehova analimbikitsa kuti: ‘Funani chokoma, si choipa ayi . . . Danani nacho choipa, nimukonde chokoma.’ (Amosi 5:14, 15) Kwa Mfumu Sauli, mneneri Samueli analengeza kuti: ‘Yehova anang’amba ufumu wa Israyeli lero kuuchotsa kwa inu.’ (1 Sam. 15:28) Polankhula kwa Ezekieli, Yehova anagwiritsa ntchito mawu ovuta kuiŵala, akumati: ‘Nyumba yonse ya Israyeli ndiyo yolimba mutu ndi youma mtima.’ (Ezek. 3:7) Pofuna kutsindika ukulu wa tchimo la Israyeli, Yehova anafunsa kuti: ‘Kodi munthu adzalanda za Mulungu? Ndipo inu mundilanda ine.’ (Mal. 3:8) Pofotokoza kuyesedwa kwa chikhulupiriro ku Babulo, Danieli anafotokoza mopereka chithunzi chooneka bwino kuti ‘Nebukadinezara anadzazidwa ndi ukali’ chifukwa Sadrake, Mesake, ndi Abedinego anakana kulambira fano lake. Choncho analamula kuti iwo amangidwe naponyedwe mu ‘ng’anjo yotentha yamoto.’ Danieli pofuna kutithandiza kumvetsa kutentha kwa motowo, anati mfumuyo inalamula anyamata ake kuti ‘asonkheze ng’anjo kasanu ndi kaŵiri kuposa umo amasonkhezera’—kunali kutentha kwakuti anyamata a mfumuwo kungoiyandikira ng’anjoyo anafa nthaŵi yomweyo. (Dan. 3:19-22) Yesu polankhula ndi anthu mu Yerusalemu kutatsala masiku ochepa kuti afe, analankhula mokhudzika mtima kuti: ‘Ine ndinafuna kangati kusonkhanitsa pamodzi ana ako, inde monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ake m’mapiko ake, koma inu simunafuna ayi! Onani, nyumba yanu yasiyidwa kwa inu yabwinja.’—Mat. 23:37, 38.

Mawu osankhidwa bwino angapereke chithunzi choonekera bwino m’maganizo mwa omvera anu. Ngati mugwiritsa ntchito mawu owakopa mtima, omvera anu akatha “kuziona” ndi “kuzigwira” m’maganizo mwawo zinthu zimene mukunena. Akatha “kulaŵa” ndi “kumva kununkhira” kwa zakudya zimene mukafotokoza, ndipo “akamva” mamvekedwe a mawu amene mukalongosola ndi mawu a anthu amene mukafotokoza. Omverawo adzatengeka maganizo ndi zimene mukunena chifukwa mukawathandiza kuona zinthuzo ngati kuti zikuchitika panthawi yomweyo.

Mawu opereka zithunzi za m’maganizo amachititsa anthu kuseka kapena kulira. Amalimbikitsa chiyembekezo, amathandiza munthu wotaya mtima kufunitsitsa kukhalabe ndi moyo ndi kum’thandiza kukonda Mlengi wake. Anthu ochuluka padziko lonse lapansi alimbikitsidwa kwambiri ndi chiyembekezo choperekedwa m’Baibulo monga pa Salmo 37:10, 11, 34; Yohane 3:16; ndi Chivumbulutso 21:4, 5.

Pamene mukuŵerenga Baibulo ndi zofalitsa za “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” mudzaona kuti amagwiritsa ntchito mawu ambiri osiyanasiyana koma otanthauza zofanana. (Mat. 24:45) Musangowaŵerenga kenako n’kuwaiŵala nthaŵi yomweyo. Sankhani amene akusangalatsani, ndipo yambani kumawagwiritsa ntchito pakulankhula kwanu kwa masiku onse.

Kalankhulidwe Kotsatira Galamala. Anthu ena amazindikira kuti nthaŵi zina salankhula mogwirizana ndi malamulo a chinenerocho. Kodi angachite chiyani kuti akonze pamenepo?

Ngati mukupitabe kusukulu, tengerani mwayi umenewu kuti muphunzire galamala yabwino ndi mawu oyenerera. Ngati simukumvetsa bwino lamulo linalake la chilankhulo, funsirani kwa mphunzitsi wanu. Musaphunzire galamala kungoti muthane nazo ayi. Inuyo muli ndi chifukwa chabwino chimene ophunzira anzanu angakhale alibe. Mukufuna kukhala mlaliki waluso wa uthenga wabwino.

Koma bwanji ngati ndinu wachikulire ndipo munakula musakulankhula chinenero chimene mukugwiritsa ntchito tsopano? Kapena simunakhale ndi mwayi wophunzira chinenero chanu kusukulu. Musataye mtima. M’malo mwake, yesetsani mwakhama kuti muchidziŵe. Chitani zimenezo kaamba ka uthenga wabwino. Zambiri za chinenero timazidziŵa mwa kumvera ena polankhula. Choncho mvetserani mosamala pamene okamba nkhani ozoloŵera akukamba nkhani zawo. Mukamaŵerenga Baibulo ndi zofalitsa zozikidwa pa Baibulo, onani kapangidwe ka masentensi, mawu amene amayendera limodzi, ndi nkhani yake imene mawuwo apezekamo. Inunso yesani kulankhula motengera zitsanzo zimenezo.

Asangalatsi otchuka komanso oimba ambiri ali ndi mawu ndi malankhulidwe owombana ndi malamulo a chinenero. Ndipo anthu ambiri amakonda kutengera malankhulidwe a asangalatsi amenewo. Apandu ogulitsa mankhwala osokoneza bongo komanso anthu ena ozoloŵera moyo wa zaupandu ndi zachiwerewere amakhala ndi mawu awoawo. Amasintha matanthauzo a mawuwo ndi kuikamo odziŵa okha. Si chinthu chanzeru Mkristu kutengera anthu otero. Tikachita zimenezo tikafanana ndi amphulupulu a dziko amenewo ndi kutengera moyo wawo.—Yoh. 17:16.

Khalani ndi chizoloŵezi cholankhula bwino masiku onse. Ngati mulekerera malankhulidwe anu a tsiku ndi tsiku kukhala osasamala, musayembekezere kuti mukalankhula bwino pazochitika zapadera. Koma ngati mukhala ndi malankhulidwe abwino pamoyo wanu wa tsiku ndi tsiku, kudzakhala kosavuta komanso kwachibadwa kulankhula bwino papulatifomu kapena polalikira kwa ena za choonadi.

ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUPITE PATSOGOLO

  • Pa maganizo operekedwa m’phunziro lino, sankhani mfundo imodzi yokha imene mukufuna kuwongolera. Kuwongolera mbaliyo kukhale cholinga chanu pa mwezi umodzi kapena ingapo.

  • Nthaŵi zonse poŵerenga kumbukirani cholinga chanucho. Chikumbukireninso pamene mukumvetsera kwa okamba nkhani aluso. Lembani mawu amene mukufuna kuti muziwagwiritsa ntchito polankhula. Patsiku limodzi kapena aŵiri alionse, gwiritsani ntchito liwu limodzi limene mwalemba.

ZOCHITA: Pokonzekera Nsanja ya Olonda kapena Phunziro la Buku la Mpingo mlungu uno, sankhani mawu angapo amene simungawafotoze bwinobwino tanthauzo lake. Ayang’aneni mu mtanthauzira mawu ngati muli naye, kapena funsani tanthauzo lake kwa munthu amene amadziŵa mawu ambiri.

Mawu amene ndikufuna kuwonjezera m’kalankhulidwe kanga

Osiyanasiyana koma ofanana Opereka mphamvu, okhudza mtima,tanthauzo ndi olondola kapena opereka bwino chithunzi

․․․․․․․․․․․․․․ ․․․․․․․․․․․․․․ ․․․․․․․․․․․․․․ ․․․․․․․․․․․․․․

․․․․․․․․․․․․․․ ․․․․․․․․․․․․․․ ․․․․․․․․․․․․․․ ․․․․․․․․․․․․․․

․․․․․․․․․․․․․․ ․․․․․․․․․․․․․․ ․․․․․․․․․․․․․․ ․․․․․․․․․․․․․․

․․․․․․․․․․․․․․ ․․․․․․․․․․․․․․ ․․․․․․․․․․․․․․ ․․․․․․․․․․․․․․

․․․․․․․․․․․․․․ ․․․․․․․․․․․․․․ ․․․․․․․․․․․․․․ ․․․․․․․․․․․․․․

․․․․․․․․․․․․․․ ․․․․․․․․․․․․․․ ․․․․․․․․․․․․․․ ․․․․․․․․․․․․․․

․․․․․․․․․․․․․․ ․․․․․․․․․․․․․․ ․․․․․․․․․․․․․․ ․․․․․․․․․․․․․․

․․․․․․․․․․․․․․ ․․․․․․․․․․․․․․ ․․․․․․․․․․․․․․ ․․․․․․․․․․․․․․

․․․․․․․․․․․․․․ ․․․․․․․․․․․․․․ ․․․․․․․․․․․․․․ ․․․․․․․․․․․․․․

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena