PHUNZIRO 53
Kulimbikitsa Omvera ndi Kuwatsitsimutsa
KAYA atumiki a Mulungu akumane ndi mavuto otani, amatha kupeza chilimbikitso mu mpingo wachikristu. Koma kuti zimenezi zitheke, akulu makamaka ayenera kuonetsetsa kuti nkhani zawo ndi uphungu wawo zikumakhala zolimbikitsa. Akulu ayenera kukhala “monga pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo; monga mitsinje yamadzi m’malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko lotopetsa.”—Yes. 32:2.
Ngati ndinu mkulu, kodi nkhani zanu zimakhala zotsitsimutsa ndi zolimbikitsa? Kodi zimapereka nyonga kwa awo amene amayesetsa kutumikira Yehova mokhulupirika? Kodi zimapatsa mphamvu yolimbikira kuchita chifuniro cha Mulungu mosasamala kanthu za mphwayi ya anthu ambiri ndi anthu otsutsa? Bwanji ngati pakati pa omvera anu pali anthu ovutika maganizo, okhala m’mavuto a zachuma, kapena ovutika ndi matenda oopsa amene alibe mankhwala? Mukhoza ‘kulimbikitsa abale anu ndi mawu a m’kamwa mwanu.’—Yobu 16:5.
Gwiritsani ntchito mpata wanu wa kulankhula pothandiza abale anu kupeza chiyembekezo ndi nyonga kwa Yehova ndi zina zonse zimene iye watigaŵira.—Aroma 15:13; Aef. 6:10.
Akumbutseni Zimene Yehova Wachita. Njira yofunika kwambiri yolimbikitsira anthu ndiyo kusonyeza mmene Yehova anathandizira anthu ake kupyola m’mavuto m’nthaŵi zakale.—Aroma 15:4.
Yehova anauza Mose kuti ‘amulimbitse mtima’ ndi ‘kumukhwimitsa’ Yoswa Aisrayeli asanaloŵe m’Dziko Lolonjezedwa, limene panthaŵiyo mitundu ya adani ndiyo inali kukhalamo. Kodi Mose anachita motani zimenezo? Pamaso pa Yoswa, Mose anakumbutsa mtundu wonsewo zimene Yehova anawachitira potuluka mu Igupto. (Deut. 3:28; 7:18) Mose anakumbutsanso za mmene Yehova anawathandizira kugonjetsa Aamori. Ndiyeno Mose analimbikitsa Yoswa kuti: ‘Khala wamphamvu, limbika mtima.’ (Deut. 31:1-8) Pofuna kulimbikitsa abale anu, kodi mumawathandiza kupeza nyonga mwa kuona zimene Yehova wawachitira kale?
Nthaŵi zina anthu ena amada nkhaŵa kwambiri ndi mavuto awo moti amakayika ngati angadzapezedi madalitso a Ufumu. Akumbutseni za kudalirika kwa malonjezo a Yehova.—Yos. 23:14.
Mayiko ena akhazikitsa malamulo oletsa abale athu kulalikira uthenga wabwino. M’zochitika ngati zimenezo, akulu achikondi akhoza kuthandiza okhulupirira anzawo kupeza nyonga mwa kuwafotokozera zimene atumwi a Yesu Kristu anakumana nazo. (Mac. 4:1–5:42) Ndiponso kufotokoza mmene Mulungu anayendetsera zinthu zolembedwa m’buku la Estere kungalimbikitse abale kukhala olimbika mtima.
Pali anthu ena amene amangofika pamisonkhano ya mpingo koma osapita patsogolo ayi. Ena amaona kuti Mulungu sangawakhululukire konse chifukwa m’mbuyomu anali ndi moyo woipitsitsa kwambiri. Mwina mungafotokoze mmene Yehova anachitira ndi Mfumu Manase. (2 Mbiri 33:1-16) Kapena mungasimbe za anthu a ku Korinto wakale amene anasintha miyoyo yawo, nakhala Akristu, ndipo Mulungu anawayesa olungama.—1 Akor. 6:9-11.
Kodi alipo amene amaona kuti akukumana ndi mavuto chifukwa Mulungu sakuwayanjanso? Mungawakumbutse zimene Yobu anakumana nazo ndi mmene anadzapezera madalitso ochuluka chifukwa chokhalabe wokhulupirika kwa Yehova. (Yobu 1:1-22; 10:1; 42:12, 13; Sal. 34:19) Otonthoza onyenga a Yobu ananenetsa molakwa kuti iye ayenera kuti anachita tchimo linalake. (Yobu 4:7, 8; 8:5, 6) Mosiyana ndi zimenezo, pamene Paulo ndi Barnaba, anali kulimbikitsa ophunzira ndi ‘kuwadandaulira kuti akhalebe m’chikhulupiriro,’ iwo anati: ‘Tiyenera kuloŵa mu ufumu wa Mulungu ndi zisautso zambiri.’ (Mac. 14:21, 22) Lerolinonso, mukhoza kulimbikitsa aja amene akukumana ndi mayesero mwa kuwatchulira kuti kupirira nsautso n’kofunika kwa Mkristu aliyense ndipo n’kwamtengo wapatali m’maso mwa Mulungu.—Miy. 27:11; Mat. 24:13; Aroma 5:3, 4; 2 Tim. 3:12.
Limbikitsani omvera anu kuganizira njira zimene Yehova wakwaniritsira malonjezo ake m’miyoyo yawo. Mwa kupereka zikumbutso zotero, iwo angaone mmene Yehova wakhala akuwathandizira, malinga ndi mmene analonjezera. Pa Salmo 32:8, timaŵerenga kuti: “Ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang’ana iwe.” Mwa kuthandiza omvera anu kukumbukira mmene Yehova wawatsogolera kapena mmene wawalimbikitsira, adzakhoza kuona mmene Yehova akuwasamalira ndi kuti adzawathandizadi pa mayesero alionse amene akukumana nawo panthaŵi ino.—Yes. 41:10, 13; 1 Pet. 5:7.
Sonyezani Kuti Mukusangalala ndi Zimene Mulungu Akuchita Tsopano. Pofuna kulimbikitsa abale anu, auzeni zimene Yehova akuchita tsopano lino. Kunena zinthu zimenezo m’njira yosonyeza kuti mukusangalala nazo kudzachititsa omvera anunso kusangalala nazo.
Sonyezani mmene Yehova amatithandizira kupirira mavuto. Iye amatisonyeza njira yabwino koposa yokhalira ndi moyo. (Yes. 30:21) Amafotokoza zifukwa zimene kwakhalira upandu, kupanda chilungamo, umphaŵi, matenda, ndi imfa, ndipo amatiuzanso mmene ati adzazithetsere zonsezo. Iye watitchinga ndi gulu la abale lachikondi. Watipatsa mwayi wamtengo wapatali wa pemphero. Watipatsanso mwayi wokhala Mboni zake. Watiunikira zakuti Kristu anakhazikitsidwa kale pa mpando wachifumu kumwamba ndi kuti masiku otsiriza a dziko lakaleli akuthamangira kumathero kwake.—Chiv. 12:1-12.
Kuwonjezera pa madalitso onsewo pali misonkhano ya mpingo ndi misonkhano ikuluikulu. Mukamafotokoza madalitso ameneŵa m’njira yosonyeza kuti mumawayamikiradi, mudzalimbikitsa ena kuti asamanyalanyaze kusonkhana pamodzi ndi abale awo.—Aheb. 10:23-25.
Timapezanso nyonga mwa kumva malipoti onena za mmene Yehova wadalitsira ntchito yathu mu utumiki wa kumunda. M’zaka 100 zoyambirira pamene Paulo ndi Barnaba anali paulendo wopita ku Yerusalemu, ‘anakondweretsa kwambiri abale onse’ mwa kuwafotokozera tsatanetsatane wa mmene amitundu anali kutembenukira. (Mac. 15:3) Inunso mungakondweretse abale mwa kuwafotokozera zokumana nazo zolimbikitsa.
Mukhoza kuwalimbikitsanso mwa kuwathandiza kuona phindu la zimene akuchita. Ayamikireni potenga mbali mu utumiki wachikristu. Athokozeni aja amene amachita zochepa zokha chifukwa cha ukalamba kapena matenda koma amapirirabe mokhulupirika. Akumbutseni kuti Yehova saiŵala chikondi chimene iwo asonyeza pa dzina lake. (Aheb. 6:10) Chikhulupiriro chopambana pa chiyeso ndi chuma cha mtengo wapatali. (1 Pet. 1:6, 7) M’pofunika kuwakumbutsa mfundo imeneyi abale athu.
Lankhulani Mwachidaliro za Madalitso a M’tsogolo. Malonjezo ouziridwa a zinthu zilinkudza ndi gweronso lalikulu la chilimbikitso kwa onse okonda Mulungu. Mwina ambiri mwa omvera anu amva mobwerezabwereza za malonjezo amenewo. Koma mwa chiyamikiro chimene mumasonyeza polankhula za malonjezo ameneŵa, mukhoza kuonetsa kuti ndi enieni, mumapereka chidaliro chakuti zidzachitikadi, ndipo mumachititsa mitima ya omverawo kusefukira ndi chiyamiko. Kugwiritsa ntchito zimene mwaphunzira mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu kungakuthandizeni kuchita zimenezo.
Yehova mwiniyo ndiye Wolimbikitsa Wamkulu ndi Wopereka nyonga kwa anthu ake. Komabe, mukhoza kuthandizana naye pakulimbikitsa ena ndi kuwapatsa nyonga. Pamene mulankhula ku mpingo, tengerani mwayi umenewo kuchita zimenezo.