Nyimbo 178
“Mtendere wa Mulungu” Wopambana
1. Mtendere wa M’lungu
Ndiwamphamvu uchotsa
Mantha ndi kudera nkhaŵa,
Choncho tiri ndi bata.
Mtendere wa M’lungu,
Umatitchinjiriza,
Nthaŵi zonse okonzeka
—Kumbali ya Ufumu.
2. Kutsenderezeka
Kwapanikiza anthu.
Anthu asokonezeka,
Ndipo ali ndi mkwiyo.
Ife sitikwiya,
Mulungu saiŵala.
Chikondi ndi tchinjirizo
Zitipatsa mtendere.
3. Tidalira M’lungu.
Amatipatsa zonse.
Ngwachisomo nthaŵi zonse,
Adzatitsogolera.
Mtendere ndimame,
Umadzetsa chimwemwe.
Tipitebe patsogolo,
Potumikira M’lungu.