Nyimbo 19
Kukondwa Tsiku Lonse
1. Idzani! Kondwani!
M’chiyanjo cha Mulungu.
Kondwa tsiku lonse,
Pochita ntchito yonse.
Sitisoŵa kanthu. Ya athandiza.
Kodi tifunenjinso kwa iye?
Tiri ndi mtendere
Ndi chikhutiro chonse.
Tiri okhutira;
Tiyandike kwa M’lungu.
Mwachisangalalo, Sitibwerera,
Mokondwa timabala zipatso.
2. Tinamasulidwa.
Chotero tikondwera.
Mwana wa Mulungu,
Anena ndipo timva.
Tinagudwa m’mwazi. Atiphunzitsa.
Mulungu wathu anatisankha.
Ufumuwo wadza,
Udzetsadi chimwemwe.
Iye wadzutsatu
“Mdindo” wosamalira.
Tatsitsimu lidwa; Tiyembekeza.
Tiuze ena chiyembekezo.
3. Chiri chimwemwedi
Kulalikira anthu.
Tiri okondwera
Popeza onga nkhosa.
Pokonda abale Timalandira
Ena ndipo tiri ndi umodzi.
Timasangalala
Podziŵitsa Ufumu.
Khamu lalikulu
Lakuladi kwambiri!
Yehova Mulungu Atitsogoze.
Timatumikira iye yekha.