Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/04 tsamba 7
  • Zinthu Zotithandiza Kuti Tipewe Magazi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zinthu Zotithandiza Kuti Tipewe Magazi
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
km 12/04 tsamba 7

Zinthu Zotithandiza Kuti Tipewe Magazi

1. Kodi khadi la Chidziŵitso kwa Dokotala/Chommasula ku Mlandu lili ndi ntchito yanji?

1 Anthu a Mulungu amazindikira kuti ayenera kupewa kugwiritsa ntchito magazi mosayenera. Baibulo limatiuza kuti mphamvu ya moyo, yochokera kwa Mulungu ndipo ndiye mwini wake, ili m’magazi. (Sal. 36:9) Khadi la Chidziŵitso kwa Dokotala/Chommasula ku Mlandu (MD) lakhala chida chofunika kwambiri pothandiza anthu a Mulungu kupewa magazi. (Mac. 15:20, 28, 29) Koma mofanana ndi chida chilichonse, khadili lingakhale lothandiza ngati tiligwiritsa ntchito moyenera.

2. (a) Kodi ofalitsa obatizidwa ayenera kuchita chiyani akalandira khadi? (b) N’chifukwa chiyani zili zofunika kuti mbonizo zimuone mwini wake wa khadilo pamene akulisaina?

2 M’chaka chatsopano cha 2005, ofalitsa onse obatizidwa adzapatsidwa khadi latsopano. Ofalitsa obatizidwa amene ali ndi ana aang’ono osabatizidwa adzalandira Makadi a Ana kuti apatse ana awo. Makadiwa muyenera kukawalemba mosamala kunyumba kwanu koma OSAWASAINA. Pa Phunziro la Buku la Mpingo mlungu wotsatira, moyang’aniridwa ndi woyang’anira phunziro la buku, makadiwa ayenera kusainidwa ndi kulembedwa deti ndi mwini wake wa khadilo pamaso pa mboni ziwiri zimene pambuyo pake nazonso zidzasaina khadilo. Eni ake a makadiwa ayenera kuonetsetsa kuti alemba zonse zofunikira asanasainidwe. Masiginecha amenewa amatsimikizira kuti khadilo lili umboni walamulo wa zofuna za mwiniwake wa khadilo, ngakhale atati wakomoka. Mbonizo ziyenera kumuona mwini wake wa khadilo akulisaina.

3. Kodi ofalitsa osabatizidwa angasankhe kuchita chiyani?

3 Mwa kukopera mawu a pa khadilo n’kuwasintha kuti agwirizane ndi mmene zinthu zilili pamoyo wawo, ndi chikhulupiriro chawo, ofalitsa osabatizidwa angadzilembere khadi lawo ndi la ana awo kuti azigwiritsa ntchito.

4. (a) Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti khadi limeneli lithandize kwambiri? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kunyamula khadi lathu osati kulivala?

4 Ngakhale zitakhala kuti khadi lathu lalembedwa bwino, lasainidwa, ndi kulembedwa deti bwinobwino, silingatithandize pokhapokha titamayenda nalo nthawi zonse. (Miy. 22:3) Chonde dziwani kuti tiyenera kunyamula khadilo, osati kulivala. Sitiyenera kuvala khadilo popeza kuti zimenezi zikhoza kupereka chithunzi cholakwika. Timadziwika kuti ndife Mboni za Yehova, osati chifukwa chakuti timavala MD monga baji, koma chifukwa cha khalidwe lathu lachikristu ndi ntchito yathu ya nthawi zonse yolalikira. (1 Pet. 2:12; Mat. 24:14) Motero, khadi lathu tiyenera kuliika pamalo abwino osaonekera, monga m’kachikwama ka ndalama kapena m’thumba.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena