Nyimbo 79
Chilengedwe Chivumbula Ulemelero wa Yehova
(Salmo 19)
1. Yehova’nu ndidziŵa bwinodi,
Miyamba ilengeza ukulu.
Zinena usana ndi usiku
Zipatsa nzeru kwa ofatsawo.
Zinena usana ndi usiku
Zipatsa nzeru kwa ofatsawo.
2. Mwapanga dzuŵa mwezi nyenyezi,
Mwaika malire a nyanjazo.
Timawona zimene mwachita,
Ndi kuperekathamo kwa inu.
Timawona zimene mwachita,
Ndi kupereka thamo kwa inu.
3. Malamulo anu ndi angwiro.
Zikumbutso zichoka kwa inu.
Zitipatsa nzeru yabwinodi.
Tizisungetu, timamatire!
Zitipatsa nzeru yabwinodi.
Tizisungetu, timamatire!