Kuthandiza Ena Kudzera mu Phunziro la Buku la Mpingo
1 Akristu oyambirira anali kukumana m’nyumba kuti alambire Yehova. (Aroma 16:3, 5; Filem. 1, 2) M’mayiko ambiri masiku ano, makamaka kumene abale athu akutumikira movutika, misonkhano imachitikira m’nyumba za abale. Masiku anonso, Maphunziro a Buku a Mpingo ambiri akuchitikira m’nyumba za abale ndipo Yehova akupitirizabe kudalitsa makonzedwe amenewa.
2 Kudzera m’Phunziro la Buku la Mpingo, akulu amatha kusamalira bwino kwambiri munthu aliyense payekha kuti akule mwauzimu, zimene zingakhale zovuta kuzichita pa misonkhano yaikulu. Woyang’anira phunziro amayesetsa kudziwa onse m’gulu lake, kuwaweta ndi kusamalira zosowa zawo zauzimu. (Miy. 27:23) Amayesetsa kupita nawo limodzi mu utumiki wa kumunda ndipo nthawi zina kukawachezera kunyumba zawo.
3 Phunziroli limachitikira kufupi ndi kumene kumakhala anthu amene amakumana kumeneko. Pachifukwachi, malo amenewa amakhalanso malo abwino okumanirana pokonzekera utumiki wa kumunda. Zimenezi zimatipatsa mwayi wolowa mu utumiki ndi anthu osiyanasiyana a m’gulu lathu, ndipo timapindula poona mmene ena amafikira pakhomo la munthu. Mukangomaliza phunziro, ndi nthawi yabwino yopangana ndi amene mudzalowere naye limodzi mu utumiki.
4 Sonyezani Chidwi kwa Ena: Kodi mumatha kuona kuti paphunziro lanu la buku pamakhala ngati pabanja? Aliyense akamasonyeza chidwi kwa anthu a m’gulu lake zimathandiza kuti aliyense amve kuti pali kugwirizana. (Agal. 6:10) Mwachitsanzo, kodi mumadziwa ngati ena sanapezeke paphunziro ndiyeno n’kuwadziwitsa kuti aliyense anawasowa kuphunziro? Ngati winawake m’banja sanapezeke pachakudya aliyense m’banjamo amadziwa, ndipo zimam’khudza. Mzimu ngati umenewu m’gulu la phunziro la buku umathandiza abale kukhala ogwirizana kwambiri ndipo umawalimbikitsa kuti asamalephere kupezeka pa “chakudya.” Mukamasonyeza chidwi kwa aliyense wa m’gulu lanu mudzathandizira kukulitsa mzimu wa “banja” umenewu.
5 Kodi mungaganizirenso njira zina zimene mungasonyezere chidwi kwa ena? Chinthu china chimene mungachite ndicho kuyesetsa kucheza ndi ena pa misonkhano, osati kungowapatsa moni basi. Ena angamaoneke ngati amanyazi koma m’pamene akufuna munthu wocheza naye ndipo ngati mutayamba kuwalankhula ndi oti mukhoza kucheza nawo. Palinso zinthu zina zambiri zimene mungachite. Woyang’anira phunziro lanu la buku angathe kukhala ndi mfundo zina zothandiza. Bwanji osam’funsa?
6 Kodi mungam’thandize bwanji munthu wa m’gulu lanu la phunziro la buku ngati akuoneka kukhala wogwa mphwayi kapena akuoneka kuti ali ndi vuto linalake? Pamenepa, langizo lakuti “limbikitsani amantha mtima” lingakhale loyenerera. (1 Ates. 5:14) Ngati wina akudwala, zimakhaladi zotsitsimula ngati mabwenzi apita kunyumba kwake kukamuona ndi kumuthandiza. Kawirikawiri chimene chimafunika n’chakuti munthu athe kuona kuti mumamuwerengera ndi kuti mumasamala za iye. Woyang’anira phunziro la buku, monga kholo, ayenera kukhala maso kuona zizindikiro zosonyeza mphwayi ndi kupereka chithandizo choyenerera.
7 Kodi Mungathandize Nawo Bwanji?: Palinso njira zina zimene mungathandizire ku phunziro la buku. Njira imodzi ndiyo chitsanzo chanu chabwino. Mwachitsanzo, mukamavala ngati mmene mumavalira mukamapita ku msonkhano ku Nyumba ya Ufumu mumasonyeza ulemu. Mumasonyeza chitsanzo chabwino kwa anthu amene ali ndi chizolowezi chovala motayirira. Kodi ndi chizolowezi chanu kufika mofulumira kuti musasokoneze msonkhano?
8 N’zoona kuti phunziro limakhala losangalatsa kwambiri aliyense akalikonzekera, mwina mwa kudula mizere kunsi kwa mayankho ndiyeno n’kumayankha m’mawu awoawo. Kuwerengeratu malemba osagwidwa mawu ndiyeno n’kukawaphatikiza mu ndemanga pamene tikuyankha kungakhale kolimbikitsa pa msonkhano. Ena amathanso kupeza nthawi yofufuza nkhani zina zimene zikuchirikiza mfundo zofunika kenako n’kukagawana ndi anzawo pa phunziro. Zimenezi n’zoyamikirika. Zinthu zonsezi zimathandiza kuti Phunziro la Buku la Mpingo likhale lotsitsimula mwauzimu ndi lolimbikitsa kwa onse opezekapo.
9 Amene nthawi zonse amapezeka ku phunziro la buku amakhulupirira kuti pamakhala madalitso a Yehova. Kumeneko munthu amapezako chithandizo chimene akufunikira ndiponso amathandiza nawo kutsitsimula ena mwauzimu. Ngati simupezeka nawo pa msonkhanowu nthawi zonse, bwanji osayesetsa kusintha pulogalamu yanu kuti muzisangalala ndi msonkhano wabwinowu umene Yehova limodzi ndi gulu lake akukonzerani.