Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 3/05 tsamba 3-4
  • Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
km 3/05 tsamba 3-4

Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Pamene tikuimirira pakhomo penipeni pa dongosolo latsopano la zinthu limene likubwera, m’pofunika kuyembekezera Yehova. (Zef. 3:8) Mneneri Danieli ananena kuti “Mulungu . . . wakuvumbulutsa zinsinsi; Iye ndiye wadziwitsa . . . chimene chidzachitika masiku otsiriza.” (Dan. 2:28) Ndi mwayidi wamtengo wapatali kukhala m’nthawi ya mapeto imene inanenedweratu ndiponso kumvetsa zinsinsi zimene Yehova akuvumbula panopa.

Kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” Yehova wavumbula pang’ono ndi pang’ono zolinga zake zosonkhanitsa “khamu lalikulu” la padziko lonse la olambira ake m’nthawi zovuta zino za “masiku otsiriza.” (Mat. 24:45; Chiv. 7:9; 2 Tim. 3:1) Yesaya 2:2, 3 amafotokoza kuti ntchito imeneyi yosonkhanitsa anthu padziko lonse ikuchitika “masiku otsiriza” ano. Chaka chilichonse, kusonkhanitsa kumeneku kumachitika m’kati mwa zisokonezo ndi ziwawa zimene zikuchitika paliponse m’dzikoli.

M’chaka chonse cha 2004, tinauzidwa kukhala osamala kwambiri kumvera mawu a Yesu akuti: ‘Dikirani . . . Khalani okonzekeratu.’ (Mat. 24:42, 44) Ndithudi, zimene zikuchitika m’dzikoli zili ndi tanthauzo lalikulu kwa Akristu amene amadziwa “zizindikiro za nyengo ino” ndi kuchita mogwirizana ndi zimenezo. (Mat. 16:1-3) Pokwaniritsa Mawu ake, Yehova adzapitirizabe kukhala ndi gulu la anthu ake limene iye walikonza mwadongosolo mosasamala kanthu za zitsutso zimene anthu akewo angakumane nazo.

Ngakhale kuti ena ayesetsa kulepheretsa kapena kuletsa ntchito yolalikira za Ufumu, abale athu akupitirizabe kulankhula za choonadi ndi kusonkhana pamodzi. (Mac. 5:19, 20; Aheb. 10:24, 25) Ku Russia mu June 2004, khoti la apilo ku Moscow linavomereza zimene linagamula khoti laling’ono zoletsa ntchito ya Mboni za Yehova ndi kutseka bungwe lawo la lamulo mu mzindawo. Komabe, abale athu sakubwerera m’mbuyo; akudziwa zimene Mulungu amafuna kuti iwo achite, ndipo amamvera iye monga Wolamulira koposa kumvera anthu. (Mac. 5:29) Tikukhulupirira kuti Yehova adzatsogolerabe atumiki ake ngakhale milandu kumakhoti isawayendere.

Ku Republic of Georgia m’zaka zingapo zapitazi, abale awonongeredwa katundu wawo, kuchitidwa za chiwawa ndi magulu a anthu, ndiponso kuona mabuku awo akuotchedwa. Koma palibe chida chosulidwira iwo chimene chapindula. (Yes. 54:17) M’chaka cha utumiki cha 2004, boma la Georgia linalolanso Mboni za Yehova mwalamulo. Misonkhano yachigawo inachitika popanda wina aliyense kusokoneza, ndiponso mabuku akulowa bwinobwino m’dzikolo. Panalinso chiwerengero chapamwamba chatsopano cha ofalitsa ndi cha opezeka pa Chikumbutso.

Ku Armenia, Eritrea, Republic of Korea, Rwanda, ndi Turkmenistan, abale atsekeredwa m’ndende chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Ngakhale kuti akuwachitira nkhanza, abalewo amadziwa chifukwa cha m’Malemba chimene akuvutikira, ndipo zimawathandiza kupitirizabe kukhala okhulupirika pamene akuyang’ana kwa Yehova kaamba ka chipulumutso.—1 Pet. 1:6; 2 Pet. 2:9.

Pamene mukuona Lipoti la Chaka cha Utumiki cha 2004 mu Nsanja ya Olonda ya February 1, 2005, mudzasangalala kuona ubwino wa Yehova. (Sal. 31:19; 65:11) Tili ndi chikhulupiriro chakuti lipoti limeneli likulimbikitsani kupitirizabe kuyenda m’njira imene Mulungu amakondwera nayo.—1 Ates. 4:1.

Tikupitirizabe kuyesetsa kufikira anthu onse ndi choonadi. Mwachitsanzo, pali mavidiyo, ma DVD, ndi zinthu zina za chinenero cha manja ndiponso mabuku a anthu osaona zimene zakonzedwa kuti zithandize mwauzimu anthu osamva ndi osaona. Ofalitsa Ufumu ambiri aphunzira zinenero zimene zimalankhulidwa ndi anthu obwera kuchokera ku mayiko ena amene akukhala m’gawo la mpingo wawo.

Kuwonjezera apo, papangidwanso magulu mahandiredi ambiri kumagawo akutali kumene kuli kovuta kufikako. Nthambi ina ili ndi magulu akutali oposa 300 okhala ndi ofalitsa oposa 7,000. Zimenezi ndi zizindikiro zakuti mipingo ina yatsopano ipangidwa. Ndiponso, mwa anthu 16,760,607 amene anapezeka pa Chikumbutso m’chaka cha utumiki chimenechi, anthu oposa 10 miliyoni sanali Mboni. Chimenechi ndi chizindikiro chakuti pali ntchito yaikulu yotuta imene ikuyembekezeka kuchitika.

Tikuthokoza Yehova chifukwa cha madalitso ake ochuluka ndiponso chifukwa chotisamalira mwachikondi tsiku ndi tsiku. (Miy. 10:22; Mal. 3:10; 1 Pet. 5:7) Pamene tikuyendera limodzi kupita patsogolo ‘m’masiku otsiriza’ ano, chidaliro chathu chonse chili mwa Yehova. Kaya tikumane ndi mavuto amtundu wanji, tiyeni tikumbukire lemba la chaka chino cha 2005 lakuti: “Thandizo langa lidzera kwa Yehova.” (Sal. 121:2) Landirani moni wathu wachikondi ndipo dziwani kuti timakupemphererani.

Ndife abale anu,

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena