Limbikirani Kulalikira
1 Tikukhala m’nthawi zowawitsa. Nkhondo za pachiweniweni, nkhondo za mafuko, masoka achilengedwe, ndi zochitika zina zochititsa mantha zili paliponse. Panopa kuposa kale lonse, anthu onse akufunika uthenga wabwino. Komabe, kunyalanyaza zinthu zauzimu kwafala kwambiri. M’madera ena, zimavuta kupeza anthu panyumba ndiponso zimavuta kwambiri kupeza anthu amene angatimvetsere kapena amene akufuna kuphunzira Baibulo. Ngakhale zili choncho, m’pofunika kulimbikira kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu umene unakhazikitsidwa.—Mat. 24:14.
2 Kukonda Anthu: Kulalikira kwathu kumasonyeza mmene Yehova amakondera anthu. ‘Safuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.’ (2 Pet. 3:9; Ezek. 33:11) Choncho, iye walamula kuti ‘uthenga wabwino uyenera uyambe kulalikidwa kwa anthu a mitundu yonse’ monga mmene Yesu ananenera. (Marko 13:10) Mulungu akupempha anthu kubwera kwa iye kuti adzapulumuke chiweruzo chimene chikubwera padziko la Satanali. (Yow. 2:28, 29, 32; Zef. 2:2, 3) Kodi ife sitikusangalala kuti Yehova anatipatsa mwayi umenewu?—1 Tim. 1:12, 13.
3 Lipoti la padziko lonse likusonyeza kuti m’chaka cha utumiki cha 2004, panali kuchitika maphunziro a Baibulo 6,085,387 mwezi uliwonse ndipo ophunzira atsopano pafupifupi 5,000 anali kubatizidwa mlungu uliwonse. Ena mwa anthu amene adziperekawa, anapezeka chifukwa chakuti Yehova anadalitsa ofalitsa akhama amene analimbikira kulankhula ndi wina aliyense m’magawo awo. Mipingo yasangalala kwambiri chifukwa cha zimenezi, ndiponso ndi mwayi waukulu kwambiri kugwira limodzi ndi Mulungu ntchito yopulumutsa moyo imeneyi.—1 Akor. 3:5, 6, 9.
4 Kulemekeza Dzina la Mulungu: Timalimbikira kulalikira kuti tilemekeze Yehova ndi kuti tiyeretse dzina lake pamaso pa anthu onse. (Aheb. 13:15) Satana wanyenga “dziko lonse” polipangitsa kuganiza kuti Mulungu alibe mphamvu zoti angathetsere mavuto a anthu, kuti alibe n’chidwi chomwe ndi mavuto a anthu, kapenanso kuwapangitsa kuganiza kuti kulibe Mulungu. (Chiv. 12:9) Tikamalalikira, timachirikiza choonadi chonena za Atate wathu wakumwamba waulemerero. Tiyeni tipitirizebe kulemekeza dzina lake, panopa mpaka muyaya.—Sal. 145:1, 2.