Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/05 tsamba 3
  • Anthu a Mitundu Yonse Adzapulumuka

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anthu a Mitundu Yonse Adzapulumuka
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mumangowona Kawonekedwe Kakunja?
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Kodi Mumaona Maonekedwe Akunja Okha?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
  • Tisamaweruze Poona Maonekedwe Akunja
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • Kodi Mumaona Anthu Mmene Yehova Amawaonera?
    Nsanja ya Olonda—2008
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
km 4/05 tsamba 3

Anthu a Mitundu Yonse Adzapulumuka

1. Kodi ubwenzi wathu ndi Mulungu umadalira chiyani?

1 Chisomo cha Mulungu chatsegula njira ya chipulumutso. N’chifuno cha Yehova kuti “anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.” (1 Tim. 2:3, 4) Ubwenzi wathu ndi Mulungu sikuti umadalira fuko lathu, kudziwika kwathu, luso lathu, kapena maonekedwe athu ayi, koma kukhulupirira kwathu nsembe ya dipo ya Yesu. (Yoh. 3:16, 36) Monga antchito anzake a Mulungu, tifunika kusiyiratu kukondera, kumene kungatichititse kukana anthu amene Yehova akufuna kuwalandira.

2, 3. Kodi n’chiyani chimene chingatithandize kuti tisaweruze anthu chifukwa cha mmene akuonekera?

2 Pewani Kuweruza: Yehova amayang’ana zimene zili mu mtima wa anthu, popanda dumbo kapena tsankho. (1 Sam. 16:7) Amathanso kudziwa kuti anthuwo akhoza kukhala otani. Motero, amaona anthu amene akufuna kum’kondweretsa kukhala ofunika. (Hag. 2:7) Kodi timaona ena monga mmene Mulungu amawaonera?

3 Anthu ena amene timakumana nawo mu utumiki akhoza kutidabwitsa chifukwa cha mmene akuonekera. Akhoza kuvala zauve kapena mopanda ulemu. Akhozanso kukhala ndi ndevu zosasamalika, kapena kuvala ndolo pamphuno kapena palilime. Ena amakhala oti alibe nyumba. Ena angatichitire zankhanza. M’malo mowaweruza kuti anthu oterewa sangakhale olambira Yehova, tiyenera kuwaona moyenera, “pakuti kale ifenso tinali opusa, osamvera, [ndi] onyengeka.” (Tito 3:3) Tikazindikira zimenezi, tidzafunitsitsa kulalikira kwa aliyense, ngakhale kwa anthu omwe tingaganize kuti ndi osayenera chifukwa cha maonekedwe awo.

4, 5. Kodi tikuphunzirapo chiyani pa zitsanzo za Yesu ndi Paulo?

4 Zitsanzo za M’zaka 100 Zoyambirira: Yesu Kristu ankayesetsa kuthandiza anthu amene ankaoneka kuti ndi osayenera, anthu amene ena ankawaona kuti ndi okanika. (Luka 8:26-39) Ngakhale kuti sanali kulekerera makhalidwe oipa, Yesu ankadziwa kuti anthu angamachite zoipa m’moyo wawo. (Luka 7:37, 38, 44-48) Pachifukwa chimenechi, iye anatha kuwamvetsetsa, ndipo ‘anagwidwa chifundo ndi iwo, chifukwa anali ngati nkhosa zopanda mbusa.’ (Marko 6:34) Kodi sitingatengereko chitsanzo chakecho?

5 Mtumwi Paulo anaponyedwa miyala, kukwapulidwa, ndi kuikidwa m’ndende. (Mac. 14:19; 16:22, 23) Kodi iye anakhumudwa chifukwa cha zinthu zopweteka zimenezi n’kuyamba kuganiza kuti anali kungotaya nthawi yake pachabe ndi anthu amitundu ndi mafuko osiyanasiyana amenewo? Ayi ndithu. Ankadziwa kuti pakati pa mafuko amenewo pakhoza kupezeka anthu oona mtima, ndipo anayesetsa kupeza anthu oterowo. Kodi ndi mmenenso timaonera anthu a m’gawo lathu amene ndi ochokera kosiyanasiyana ndiponso azikhalidwe zosiyanasiyana?

6. Kodi pangakhale zotsatirapo zotani ndi mmene timaonera atsopano pa misonkhano ya mpingo?

6 Kulandira Ena Masiku Ano: Ambiri mwa anthu a Mulungu amathokoza kuti abale ndi alongo sanayang’ane maonekedwe awo akunja koma anawalandira mu mpingo. Mwamuna wina anafika pa Nyumba ya Ufumu ku Germany atavala zovala zosachapa, ali ndi ndevu zosasamalika ndiponso tsitsi lalitali lofika m’mapewa. Mwamunayo anali wodziwika ndi mbiri yoipa. Koma ngakhale zinali choncho, anamulandira ndi manja awiri pamsonkhanopo. Mwamunayo anasangalala kwambiri mwakuti patatha mlungu umodzi anabweranso. Posapita nthawi, anayamba kudzisamalira bwino, anasiya kusuta fodya, ndipo anakalembetsa ukwati wake kuboma. Kenako, iye ndi mkazi wake pamodzi ndi ana awo aakazi amapasa anayamba kutumikira Yehova monga banja logwirizana.

7. Kodi tingam’tsanzire bwanji Mulungu wathu wopanda tsankho?

7 Mwa kutsanzira Mulungu wathu wopanda tsankho, tiyeni tiitane anthu onse kuti adzapindule ndi chisomo cha Mulungu.

[Mawu Otsindika patsamba 3]

“Mulungu alibe, tsankhu koma m’mitundu yonse, wakumuopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” —Machitidwe 10:34, 35.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena