Nyimbo 111
Kuunika Kumkabe Kuuŵala
1. Kuunika kwa Mawu kuŵalabe,
Ku kuŵalirirabe Tsikulo lidza (mwamsangaditu).
Cho’nadi cha Ufumu chiwoneka;
Kwa ife akupempha: ‘Mvetseranitu’ (kwambiridi).
Nthaŵi yapita pamene
Tinaikidwa mundende.
Tsiku Lake.
Cho’nadi chadza.
Kuŵala kuwoneka ngati dzuŵa,
Kuunika kuŵalira olungamawo,
Kuŵala kwa Ya.
2. Kuŵala panjira ya olungama.
Yehova achititsa Mwachikondidi (chachikuludi).
Avumbula kumvetsetsa kowona;
Aumba anthu ake ndi chowonadi (cha ufumu).
Chifukwa chosalungama
Pangakhale kupatuka;
Chowonadi
Chikuŵalabe.
Mulungu watumiza chithandizo.
Aunikira mwaulemelero wake,
Kuŵalirabe.
3. Kuŵalako ku’nikira panjira
Monga dzuŵa masana kopanda mtambo (kokongoladi).
Ya nkuŵala amatiunikira;
Aŵalitsa njirayo, tisausetu (moyo wathu).
Tisakayikire ndithu,
Kukakamiza cho’nadi.
Munjirayo
Tikhalemobe.
Kuŵala kudzawonjezerekabe.
Olungama akondwera nako kuŵala.
Kuunikadi.